< Jueces 5 >

1 Y aquel día cantó Débora y Barac hijo de Abinoem, diciendo:
“Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:
2 Porque ha vengado las injurias de Israel, porque el pueblo se ha ofrecido de su voluntad, load a Jehová.
“Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli; ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu, tamandani Yehova:
3 Oíd reyes: estád atentos príncipes, yo cantaré a Jehová: diré salmos a Jehová Dios de Israel.
“Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu! Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova, Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.
4 Cuando saliste de Seir, oh Jehová, cuando te apartaste del campo de Edom, la tierra tembló, y los cielos destilaron, y las nubes gotearon aguas.
“Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri, pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu, dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka nigwetsa madzi.
5 Los montes se derritieron delante de Jehová, este Sinaí, delante de Jehová Dios de Israel.
Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israeli.
6 En los días de Samgar hijo de Anat, en los días de Jahel cesaron los caminos; y los que andaban por las sendas, se apartaban por sendas torcidas.
“Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati, pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa; alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.
7 Las aldeas habían cesado en Israel, habían cesado: hasta que yo Débora me levanté, me levanté madre en Israel.
Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi mpaka pamene iwe Debora unafika; unafika ngati mayi ku Israeli.
8 En escogiendo nuevos dioses, la guerra estaba a las puertas: ¿Se veía escudo o lanza entre cuarenta mil en Israel?
Pamene anasankha milungu ina, nkhondo inabwera ku zipata za mzinda, ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
9 Mi corazón es a los príncipes de Israel, a los voluntarios en el pueblo, load a Jehová.
Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli, uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu. Tamandani Yehova!
10 Los que cabalgáis en asnas blancas, los que presidís en juicio, y los que andáis por el camino, hablád.
“Inu okwera pa abulu oyera, okhala pa zishalo, ndi inu oyenda pa msewu, yankhulani.
11 A causa del estruendo de los flecheros quitado de entre los que sacan las aguas: allí recuenten las justicias de Jehová, las justicias de sus aldeas en Israel. Ahora el pueblo de Jehová descenderá a las puertas.
Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta; kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana; akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli. “Choncho anthu a Yehova anasonkhana ku zipata za mzinda.
12 Despierta, despierta Débora, despierta, despierta, di canción. Levántate Barac, y lleva tus cautivos, hijo de Abinoem.
Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera; tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Iwe Baraki! nyamuka Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’
13 Entonces ha hecho que el que quedó del pueblo; señoree los magníficos: Jehová me hizo enseñorear sobre los fuertes.
“Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo; anthu a Yehova anapita kukamenyera Yehova nkhondo kulimbana ndi adani amphamvu.
14 De Efraím salió su raíz contra Amalec: tras ti vino Ben-jamín contra tus pueblos. De Maquir descendieron príncipes: y de Zabulón los que solían tratar cincel de escriba.
Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu; akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako. Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri, ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
15 Príncipes también de Isacar fueron con Débora: y también Isacar, como Barac, se puso a pie en el valle: de las divisiones de Rubén son grandes las disputas del corazón.
Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora; inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki, ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira. Koma pakati pa mafuko a Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
16 ¿Por qué te quedaste entre las majadas, para oír los silvos de los rebaños? De las divisiones de Rubén grandes son las disputas del corazón.
Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera zitoliro zoyitanira nkhosa? Pakati pa anthu a fuko la Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
17 Galaad se quedó de la otra parte del Jordán: y Dan ¿por qué habitó junto a los navíos? Aser se asentó en la ribera de la mar, y en sus quebraduras se quedó.
Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani. Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi? Aseri anali pa gombe la Nyanja; anangokhala mʼmadooko mwawo.
18 El pueblo de Zabulón puso su vida a la muerte, y Neftalí en las alturas del campo.
Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa. Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.
19 Vinieron reyes, y pelearon: entonces pelearon los reyes de Canaán en Tane junto a las aguas de Mageddo, mas ninguna ganancia de dinero llevaron.
“Mafumu anabwera, anachita nkhondo; mafumu Akanaani anachita nkhondo ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido, koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
20 De los cielos pelearon: las estrellas desde sus caminos pelearon contra Sísera.
Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo, zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
21 El arroyo de Cisón los barrió, el arroyo de las antigüedades, el arroyo de Cisón: pisaste, oh alma mía, con fortaleza.
Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola. Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
22 Las uñas de los caballos se embotaron entonces, por los encuentros, los encuentros de sus valientes.
Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu, akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
23 Maldecíd a Meros, dijo el ángel de Jehová: maldecíd con maldición a sus moradores: porque no vinieron en socorro a Jehová, en socorro a Jehová contra los fuertes.
Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’ ‘Tembererani nzika zake mwaukali, chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova, kulimbana ndi adani ake amphamvu.’
24 Bendita sea sobre las mujeres Jahel la mujer de Jeber Cineo: sobre las mujeres sea bendita en la tienda.
“Akhale wodala kupambana akazi onse, Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.
25 El pidió agua, y ella le dio leche: en tazón de nobles le presentó manteca.
Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka; anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.
26 Su mano tendió a la estaca, y su diestra al mazo de trabajadores, y majó a Sísera; hirió su cabeza; llagó, y pasó sus sienes.
Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake, anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja. Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake, ndi kumubowola mu litsipa mwake.
27 Cayó encorvado entre sus pies, quedó tendido: entre sus pies cayó encorvado: donde se encorvó, allí cayó muerto.
Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa, anagwa; iye anagona pamenepo. Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa; pamene anagwera, pamenepo anaferapo.
28 La madre de Sísera asomándose a la ventana aulla, mirando por entre las rejas, diciendo: ¿Por qué se detiene su carro, que no viene? ¿por qué se tardan las ruedas de sus carros?
“Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera; nafuwula mokweza kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika? Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
29 Las sabias mujeres de sus príncipes le respondían: y aun ella a sí misma se respondía:
Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha, ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,
30 ¿No han hallado despojos y los están repartiendo? a cada uno una moza, o dos: los despojos de colores, a Sísera; los despojos bordados de colores: la ropa de color bordada de ambas partes, para el cuello del despojo.
‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane; akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri. Sisera akumupatsa zofunkha: zovala zonyikidwa mu utoto, zoti ndizivala mʼkhosi zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’
31 Así perezcan todos tus enemigos oh Jehová: mas los que le aman, sean como el sol cuando nace en su fortaleza. Y la tierra reposó cuarenta años.
“Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke, koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa pamene lituluka ndi mphamvu zake.” Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.

< Jueces 5 >