< Salmos 40 >
1 Pacientemente esperé a Yavé, Y se inclinó hacia mí y escuchó mi clamor.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
2 Me sacó del pozo de la desesperación, del lodo cenagoso. Asentó mis pies sobre una roca y afirmó mis pasos.
Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko, mʼthope ndi mʼchithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
3 Puso en mi boca un canto nuevo, Alabanza a nuestro ʼElohim. Muchos verán esto. Temerán y confiarán en Yavé
Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga, nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga. Ambiri adzaona, nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.
4 ¡Cuán bendecido es el varón quien fijó en Yavé su confianza, Que no mira a los soberbios Ni a los que se desvían hacia la falsedad!
Ndi wodala munthu amakhulupirira Yehova; amene sayembekezera kwa odzikuza, kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
5 ¡Oh Yavé, mi ʼElohim, Aumentaste tus maravillas y tus designios para nosotros! ¡Nadie puede compararse contigo! Si los anuncio y hablo de ellos, No pueden ser enumerados.
Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza.
6 Sacrificio y ofrenda no te agradan. Abriste mis oídos. No demandas holocausto y sacrificio que apacigua.
Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna, koma makutu anga mwawatsekula; zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo Inu simunazipemphe.
7 Entonces dije: Aquí vengo. En la cabecilla del rollo está escrito acerca de Mí.
Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera. Mʼbuku mwalembedwa za ine.
8 Oh mi ʼElohim, hacer tu voluntad me agrada, Y tu Ley está dentro de mi corazón.
Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga; lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”
9 Anuncié justicia en la gran congregación. Ciertamente no refrené mis labios. Tú lo sabes, oh Yavé,
Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova.
10 Ni encubrí tu justicia dentro de mi corazón. He proclamado tu fidelidad y tu salvación. No oculté de la gran congregación tu misericordia y tu verdad.
Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu.
11 Tú, oh Yavé, no retengas de mí tu compasión. Que tu misericordia y tu verdad me guarden siempre.
Musandichotsere chifundo chanu Yehova; chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
12 Porque me rodearon calamidades incontables. Me alcanzaron mis iniquidades, Y no puedo levantar la vista. Son más numerosas que los cabellos de mi cabeza, Y mi corazón me falla.
Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira; machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona. Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga, ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.
13 ¡Oh Yavé, complácete en librarme! ¡Apresúrate, oh Yavé, a socorrerme!
Pulumutseni Yehova; Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.
14 ¡Sean avergonzados y humillados Los que buscan mi vida para destruirla! Sean vueltos atrás y deshonrados Los que se deleitan en mi calamidad.
Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene amakhumba chiwonongeko changa abwezedwe mwamanyazi.
15 Queden consternados a causa de su vergüenza Los que me dicen: ¡Ea, ea!
Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!” abwerere akuchita manyazi.
16 ¡Regocíjense y alégrense en Ti todos los que te buscan! Digan siempre los que aman tu salvación: ¡Engrandecido sea Yavé!
Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”
17 Aunque estoy afligido y necesitado, ʼAdonay pensará en mí. Tú eres mi ayuda y mi Libertador. ¡Mi ʼElohim, no te tardes!
Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.