< Oseas 2 >

1 DECID á vuestros hermanos, Ammi, y á vuestras hermanas, Ruhama:
“Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’”
2 Pleitead con vuestra madre, pleitead; porque ella no es mi mujer, ni yo su marido; quite pues sus fornicaciones de su rostro, y sus adulterios de entre sus pechos;
“Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo, pakuti si mkazi wanga, ndipo ine sindine mwamuna wake. Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake, ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
3 No sea que yo la despoje desnuda, y la haga tornar como el día en que nació, y la ponga como un desierto, y la deje como tierra seca, y la mate de sed.
Akapanda kutero ndidzamuvula, ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa; ndidzamuwumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndi kumupha ndi ludzu.
4 Ni tendré misericordia de sus hijos: porque son hijos de fornicaciones.
Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake, chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
5 Porque su madre fornicó; la que los engendró fué avergonzada; porque dijo: Iré tras mis amantes, que me dan mi pan y mi agua, mi lana y mi lino, mi aceite y mi bebida.
Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi. Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga, zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
6 Por tanto, he aquí yo cerco tu camino con espinas, y la cercaré con seto, y no hallará sus caminos.
Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga; ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
7 Y seguirá sus amantes, y no los alcanzará; buscarálos, y no los hallará. Entonces dirá: Iré, y volveréme á mi primer marido; porque mejor me iba entonces que ahora.
Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza; adzazifunafuna koma sadzazipeza. Pamenepo iye adzati, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja, pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
8 Y ella no reconoció que yo le daba el trigo, y el vino, y el aceite, y que les multipliqué la plata y el oro con que hicieron á Baal.
Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta. Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide, zimene ankapangira mafano a Baala.
9 Por tanto yo tornaré, y tomaré mi trigo á su tiempo, y mi vino á su sazón, y quitaré mi lana y mi lino [que había dado] para cubrir su desnudez.
“Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola, ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa. Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa, zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
10 Y ahora descubriré yo su locura delante de los ojos de sus amantes, y nadie la librará de mi mano.
Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake pamaso pa zibwenzi zake; palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
11 Y haré cesar todo su gozo, sus fiestas, sus nuevas lunas y sus sábados, y todas sus festividades.
Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse: zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano, za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
12 Y haré talar sus vides y sus higueras, de que ha dicho: Mi salario me son, que me han dado mis amantes. Y reducirélas á un matorral, y las comerán las bestias del campo.
Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu, imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake. Ndidzayisandutsa chithukuluzi, ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
13 Y visitaré sobre ella los tiempos de los Baales, á los cuales incensaba, y adornábase de sus zarcillos y de sus joyeles, é íbase tras sus amantes olvidada de mí, dice Jehová.
Ndidzamulanga chifukwa cha masiku amene anafukiza lubani kwa Abaala; anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali ndipo anathamangira zibwenzi zake, koma Ine anandiyiwala,” akutero Yehova.
14 Empero he aquí, yo la induciré, y la llevaré al desierto, y hablaré á su corazón.
“Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo; ndidzapita naye ku chipululu ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
15 Y daréle sus viñas desde allí, y el valle de Achôr por puerta de esperanza; y allí cantará como en los tiempos de su juventud, y como en el día de su subida de la tierra de Egipto.
Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa, ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo. Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake, monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.
16 Y será que en aquel tiempo, dice Jehová, me llamarás Marido mío, y nunca más me llamarás Baali.
“Tsiku limeneli,” Yehova akuti, “udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’ sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
17 Porque quitaré de su boca los nombres de los Baales, y nunca más serán mentados por sus nombres.
Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake; sadzatchulanso mayina awo popemphera.
18 Y haré por ellos concierto en aquel tiempo con las bestias del campo, y con las aves del cielo, y con las serpientes de la tierra: y quebraré arco, y espada, y batalla de la tierra, y harélos dormir seguros.
Tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga. Ndidzachotsa mʼdzikomo uta, lupanga ndi zida zonse zankhondo, kuti onse apumule mwamtendere.
19 Y te desposaré conmigo para siempre; desposarte he conmigo en justicia, y juicio, y misericordia, y miseraciones.
Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya; ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro, mwachikondi ndi mwachifundo.
20 Y te desposaré conmigo en fe, y conocerás á Jehová.
Ndidzakutomera mokhulupirika ndipo udzadziwa Yehova.
21 Y será que en aquel tiempo responderé, dice Jehová, yo responderé á los cielos, y ellos responderán á la tierra;
“Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,” akutero Yehova. “Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;
22 Y la tierra responderá al trigo, y al vino, y al aceite, y ellos responderán á Jezreel.
ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo zidzamvera Yezireeli.
23 Y sembraréla para mí en la tierra, y tendré misericordia de Lo-ruhama: y diré á Lo-ammi: Pueblo mío tú; y él dirá: Dios mío.
Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’”

< Oseas 2 >