< Números 30 >

1 Y habló Moisés a los príncipes de las tribus de los hijos de Israel, diciendo: Esto es lo que Jehová ha mandado:
Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi:
2 Cuando alguno hiciere voto a Jehová, o jurare juramento, ligando su alma con obligación, no contaminará su palabra: conforme a todo lo que salió por su boca, hará.
Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena.
3 Mas la mujer cuando hiciere voto a Jehová, y se ligare con obligación en casa de su padre en su mocedad;
“Pamene munthu wamkazi amene akukhalabe mʼnyumba ya abambo ake alumbira kwa Yehova kuti adzachita zimene walonjeza pa ubwana wake,
4 Si su padre oyere su voto, y la obligación con que ligó su alma, y su padre callare a él, todos los votos de ella serán firmes, y toda obligación, con que hubiere obligado su alma, será firme:
abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija.
5 Mas si su padre lo vedare el día que oyere todos sus votos, y sus ataduras con que ella hubiere ligado su alma, no serán firmes, y Jehová la perdonará, por cuanto su padre lo vedó.
Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza.
6 Empero si fuere casada, e hiciere votos, o pronunciare de sus labios cosa con que obligue su alma;
“Ngati akwatiwa atalumbira kale kapena ngati alonjeza mofulumira ndi pakamwa pake,
7 Si su marido lo oyere, y cuando lo oyere, callare a ello, los votos de ella serán firmes, y la atadura con que ligó su alma, será firme.
mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma wosanenapo kanthu, mkaziyo achitedi zomwe walumbirazo. Achite ndithu zomwe walonjeza zija.
8 Mas si cuando su marido lo oyó, lo vedó, entonces el voto que ella hizo, y lo que pronunció de sus labios con que ató su alma, será ninguno, y Jehová la perdonará.
Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira.
9 Empero todo voto de viuda, o repudiada, con que ligare su alma, será firme.
“Mayi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi.
10 Mas si lo hubiere hecho en casa de su marido, y hubiere ligado su alma con obligación de juramento;
“Koma ngati mayi wokwatiwa alumbira nalonjeza kuti adzachitadi zimene walonjeza,
11 Si su marido oyó, y calló a ello, y no lo vedó, entonces todos sus votos serán firmes, y toda obligación con que hubiere ligado su alma, será firme.
mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma osayankhulapo kanthu, osamuletsa, ayenera kuchitadi zonse zimene walumbira ndi zonse zimene walonjeza.
12 Mas si su marido los anuló el día que los oyó, todo lo que salió de sus labios, cuanto a sus votos, y cuanto a la obligación de su alma, será ninguno, su marido los anuló, y Jehová la perdonará.
Koma ngati mwamuna wake amva ndi kumuletsa kuti asachite zomwe walumbirazo, palibe lamulo lomukakamiza mayiyo kuchita zomwe walumbirazo kapenanso zimene walonjeza. Popeza mwamuna wake wamuletsa, Yehova adzamukhululukira mayiyo.
13 Todo voto, o todo juramento de obligación para afligir el alma, su marido lo confirmará, o su marido lo anulará.
Mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana zimene mayiyo walumbira kapena zimene walonjeza zokhudza kudzilanga yekha.
14 Empero si su marido callare a ello de día en día, entonces confirmó todos sus votos, y todas las obligaciones, que están sobre ella; confirmólas, por cuanto calló a ello, el día que lo oyó.
Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira.
15 Mas si las anulare después que las oyó, entonces él llevará el pecado de ella.
Koma ngati mwamunayo amukaniza patapita kanthawi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa mʼmalo mwa mayiyo.”
16 Estas son las ordenanzas que Jehová mandó a Moisés para entre el varón y su mujer, y entre el padre y su hija en su mocedad en casa de su padre.
Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo.

< Números 30 >