< Sefania 1 >

1 Neno la Bwana lililomjia Sefania mwana wa Kushi, mwana wa Gedalia, mwana wa Amaria, mwana wa Hezekia, wakati wa utawala wa Yosia mwana wa Amoni mfalme wa Yuda:
Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda.
2 Bwana asema, “Nitafagia kila kitu kutoka kwenye uso wa dunia.”
“Ndidzawononga kotheratu zinthu zonse pa dziko lapansi,” akutero Yehova.
3 “Nitafagilia mbali watu na wanyama; nitafagilia mbali ndege wa angani na samaki wa baharini. Wafanyao maovu watapata tu kokoto, nami nitamkatilia mbali mwanadamu atoke katika dunia,” asema Bwana.
“Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe; ndidzawononga mbalame zamlengalenga ndi nsomba za mʼnyanja. Ndidzawononga anthu oyipa, ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,” akutero Yehova.
4 “Nitaiadhibu Yuda na wote wakaao Yerusalemu. Kutoka mahali hapa nitakatilia mbali kila mabaki ya Baali, majina ya wapagani na makuhani waabuduo sanamu:
Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala, mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:
5 wale ambao husujudu juu ya mapaa kuabudu jeshi la vitu vya angani, wale ambao husujudu na kuapa kwa Bwana na ambao pia huapa kwa Malkamu,
amene amagwada pa madenga a nyumba zawo kupembedza zolengedwa zamumlengalenga, amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova, komanso mʼdzina la Moleki,
6 wale wanaoacha kumfuata Bwana, wala hawamtafuti Bwana wala kutaka shauri lake.
amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova, osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova.
7 Nyamazeni mbele za Bwana Mwenyezi, kwa maana siku ya Bwana iko karibu. Bwana ameandaa dhabihu, amewaweka wakfu wale aliowaalika.
Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova, chifukwa tsiku la Yehova layandikira. Yehova wakonzekera kupereka nsembe; wapatula iwo amene wawayitana.
8 Katika siku ya dhabihu ya Bwana nitawaadhibu wakuu na wana wa mfalme na wale wote wanaovaa nguo za kigeni.
Pa tsiku la nsembe ya Yehova ndidzalanga akalonga ndi ana aamuna a mfumu ndi onse amene amavala zovala zachilendo.
9 Katika siku hiyo nitaadhibu wote ambao hukwepa kukanyaga kizingiti, ambao hujaza hekalu la miungu yao kwa dhuluma na udanganyifu.”
Pa tsiku limenelo ndidzalanga onse amene safuna kuponda pa chiwundo, amene amadzaza nyumba ya ambuye awo ndi chiwawa ndi chinyengo.
10 Bwana asema, “Katika siku hiyo kilio kitapanda juu kutoka lango la Samaki, maombolezo kutoka mtaa wa pili, na mshindo mkubwa kutoka vilimani.
“Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova, “Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba, kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano, ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.
11 Ombolezeni, ninyi mnaoishi katika eneo la sokoni; wafanyabiashara wenu wote wameangamizwa, wote ambao wanafanya biashara ya fedha wataangamizwa.
Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika; a malonda anu onse adzapululidwa, ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa.
12 Wakati huo nitasaka mji wa Yerusalemu kwa taa, na kuwaadhibu wale ambao wanakaa katika hali ya kuridhika, ambao ni kama divai iliyobaki kwenye machicha, ambao hudhani, ‘Bwana hatafanya lolote, jema au baya.’
Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale ndi kulanga onse amene sakulabadira, amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa, amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse, chabwino kaya choyipa.’
13 Utajiri wao utatekwa nyara, nyumba zao zitabomolewa. Watajenga nyumba, lakini hawataishi ndani yake; watapanda mizabibu lakini hawatakunywa divai yake.
Chuma chawo chidzafunkhidwa, nyumba zawo zidzagwetsedwa. Adzamanga nyumba, koma osakhalamo; adzadzala minda ya mpesa koma sadzamwako vinyo wake.”
14 “Siku kubwa ya Bwana iko karibu: iko karibu na inakuja haraka. Sikilizeni! Kilio katika siku ya Bwana kitakuwa kichungu, hata shujaa atapiga kelele.
Tsiku lalikulu la Yehova layandikira, layandikira ndipo lifika msanga. Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa, ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.
15 Siku ile ni siku ya ghadhabu, siku ya fadhaa na dhiki, siku ya uharibifu na ukiwa, siku ya giza na utusitusi, siku ya mawingu na giza nene,
Tsiku limenelo lidzakhala la ukali, tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni, tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko, tsiku la mdima ndi lachisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
16 siku ya tarumbeta na mlio wa vita dhidi ya miji yenye ngome na dhidi ya minara mirefu.
Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo, tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa ndi nsanja za pa ngodya.
17 Nitawaletea watu dhiki, nao watatembea kama vipofu, kwa sababu wametenda dhambi dhidi ya Bwana. Damu yao itamwagwa kama vumbi na matumbo yao kama taka.
Ndidzabweretsa msautso pa anthu ndipo adzayenda ngati anthu osaona, chifukwa achimwira Yehova, magazi awo adzamwazika ngati fumbi ndi mnofu wawo ngati ndowe.
18 Fedha yao wala dhahabu yao hazitaweza kuwaokoa katika siku hiyo ya ghadhabu ya Bwana. Katika moto wa wivu wake dunia yote itateketezwa, kwa maana ataleta mwisho wa wote wanaoishi katika dunia ghafula.”
Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Dziko lonse lapansi lidzanyeka mʼmoto wa nsanje yake chifukwa adzakantha modzidzimutsa onse okhala pa dziko lapansi.

< Sefania 1 >