< Esdras 7 >

1 Después de estas cosas, cuando Artajerjes era rey de Persia, Esdras, hijo de Seraías, hijo de Azarías, hijo de Hilcías,
Zitatha izi, Aritasasita ali mfumu ya ku Perisiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu abambo ake anali Seraya mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
2 El hijo de Salum, el hijo de Sadoc, el hijo de Ahitob.
mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi,
3 El hijo de Amarías, el hijo de Azarías, el hijo de Meraiot,
mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Merayoti,
4 El hijo de Seraías, el hijo de Uzi, el hijo de Buqui,
mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,
5 El hijo de Abisúa, el hijo de Finees, el hijo de Eleazar, el hijo de Aarón, el principal sacerdote.
mwana wa Abisuwa, mwana wa Finehasi, mwana wa Eliezara, mwana wa Aaroni mkulu wa ansembe uja.
6 Este Esdras subió de Babilonia; y era un escriba, experto en la ley de Moisés que el Señor, el Dios de Israel, había dado; y el rey, movido por el Señor su Dios, le dio todo lo que pidió.
Ezara ameneyu anabwera kuchokera ku Babuloni. Iyeyu anali wophunzira kwambiri za malamulo a Mose, amene Yehova Mulungu wa Israeli anapereka. Mfumu inamupatsa chilichonse chimene anapempha pakuti dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye.
7 Y subieron algunos de los hijos de Israel, con algunos de los sacerdotes y los levitas y los cantores y los encargados de las puertas y los sirvientes del templo, a Jerusalén, en el séptimo año del rey Artajerjes.
Tsono mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wa Aritasasita, Ezara pamodzi ndi Aisraeli ena, kuphatikizapo ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda, ndi anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ananyamuka kubwerera ku Yerusalemu.
8 Y vino a Jerusalén en el quinto mes, en el séptimo año del gobierno del rey.
Ezara anafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.
9 Comenzando su viaje desde Babilonia el primer día del primer mes, llegó a Jerusalén el primer día del quinto mes, con la ayuda de su Dios.
Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye.
10 Porque Esdras se había preocupado de aprender la ley del Señor y de hacerlo, y de enseñar sus reglas y decisiones en Israel.
Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.
11 Ahora, esta es una copia de la carta que el rey Artajerjes le dio a Esdras, sacerdote y escriba, quien escribió las palabras de las órdenes del Señor y sus reglas para Israel:
Iyi ndi kalata imene mfumu Aritasasita anapereka kwa wansembe Ezara, mlembi wa malamulo, munthu wophunzira kwambiri zokhudza malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli.
12 Artajerjes, rey de los reyes, a Esdras el sacerdote, escriba de la ley del Dios del cielo, toda paz;
Ndine Aritasasita, mfumu ya mafumu. Ndikulembera iwe Ezara wansembe ndi mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba. Malonje.
13 Y ahora es mi orden que todos los del pueblo de Israel, y sus sacerdotes y levitas en mi reino, que están listos y desean ir a Jerusalén, vayan con ustedes.
Tsopano ndikulamula kuti Mwisraeli aliyense, wansembe kapena Mlevi wokhala mʼdziko langa, amene akufuna kupita ku Yerusalemu ndi iwe, apite.
14 Porque eres enviado por el rey y sus siete reyes consejeros, para conocer a Judá y a Jerusalén, como lo ordena la ley de tu Dios que está en tu mano;
Ine mfumu pamodzi ndi alangizi anga asanu ndi awiri tikukutumani kuti mukafufuze za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu kuti mukaone mmene anthu akutsatira malamulo a Mulungu wanu, amene anawapereka kwa inu.
15 Y para llevar con usted la plata y el oro ofrecidos libremente por el rey y sus sabios al Dios de Israel, cuyo Templo está en Jerusalén,
Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi alangizi anga tapereka mwa ufulu kwa Mulungu wa Israeli, amene amakhala ku Yerusalemu.
16 Así como toda la plata y el oro que obtienes de la tierra de Babilonia, junto con la ofrenda del pueblo y de los sacerdotes, entregados gratuitamente para la casa de su Dios, que está en Jerusalén:
Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu.
17 Con este dinero, compren los bueyes, ovejas y corderos, con sus ofrendas de cereales y sus ofrendas de bebidas, para ser ofrecidos en el altar del templo de su Dios, que está en Jerusalén.
Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
18 Y todo lo que les parezca bien a ti y a tus hermanos hacer con el resto de la plata y el oro, eso es conforme a la voluntad de su Dios.
Ndalama zotsala mudzagwiritse ntchito zimene inuyo ndi abale anu zikakukomerani malingana nʼkufuna kwa Mulungu wanu.
19 Y las vasijas que te han sido dadas para los usos del templo de tu Dios, debes entregarlas al Dios de Jerusalén.
Ziwiya zonse zimene akupatsani kuti mukatumikire nazo mʼNyumba ya Mulungu wanu, kaziperekeni kwa Mulungu ku Yerusalemu.
20 Y lo que sea necesario para la casa de tu Dios, y que tengas que dar, tómalo del almacén del rey.
Ndipo chilichonse chimene chingafunike mʼNyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze mpata wopereka, ndalama zake zogulira zidzachokere mʼthumba la chuma cha mfumu.
21 Y yo, también, el rey Artajerjes, ahora doy órdenes a todos los guardianes del dinero del rey al oeste del río, para que todo lo que él sacerdote Esdras necesite, el escriba de la ley del Dios del cielo, se lo den, debe ser hecho prestamente,
Tsopano Ine, mfumu Aritasasita, ndikulamula asungichuma onse a dera la Patsidya pa Yufurate kuti, chilichonse chimene wansembe Ezara, mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba adzapempha kwa inu, mupatseni mwa msanga.
22 Hasta cien talentos de plata, cien medidas de grano, cien medidas de vino y cien medidas de aceite y sal sin medida.
Ngakhale atafunika makilogalamu 3,400 asiliva, makilogalamu 10,000 a tirigu, malita 2,000 a vinyo, malita 2,000 a mafuta ndi mchere wochuluka motani, zonsezi mupereke monga zingafunikire.
23 Lo que sea ordenado por el Dios del cielo, hágase rápidamente por la casa del Dios del cielo; para que no haya ira contra el reino del rey y sus hijos.
Chimene Mulungu Wakumwamba walamula, chichitike mosamalitsa ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba kuopa kuti mkwiyo wa Mulungu ungayakire mfumu, dziko lake ndi ana ake.
24 Además, le dejamos en claro que será ilegal poner impuestos o pagos en bienes o pagos forzosos a cualquiera de los sacerdotes o levitas, los cantores, los porteros, los sirvientes del templo o Cualquier siervo de esta casa de Dios.
Tikukudziwitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kukhometsa msonkho uliwonse anthu awa: ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda kapena aliyense wogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.
25 Y tú, Esdras, por la sabiduría de tu Dios que está en ti, debes poner a los gobernantes y jueces para que tengan autoridad sobre todas las personas a oeste del río que tienen conocimiento de las leyes de tu Dios; y tú debes dar enseñanza a quien no tiene conocimiento de ellos.
Ndipo iwe, Ezara, monga mwa nzeru za Mulungu wako zimene uli nazo, usankhe oyendetsa zinthu ndi oweruza kuti azilamulira anthu onse okhala ku dera la Patsidya pa Yufurate, onse amene amadziwa malamulo a Mulungu wako. Ndipo uphunzitse aliyense amene sawadziwa.
26 Y si alguien no cumple la ley de tu Dios y la ley del rey, tenga cuidado de que se le aplique un castigo, ya sea por muerte o destierro de su país o quitándole sus bienes o poniéndolo en prisión.
Ndipo amene sadzamvera lamulo la Mulungu wako ndi lamulo la mfumu alangidwe kolimba kapena aphedwe kapena achotsedwe mʼdzikolo, kapena katundu wake alandidwe, kapena aponyedwe mʼndende.
27 Alabado sea el Señor, el Dios de nuestros padres, que ha puesto tal cosa en el corazón del rey, para reparar el templo del Señor que está en Jerusalén;
Ezara anati atamandike Yehova, Mulungu wa makolo athu, amene wayika ichi mu mtima wa mfumu kuti alemekeze Nyumba ya Yehova ya ku Yerusalemu mʼnjira imeneyi.
28 Y me ha dado misericordia ante el rey y su gobierno y ante todos los grandes capitanes del rey. Y fui fortalecido por la mano del Señor mi Dios que estaba sobre mí, y reuní a los principales hombres de Israel para que subieran conmigo.
Ameneyonso waonetsa chikondi chake chosasinthika kwa ine pamaso pa mfumu, alangizi ake ndi nduna zake zamphamvu kuti andikomere mtima. Choncho ndinalimba mtima popeza Yehova, Mulungu wanga anali nane, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Israeli kuti apite nane pamodzi.

< Esdras 7 >