< Amosi 2 >

1 Hili ndilo asemalo Bwana: “Kwa dhambi tatu za Moabu, hata kwa dhambi nne, sitaizuia ghadhabu yangu. Kwa sababu alichoma mifupa ya mfalme wa Edomu, ikawa kama chokaa.
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu, mpaka kuwasandutsa phulusa,
2 Nitatuma moto juu ya Moabu ambao utateketeza ngome za Keriothi. Moabu ataanguka kwa ghasia kubwa katikati ya vilio vya vita na mlio wa tarumbeta.
Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti. Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa, mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.
3 Nitamwangamiza mtawala wake na kuwaua maafisa wake wote pamoja naye,” asema Bwana.
Ndidzawononga wolamulira wake ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,” akutero Yehova.
4 Hili ndilo asemalo Bwana: “Kwa dhambi tatu za Yuda, hata kwa dhambi nne, sitaizuia ghadhabu yangu. Kwa sababu wameikataa sheria ya Bwana na hawakuzishika amri zake, kwa sababu wamepotoshwa na miungu ya uongo, miungu ambayo babu zao waliifuata.
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo akana lamulo la Yehova ndipo sanasunge malangizo ake, popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza, milungu imene makolo awo ankayitsatira,
5 Nitatuma moto juu ya Yuda ambao utateketeza ngome za Yerusalemu.”
Ine ndidzatumiza moto pa Yuda, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”
6 Hili ndilo asemalo Bwana: “Kwa dhambi tatu za Israeli, hata kwa dhambi nne, sitaizuia ghadhabu yangu. Wanawauza wenye haki kwa fedha, na maskini kwa jozi ya viatu.
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva, ndi osauka ndi nsapato.
7 Wanakanyaga juu ya vichwa vya maskini, kama vile juu ya mavumbi ya nchi, na kukataa haki kwa walioonewa. Baba na mwanawe hushiriki msichana mmoja, kwa hivyo hulinajisi Jina langu takatifu.
Amapondereza anthu osauka ngati akuponda fumbi, ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa. Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo, ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
8 Watu hulala kando ya kila madhabahu juu ya nguo zilizowekwa rehani. Katika nyumba ya mungu wao hunywa mvinyo ulionunuliwa kwa fedha walizotozwa watu.
Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe pa zovala zimene anatenga ngati chikole. Mʼnyumba ya mulungu wawo amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.
9 “Nilimwangamiza Mwamori mbele yao, ingawa alikuwa mrefu kama mierezi, na mwenye nguvu kama mialoni. Niliyaangamiza matunda yake juu na mizizi yake chini.
“Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo, ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu. Ndinawononga zipatso zawo ndiponso mizu yawo.
10 “Niliwapandisha toka Misri, na nikawaongoza miaka arobaini jangwani niwape nchi ya Waamori.
“Ine ndinakutulutsani ku Igupto, ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kudzakupatsani dziko la Aamori.
11 Pia niliinua manabii kutoka miongoni mwa wana wenu na Wanadhiri kutoka miongoni mwa vijana wenu. Je, hii si kweli, enyi watu wa Israeli?” asema Bwana.
Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri, ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri. Kodi si choncho, inu Aisraeli?” akutero Yehova.
12 “Lakini mliwafanya Wanadhiri kunywa mvinyo na kuwaamuru manabii wasitoe unabii.
“Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja, ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.
13 “Sasa basi, nitawaponda kama gari lipondavyo wakati limejazwa nafaka.
“Tsono Ine ndidzakupsinjani monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.
14 Mkimbiaji hodari hatanusurika, wenye nguvu wataishiwa nguvu zao, na shujaa hataweza kuokoa maisha yake.
Munthu waliwiro sadzatha kuthawa, munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga, wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15 Mpiga upinde atakimbia, askari wapiga mbio hawataweza kutoroka, na mpanda farasi hataokoa maisha yake.
Munthu wa uta sadzalimbika, msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka, ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16 Hata askari walio mashujaa sana siku hiyo watakimbia uchi,” asema Bwana.
Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri adzathawa ali maliseche pa tsikulo,” akutero Yehova.

< Amosi 2 >