< Torati 27 >
1 Mose na wazee wa Israeli wakawaagiza watu: “Yashikeni maagizo haya yote ninayowaagiza leo.
Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino.
2 Mtakapokuwa mmevuka Mto Yordani na kuingia katika nchi awapayo Bwana Mungu wenu, msimamishe mawe makubwa na mkayatie lipu.
Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza.
3 Andikeni juu yake maneno yote ya sheria hii wakati mtakapokuwa mmevuka na kuingia katika nchi awapayo Bwana Mungu wenu, nchi itiririkayo maziwa na asali, kama vile Bwana, Mungu wa baba zenu, alivyowaahidi.
Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.
4 Mtakapokuwa mmevuka Yordani, simamisheni mawe haya juu ya Mlima Ebali, kama ninavyowaagiza leo, mkayatie lipu.
Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize.
5 Huko mjengeeni Bwana Mungu wenu madhabahu, madhabahu ya mawe. Msitumie kifaa chochote cha chuma juu yake.
Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo.
6 Jengeni madhabahu ya Bwana Mungu wenu kwa mawe ya shambani, na mtoe sadaka za kuteketezwa juu yake kwa Bwana Mungu wenu.
Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu.
7 Toeni sadaka za amani juu yake, mkizila na kufurahia mbele za Bwana Mungu wenu.
Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
8 Nanyi mtaandika maneno yote ya sheria hii kwa wazi sana juu ya mawe haya ambayo mmesimamisha.”
Ndipo pa miyalapo mudzalembepo mawu onse a malamulo ndi malemba akuluakulu.”
9 Kisha Mose na makuhani, ambao ni Walawi, wakawaambia Israeli wote, “Nyamaza ee Israeli, sikiliza! Sasa umekuwa taifa la Bwana Mungu wako.
Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu.
10 Mtii Bwana Mungu wako, na kufuata amri zake na maagizo ninayokupa leo.”
Muzimvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsata malamulo ake ndi malangizo ake omwe ndikukupatsani lero lino.”
11 Siku ile ile Mose akawaagiza watu:
Tsiku lomwelo Mose analamula anthu kuti:
12 Mtakapovuka Mto Yordani, makabila haya yatasimama juu ya Mlima Gerizimu kubariki watu: Simeoni, Lawi, Yuda, Isakari, Yosefu na Benyamini.
Mukawoloka Yorodani, mafuko awa akayimirire pa Phiri la Gerizimu ndi kudalitsa anthu: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini.
13 Makabila haya yatasimama juu ya Mlima Ebali kwa kutamka laana: Reubeni, Gadi, Asheri, Zabuloni, Dani na Naftali.
Ndipo mafuko awa akayimirire pa Phiri la Ebala ndi kutchula matemberero: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafutali.
14 Nao Walawi watawasomea watu wote wa Israeli kwa sauti kubwa:
Alevi adzayankhula mokweza kwa Aisraeli onse kuti:
15 “Alaaniwe mtu afanyaye sanamu ya kuchonga au mwenye kusubu sanamu, kitu ambacho ni chukizo kwa Bwana, kazi ya mikono ya fundi stadi, na kuisimamisha kwa siri.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.”
16 “Alaaniwe mtu amdharauye baba yake na mama yake.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.”
17 “Alaaniwe mtu asogezaye jiwe la mpaka wa jirani yake.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.”
18 “Alaaniwe mtu ampotoshaye kipofu njiani.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.”
19 “Alaaniwe mtu apotoshaye haki ya mgeni, yatima au mjane.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.”
20 “Alaaniwe mtu akutanaye kimwili na mke wa baba yake, kwa maana anadharau malazi ya baba yake.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.”
21 “Alaaniwe mtu akutanaye kimwili na mnyama yeyote.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.”
22 “Alaaniwe mtu akutanaye kimwili na dada yake, binti wa baba yake au binti wa mama yake.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.”
23 “Alaaniwe mtu akutanaye kimwili na mama mkwe wake.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.”
24 “Alaaniwe mtu amuuaye jirani yake kwa siri.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.”
25 “Alaaniwe mtu apokeaye rushwa ili kumuua mtu asiye na hatia.”
“Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.”
26 “Alaaniwe mtu yule ambaye hatashikilia maneno ya sheria hii kwa kuyatekeleza.”
“Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.”