< Jueces 10 >

1 Después de Abimelec, Tola, hijo de Púa, hijo de Dodo, varón de Isacar, quien vivía en Samir, en la región montañosa de Efraín, se levantó para librar a Israel.
Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu.
2 Éste juzgó a Israel 23 años y murió. Fue sepultado en Samir.
Iye anatsogolera Aisraeli kwa zaka 23, ndipo anamwalira ndi kuyikidwa ku Samiri.
3 Tras él se levantó Jaír galaadita, quien juzgó a Israel 22 años.
Atafa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi, amene anatsogolera Israeli kwa zaka 22.
4 Tuvo 30 hijos que cabalgaban en 30 asnos y poseían 30 villas en la tierra de Galaad, que hasta hoy se llaman Villas de Jaír.
Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi.
5 Jaír murió y fue sepultado en Camón.
Atamwalira Yairi anayikidwa mʼmanda ku Kamoni.
6 Pero los hijos de Israel volvieron a hacer lo malo ante Yavé y sirvieron a los baales y a Astarot, a los ʼelohim de Siria, de Sidón, de Moab, de los hijos de Amón y de los filisteos. Abandonaron a Yavé y no le sirvieron.
Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova.
7 Se encendió la ira de Yavé contra Israel y los entregó en las manos de los filisteos y de los hijos de Amón,
Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni.
8 quienes a partir de aquel año oprimieron y vejaron a los israelitas durante 18 años, a todos los hijos de Israel que vivían al otro lado del Jordán en Galaad, la tierra de los amorreos.
Iwowa anawagonjetseratu Aisraeli mʼchaka chimenechi, ndipo kwa zaka 18 anakhala akusautsa Aisraeli onse amene anali pa tsidya la Yorodani, mʼdziko la Aamori ku Giliyadi.
9 Así que los hijos de Amón cruzaron el Jordán para combatir contra Judá, Benjamín y la casa de Efraín. Esto angustió mucho a Israel.
Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri.
10 Entonces los hijos de Israel clamaron a Yavé: ¡Pecamos contra ti, porque abandonamos a nuestro ʼElohim para servir a los baales!
Kenaka Aisraeli analira kwa Yehova kuti, “Ife takuchimwirani popeza tasiya Inu Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.”
11 Yavé dijo a los hijos de Israel: ¿No los libré Yo de Egipto, de los amorreos, de los hijos de Amón y de los filisteos?
Yehova anawafunsa kuti, “Suja ine ndinakupulumutsani kwa Aigupto, Aamori, Aamoni ndi Afilisti?
12 Cuando los sidonios, los amalecitas y los maonitas los oprimieron, y clamaron a Mí, Yo los libré de su mano.
Ndiponso pamene Asidoni, Aamaleki ndi Amoni anakuzunzani, inu nʼkulirira kwa ine suja ndinakupulumutsani kwa anthu amenewa?
13 Pero ustedes me abandonaron y sirvieron a otros ʼelohim. Por tanto, no los libraré.
Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso.
14 ¡Vayan, clamen a los ʼelohim que se eligieron! ¡Que ellos los salven en el tiempo de su angustia!
Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.”
15 Entonces los hijos de Israel respondieron a Yavé: ¡Pecamos! Haz con nosotros lo que te parezca bien. Solo te rogamos que nos libres hoy.
Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.”
16 Apartaron los ʼelohim extraños de en medio de ellos y sirvieron a Yavé, y Él no soportó más la aflicción de Israel.
Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira.
17 Entonces los hijos de Amón se reunieron y acamparon en Galaad. También los hijos de Israel se reunieron y acamparon en Mizpa.
Tsono Aamoni anasonkhana ndi kumanga zithando za nkhondo ku Giliyadi. Nawonso Aisraeli anasonkhana ndi kumanga zithando zawo za nkhondo ku Mizipa.
18 Y cada uno de los jefes del pueblo de Galaad decían a su prójimo: Cualquier hombre que comience la lucha contra los hijos de Amón será caudillo de todos los habitantes de Galaad.
Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”

< Jueces 10 >