< Gálatas 4 >

1 TAMBIÉN digo: Entre tanto que el heredero es niño, en nada difiere del siervo, aunque es señor de todo;
Chimene ndikunena ndi chakuti, ngati mlowamʼmalo akali wamngʼono, sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti chuma chonse ndi chake.
2 Mas está debajo de tutores y curadores hasta el tiempo señalado por el padre.
Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso anthu oyangʼanira chuma mpaka nthawi imene abambo ake anakhazikitsa.
3 Así también nosotros, cuando éramos niños, éramos siervos bajo los rudimentos del mundo.
Chomwechonso, ife pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo ya dziko lapansi.
4 Mas venido el cumplimiento del tiempo, Dios envió su Hijo, hecho de mujer, hecho súbdito á la ley,
Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, wobadwa mwa mayi, wobadwa pansi pa lamulo,
5 Para que redimiese á los que estaban debajo de la ley, á fin de que recibiésemos la adopción de hijos.
kudzawombola amene anali pansi pa lamulo, kuti tilandiridwe monga ana.
6 Y por cuanto sois hijos, Dios envió el Espíritu de su Hijo en vuestros corazones, el cual clama: Abba, Padre.
Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.”
7 Así que ya no eres más siervo, sino hijo; y si hijo, también heredero de Dios por Cristo.
Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.
8 Antes, en otro tiempo, no conociendo á Dios, servíais á los que por naturaleza no son dioses:
Koma poyamba pamene simunkamudziwa Mulungu, munali akapolo a zimene mwachilengedwe si milungu.
9 Mas ahora, habiendo conocido á Dios, ó más bien, siendo conocidos de Dios, ¿cómo os volvéis de nuevo á los flacos y pobres rudimentos, en los cuales queréis volver á servir?
Koma tsopano pakuti mukumudziwa Mulungu, kapena ndinene kuti Mulungu akukudziwani, nʼchifukwa chiyani mukubwereranso ku miyambo yofowoka ndi yomvetsa chisoni? Kodi mukufuna musandukenso akapolo?
10 Guardáis los días, y los meses, y los tiempos, y los años.
Mumasunga masiku, miyezi ndi nyengo ndi zaka.
11 Temo de vosotros, que no haya trabajado en vano en vosotros.
Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe.
12 Hermanos, os ruego, sed como yo, porque yo soy como vosotros: ningún agravio me habéis hecho.
Abale, ndikukudandaulirani, mukhale ngati ine, popeza ine ndinakhala ngati inu. Inu simunandilakwire.
13 Que vosotros sabéis que por flaqueza de carne os anuncié el evangelio al principio:
Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka.
14 Y no desechasteis ni menospreciasteis mi tentación que [estaba] en mi carne: antes me recibisteis como á un ángel de Dios, como á Cristo Jesús.
Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini.
15 ¿Dónde está pues vuestra bienaventuranza? porque yo os doy testimonio que si se pudiera [hacer], os hubierais sacado vuestros ojos para dármelos.
Kodi chimwemwe chanu chonse chija chili kuti? Ine nditha kuchitira umboni kuti, ngati kukanatheka, inu mukanakolowola maso anu ndi kundipatsa.
16 ¿Heme pues hecho vuestro enemigo, diciéndoos la verdad?
Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi?
17 Tienen celos de vosotros, [pero] no bien: antes os quieren echar fuera para que vosotros los celéis á ellos.
Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo.
18 Bueno es ser celosos en bien siempre; y no solamente cuando estoy presente con vosotros.
Nʼkwabwino kuchita changu, ngati cholingacho chili chabwino ndi kukhala otero nthawi zonse osati pokhapo pamene ine ndili ndi inu.
19 Hijitos míos, que vuelvo otra vez á estar de parto de vosotros, hasta que Cristo sea formado en vosotros;
Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu,
20 Querría cierto estar ahora con vosotros, y mudar mi voz; porque estoy perplejo en cuanto á vosotros.
ine ndikanakonda ndikanakhala nanu tsopano kuti ndisinthe mawu anga, chifukwa ndathedwa nanu nzeru.
21 Decidme, los que queréis estar debajo de la ley, ¿no habéis oído la ley?
Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena?
22 Porque escrito está que Abraham tuvo dos hijos; uno de la sierva, el otro de la libre.
Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu.
23 Mas el de la sierva nació según la carne; pero el de la libre [nació] por la promesa.
Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.
24 Las cuales cosas son dichas por alegoría: porque estas [mujeres] son los dos pactos; el uno ciertamente del monte Sinaí, el cual engendró para servidumbre, que es Agar.
Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo.
25 Porque Agar ó Sinaí es un monte de Arabia, el cual es conjunto á la que ahora es Jerusalem, la cual sirve con sus hijos.
Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake.
26 Mas la Jerusalem de arriba libre es; la cual es la madre de todos nosotros.
Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.
27 Porque está escrito: Alégrate, estéril, que no pares: prorrumpe y clama, la que no estás de parto; porque más son los hijos de la dejada, que de la que tiene marido.
Pakuti kwalembedwa kuti, “Sangalala, iwe mayi wosabala, amene sunabalepo mwana; imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa.”
28 Así que, hermanos, nosotros como Isaac somos hijos de la promesa.
Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake.
29 Empero como entonces el que era engendrado según la carne, perseguía al que [había nacido] según el Espíritu, así también ahora.
Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero.
30 Mas ¿qué dice la Escritura? Echa fuera á la sierva y á su hijo; porque no será heredero el hijo de la sierva con el hijo de la libre.
Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.”
31 De manera, hermanos, que no somos hijos de la sierva, mas de la libre.
Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.

< Gálatas 4 >