< Génesis 19 >
1 Y al caer la noche, los dos ángeles llegaron a Sodoma; y Lot estaba sentado en el camino a la ciudad; y cuando los vio, se levantó y vino delante de ellos, cayendo de bruces sobre la tierra.
Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu.
2 Y él dijo: Mis amos, ven ahora a la casa de tu siervo, y descansen allí pasen la noche, y laven sus pies; y temprano en la mañana pueden continuar su camino. Y dijeron: No es así, pero tomaremos el resto de nuestra noche en la calle.
Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.” Iwo anati, “Ayi, tigona panja.”
3 Pero él hizo su petición con mayor fuerza, por lo que fueron con él a su casa; y les preparó comida, e hizo pan sin levadura, del cual tomaron.
Koma iye anawawumiriza kwambiri kotero kuti anapita naye pamodzi ku nyumba kwake. Anawakonzera chakudya buledi wopanda yisiti ndipo anadya.
4 Pero antes de acostarse, los hombres de la ciudad, todos los hombres de Sodoma, recorrieron la casa, jóvenes y viejos, de todas partes de la ciudad;
Alendo aja asanapite kogona, amuna onse achinyamata ndi achikulire ochokera mbali zonse za mzinda wa Sodomu anazinga nyumba ya Loti.
5 Y clamando a Lot, dijeron: ¿Dónde están los hombres que vinieron a tu casa esta noche? Envíanoslos a nosotros, para que podamos tener nuestro placer con ellos.
Iwo anayitana Loti namufunsa kuti, “Ali kuti amuna aja amene afika kuno usiku womwe uno? Atulutse, utipatse kuti tigone nawo malo amodzi.”
6 Y salió Lot a ellos en el portal, cerrando la puerta tras él.
Loti anatuluka panja kukakumana nawo natseka chitseko
7 Y dijo: Hermanos míos, no hagan está maldad.
ndipo anati, “Ayi anzanga, musachite zinthu zoyipa zotere.
8 Vean ahora, tengo dos hijas solteras; las enviaré a ti para que les hagan lo que les parezca mejor: no hagas nada a estos hombres, porque es por eso que han caído bajo la sombra de mi techo.
Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.”
9 Y dijeron: Hazte a un lado! Este hombre, dijeron, vino aquí de un país extraño, ¿y ahora será nuestro juez? ahora te haremos peor que a ellos; y empujando violentamente a Lot, se acercaron para abrir la puerta.
Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko.
10 Pero los hombres extendieron sus manos y llevaron a Lot dentro de la casa, cerrando de nuevo la puerta.
Koma anthu aja anali mʼkatiwa anasuzumira namukokera Loti uja mʼkati mwa nyumba nʼkutseka chitseko.
11 Pero los hombres que estaban afuera de la puerta se quedaron ciegos, todos ellos, pequeños y grandes, y se cansaron de buscar la puerta.
Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo.
12 Entonces los hombres dijeron a Lot: ¿Hay otros de tu familia aquí? yernos o hijos o hijas, sacarlos a todos de este lugar;
Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno,
13 Porque estamos a punto de enviar destrucción a este lugar, porque una gran protesta contra ellos ha llegado a los oídos del Señor; y el Señor nos ha enviado a poner fin a la ciudad.
chifukwa tiwononga malo ano. Yehova waona kuti kuyipa kwa anthu a mu mzindawu kwakulitsa. Choncho watituma kuti tiwuwononge.”
14 Y salió Lot, y dijo a sus yernos, que estaban casados con sus hijas: Vengan, salgamos de este lugar, porque el Señor está a punto de enviar destrucción sobre la ciudad. Pero sus yernos no lo tomaron en serio.
Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula.
15 Y cuando amaneció, los ángeles hicieron todo lo que pudieron para hacer ir a Lot, diciendo: Levántate pronto, toma a tu mujer y a tus dos hijas que están aquí, y vete, por temor a que vengas a la destrucción en el castigo de la ciudad.
Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.”
16 Mientras esperaba, los hombres tomaron de la mano a él, a su mujer y a sus hijas, porque el Señor tuvo misericordia de ellos y los puso fuera de la ciudad.
Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo.
17 Y cuando los pusieron, él dijo: Huyan por su vida, sin mirar atrás ni esperar en la tierra baja; ve rápidamente a la montaña o llegarás a la destrucción.
Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!”
18 Y Lot les dijo: No es así, oh mi Señor;
Koma Loti anawawuza kuti, “Ayi, ambuye anga chonde musatero!
19 Ahora, tu siervo ha tenido la gracia en tus ojos y grande es tu misericordia para mantener mi vida lejos de la destrucción, pero no puedo llegar a la montaña antes de que el mal me alcance y la muerte;
Taonani, Inu mwachitira mtumiki wanu chifundo, ndipo mwaonetsa kukoma mtima kwanu pondipulumutsa. Sindingathawire ku mapiri chifukwa chiwonongekochi chikhoza kundipeza ndisanafike ku mapiriko ndipo ndingafe.
20 Esta ciudad, ahora, está cerca, y es una pequeña: O, déjame ir allí (¿no es una pequeña?) para que mi vida esté a salvo.
Koma, chapafupi pomwepa pali mudzi woti ndikhoza kuthamanga nʼkukafikako. Mundilole ndithawireko, ndi waungʼono kwambiri, si choncho? Mukatero, moyo wanga upulumuka.”
21 Y él dijo: Mira, te he dado tu petición en esto una cosa más: no enviaré destrucción sobre esta ciudad.
Mngeloyo anati kwa iye, “Chabwino, ndavomeranso pempho lako, sindiwononga mudzi ukunenawo.
22 Ve allí rápidamente, porque no puedo hacer nada hasta que hayas llegado ahí. Por esta razón, la ciudad fue nombrada Zoar.
Koma uthawireko mofulumira chifukwa sindichita kena kalikonse mpaka utafikako.” (Nʼchifukwa chake mudziwo unatchedwa Zowari).
23 El sol salió cuando Lot llegó a Zoar.
Pamene Loti amafika ku Zowari, nʼkuti dzuwa litatuluka.
24 Entonces él Señor envió fuego y humo ardiente desde los cielos sobre Sodoma y Gomorra.
Ndiye Yehova anathira sulufule wamoto wochokera kumwamba kwa Yehova pa Sodomu ndi Gomora.
25 Y envió destrucción sobre aquellas ciudades, con toda la tierra baja y toda la gente de esas ciudades y todas las cosas verdes en la tierra.
Kotero, anawononga mizindayo, chigwa chonse pamodzi ndi onse okhala mʼmizindayo. Anawononganso zomera zonse za mʼdzikolo.
26 Pero la esposa de Lot, mirando hacia atrás, se convirtió en una columna de sal.
Koma mkazi wa Loti anachewuka ndipo anasanduka mwala wa mchere.
27 Y Abraham se levantó temprano en la mañana y fue al lugar donde había estado hablando con el Señor:
Mmawa mwake, Abrahamu ananyamuka nabwerera kumalo kumene anakumana ndi Yehova kuja.
28 Y mirando en dirección a Sodoma y Gomorra y la tierra baja, vio el humo de la tierra subir como el humo de un horno.
Anayangʼana kumunsi ku Sodomu, Gomora ndi ku dziko lonse la ku chigwa, ndipo anaona chiwutsi chikufuka mʼdzikolo ngati chikuchokera mʼngʼanjo.
29 Y aconteció que cuando Dios envió destrucción sobre las ciudades de la llanura, cumplió su palabra a Abraham, y envió lejos a Lot cuando puso fin a las ciudades donde vivía.
Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako.
30 Entonces Lot subió de Zoar al monte, y vivía allí con sus dos hijas, por temor a que no viviera en Zoar; y él y sus hijas se ganaron la vida en una cueva de la peña.
Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga.
31 Y la hija mayor dijo a su hermana: Nuestro padre es viejo, y no hay hombre que sea nuestro esposo en la forma natural:
Tsiku lina mwana wake wamkazi wamkulu anawuza mngʼono wake kuti, “Abambo athu ndi wokalamba ndipo palibe mwamuna aliyense pano woti atikwatire ndi kubereka ana monga mwa chikhalidwe cha pa dziko lonse lapansi.
32 Ven, démosle mucho vino a nuestro padre, y nos iremos a su cama, para que tengamos descendencia de nuestro padre,
Tiye tiwamwetse vinyo ndipo tigone nawo. Tikatero mtundu wathu udzakhalapobe.”
33 Y esa noche hicieron que su padre bebiera mucho vino; y la hija mayor se metió en su cama; y él no sabía cuándo ella entró o cuándo se fue.
Usiku umenewo analedzeretsa vinyo abambo awo, ndipo wamkuluyo analowa nagona naye. Abambo awo samadziwa kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.
34 Y el día después, la hija mayor dijo a la menor: Anoche estaba con mi padre; hagamos que tome mucho vino esta noche otra vez, y ve a él, para que podamos tener descendencia de nuestro padre.
Tsiku linali mwana wamkazi wamkulu uja anati kwa mngʼono wake, “Usiku wathawu ine ndinagona ndi abambo anga. Tiye tiwaledzeretsenso vinyo usiku uno ndipo iwe upite ndi kugona nawo ndipo mtundu wathu udzakhalapobe.”
35 Y esa noche otra vez hicieron que su padre tomara mucho vino; y la hija menor se metió en su cama; y él no sabía cuándo ella entró o cuándo se fue.
Choncho analedzeranso vinyo abambo awo usiku umenewonso, ndipo mwana wamkazi wamngʼono anapita nagona nawo. Abambo awo sanadziwenso kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.
36 Y así las dos hijas de Lot fueron embarazadas por su padre.
Choncho ana onse awiri a Loti aja anatenga pathupi pa abambo awo.
37 Y la hija mayor tuvo un hijo, y le dio el nombre de Moab: es el padre de los moabitas hasta hoy.
Mwana wamkazi wamkulu uja anabereka mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse.
38 Y el menor tuvo un hijo, y le dio el nombre de Ben-ammi; de él vienen los hijos de Ammón hasta hoy.
Mwana wamkazi wamngʼono naye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha iye Beni-Ammi. Iyeyu ndiye kholo la Aamoni onse.