< Psaltaren 44 >

1 En undervisning Korah barnas, till att föresjunga. Gud, vi hafve med våra öron hört, våre fäder hafva det förtäljt oss, hvad du i deras dagar gjort hafver fordom.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.
2 Du hafver med dine hand fördrifvit Hedningarna; men dem hafver du insatt. Du hafver förderfvat folken; men dem hafver du utvidgat.
Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena ndi kudzala makolo athu; Inu munakantha mitundu ya anthu, koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
3 Ty de hafva icke intagit landet genom sitt svärd, och deras arm halp dem intet; utan din högra hand, din arm och ditt ansigtes ljus; ty du hade ett behag till dem.
Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.
4 Gud, du äst den samme min Konung, som Jacob hjelp tillsäger.
Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
5 Igenom dig skole vi nederslå våra fiendar. I ditt Namn vilje vi undertrampa dem som sig emot oss sätta.
Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu; kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
6 Ty Jag förlåter mig icke uppå min båga, och mitt svärd kan intet hjelpa mig;
Sindidalira uta wanga, lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
7 Utan du hjelper oss ifrå våra fiendar, och gör dem till skam, som hata oss.
koma Inu mumatigonjetsera adani athu, mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
8 Vi vilje dagliga berömma oss af Gudi, och tacka dino Namne evinnerliga. (Sela)
Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse, ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
9 Hvi bortdrifver du då nu oss, och låter oss till skam varda; och drager icke ut i vårom här?
Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa; Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
10 Du låter oss fly för våra fiendar, att de, som oss hata, skola beröfva oss.
Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
11 Du låter uppäta oss såsom får, och förströr oss ibland Hedningarna.
Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
12 Du säljer ditt folk förgäfves, och tager der intet före.
Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, osapindulapo kanthu pa malondawo.
13 Du gör oss till smälek vårom grannom; till spott och hån dem som omkring oss äro.
Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina, chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
14 Du gör oss till ett ordspråk ibland Hedningarna, och att folken rista hufvudet öfver oss.
Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina; anthu amapukusa mitu yawo akationa.
15 Dagliga är min smälek för mig, och mitt ansigte är fullt med skam;
Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
16 Att jag måste de försmädare och lastare höra, och fienderna och de hämndgiruga se.
chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe, chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.
17 Allt detta är öfver oss kommet, och vi hafve dock intet förgätit dig, eller otroliga i ditt förbund handlat.
Zonsezi zinatichitikira ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
18 Vårt hjerta är icke affallet, eller vår gång viken ifrå din väg;
Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo; mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
19 Att du så sönderslår oss ibland drakar, och öfvertäcker oss med mörker.
Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.
20 Om vi vår Guds Namn förgätit hade, och våra händer upplyft till en främmande Gud;
Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21 Det kunde Gud väl finna. Nu känner han ju vår hjertans grund.
kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22 Ty vi varde ju dagliga för dina skull dräpne, och äro räknade såsom slagtefår.
Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse, tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
23 Uppväck dig, Herre; hvi sofver du? Vaka upp, och bortdrif oss icke med allo.
Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona! Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24 Hvi fördöljer du ditt ansigte; och förgäter vårt elände och tvång?
Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu, ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
25 Ty vår själ är nederböjd till jordena; vår buk låder vid jordena.
Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi; matupi athu amatirira pa dothi.
26 Statt upp, hjelp oss, och förlös oss, för dina godhets skull.
Imirirani ndi kutithandiza, tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

< Psaltaren 44 >