< Josué 8 >
1 Yavé dijo a Josué: ¡No temas ni desmayes! Toma contigo a toda la gente de guerra. Vé y sube a Hai. Mira, Yo entregué en tu mano al rey de Hai, su pueblo, su ciudad y su tierra.
Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako.
2 Tú harás con Hai y su rey como hiciste con Jericó y su rey, solo que podrán tomar para ustedes su botín y su ganado. Prepara una emboscada contra la ciudad, por detrás.
Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”
3 Josué se levantó con toda la gente de guerra para subir contra Hai. Escogió Josué 30.000 hombres fuertes, a los cuales envió de noche.
Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku
4 Les mandó: Miren, pondrán una emboscada a la ciudad, detrás de ella. No se alejen mucho de la ciudad, y estén todos preparados.
nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo.
5 Después yo y todo el pueblo que está conmigo nos acercaremos a la ciudad, y cuando ellos salgan contra nosotros, como hicieron antes, huiremos delante de ellos.
Ine ndi gulu langa lonse tikayamba kuwuputa mzindawu, ndipo akadzangotuluka kudzalimbana nafe, ife tidzawathawa monga tinachitira poyamba.
6 Ellos saldrán tras nosotros, y haremos que se aparten de la ciudad, porque dirán: ¡Huyen de nosotros como la primera vez!
Iwo adzatithamangitsa mpaka titawakokera kutali ndi mzindawo, pakuti iwo adzati, ‘Akutithawa monga anachitira poyamba.’ Pamene ife tizidzathawa,
7 Mientras huimos de ellos, ustedes saldrán de la emboscada y tomarán la ciudad, pues Yavé su ʼElohim la entregó en su mano.
inu mudzatuluke pamene mwabisalapo ndi kulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mzindawo.
8 Cuando la ocupen, la incendiarán con fuego. Harán conforme a la Palabra de Yavé. Miren que se lo mandé.
Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”
9 Entonces Josué los envió, y fueron a la emboscada. Se ubicaron entre Bet-ʼEl y Hai, al occidente de Hai. Josué pasó aquella noche en medio del pueblo.
Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo.
10 Josué se levantó muy de mañana, pasó revista al pueblo, y subió al frente del pueblo contra Hai junto con los ancianos de Israel.
Mmawa mwake, Yoswa anadzuka nayitana asilikali ake. Tsono iye pamodzi ndi akuluakulu a Aisraeli anatsogola kupita ku Ai.
11 Toda la gente de guerra que lo acompañaba subió también y se acercaban hasta llegar frente a la ciudad. Acamparon al lado norte de Hai, y dejó el valle por medio entre él y Hai.
Gulu lonse la nkhondo limene linali ndi iye linatsogolako ndi kukamanga zithando pafupi ndi mzindawo chakumpoto mopenyana nawo. Pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa.
12 Entonces tomó unos 5.000 hombres, y los emboscó entre Bet-ʼEl y Hai, al occidente de la ciudad.
Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo.
13 Así dispusieron al pueblo: todo el ejército al norte de la ciudad, y su retaguardia al occidente de la ciudad, mientras Josué pasó la noche en el medio del valle.
Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa.
14 Sucedió que cuando el rey de Hai vio esto, los hombres de la ciudad se apresuraron. Él y todo su pueblo madrugaron y salieron a la batalla contra Israel en el lugar designado frente al Arabá, pero no sabía que había una emboscada contra él detrás de la ciudad.
Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo.
15 Entonces Josué y todo Israel fingieron que estaban derrotados y huyeron por el camino del desierto.
Yoswa ndi Aisraeli onse anachita ngati agonja ndi kumathawira ku chipululu.
16 Todo el pueblo que estaba en la ciudad fue convocado para perseguirlos. Persiguieron a Josué y se apartaron de la ciudad.
Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo.
17 No quedó ni un hombre en Hai o en Bet-ʼEl que no saliera a perseguir a Israel, y dejaron abierta la ciudad.
Palibe munthu wamwamuna wa mzinda wa Ai kapena wa Beteli amene sanatuluke kukapirikitsa Aisraeli. Iwo anasiya mzinda wosatseka ndi kumapirikitsa Aisraeli.
18 Entonces Yavé dijo a Josué: Extiende la lanza que llevas en tu mano hacia Hai, porque la entregaré en tu mano. Y Josué extendió hacia la ciudad la lanza que tenía en su mano.
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai.
19 Tan pronto como él la extendió, los emboscados salieron rápidamente de su lugar y corrieron. Entraron en la ciudad, la capturaron y se apresuraron a ponerle fuego.
Atangotambalitsa dzanja lake, anthu amene anabisala aja ananyamuka msangamsanga pamalo pawo ndi kuthamangira kutsogolo. Iwo analowa mu mzindamo ndi kuwulanda ndipo anawutentha mofulumira.
20 Cuando los hombres de Hai volvieron la cara y miraron, ciertamente la humareda de la ciudad subía al cielo. No tuvieron lugar para huir, ni por un lado ni por el otro, porque el pueblo que huía al desierto regresó contra sus perseguidores.
Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa.
21 Pues Josué y todo Israel, al ver que los de la emboscada habían tomado la ciudad, y que la humareda de la ciudad subía, regresaron y atacaron a los hombres de Hai.
Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai.
22 Los otros salieron de la ciudad a su encuentro, y así quedaron en medio de Israel, unos por una parte y otros por la otra. Así los mataron hasta que no quedó algún sobreviviente ni fugitivo.
Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa
23 Pero el rey de Hai fue capturado vivo y lo llevaron a Josué.
kupatula mfumu ya ku Ai yokha imene anayigwira nabwera nayo kwa Yoswa.
24 Cuando Israel puso fin a la matanza de todos los habitantes de Hai en el campo, aun en el desierto hasta donde los persiguieron, y todos cayeron a filo de espada hasta que fueron consumidos, sucedió que todo Israel regresó a Hai y la arrasaron a filo de espada.
Aisraeli aja atatha kupha anthu onse a ku Ai amene anali mʼthengo ndi mʼchipululu kumene anawapirikitsira, onse anabwerera ku Ai ndi kupha onse amene anali mu mzindamo.
25 Los que cayeron en aquel día, hombres y mujeres, fueron 12.000, todos los de Hai,
Chiwerengero cha anthu onse a ku Ai, amuna ndi akazi, amene anaphedwa pa tsiku limeneli chinali 12,000.
26 porque Josué no retrajo su mano con la cual sostenía la lanza hasta que exterminó a todos los habitantes de Hai.
Yoswa sanatsitse dzanja lake limene ananyamula mkondo mpaka ataona kuti onse amene amakhala mu mzinda wa Ai aphedwa.
27 Israel tomó como botín solo los animales y el despojo de la ciudad, conforme a la Palabra que Yavé ordenó a Josué.
Tsono Aisraeli anatenga zoweta ndi katundu yense wa anthu ophedwa aja, monga momwe Yehova analamulira Yoswa.
28 Luego Josué incendió a Hai y la redujo a un montón de ruinas perpetuas, una desolación que se mantiene hasta hoy.
Pambuyo pake Yoswa anawutentha mzinda wa Ai ndi kuwusiya bwinja monga ulili leromu.
29 Colgó de un árbol al rey de Hai hasta la llegada de la noche, pero al ocultarse el sol, Josué dio orden para que bajaran su cadáver del árbol. Lo echaron en la entrada de la ciudad e hicieron levantar sobre él un gran montón de piedras, que permanece hasta hoy.
Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino.
30 Entonces Josué edificó un altar a Yavé ʼElohim de Israel en la montaña Ebal,
Ndipo Yoswa anamanga guwa lansembe la Yehova Mulungu wa Israeli pa phiri la Ebala.
31 tal como Moisés, esclavo de Yavé, ordenó a los hijos de Israel, según está escrito en el Rollo de la Ley de Moisés, un altar de piedras sin labrar sobre las cuales ningún hombre alzó herramientas de hierro. Ofrecieron holocaustos y sacrificaron ofrendas de paz a Yavé sobre él.
Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano.
32 [Josué] escribió allí sobre las piedras una copia de la Ley de Moisés, la cual escribió en presencia de los hijos de Israel.
Kenaka anthu onse akupenya, Yoswa analemba pa miyala chitsanzo cha malamulo amene Mose analemba.
33 Todo Israel, sus ancianos, oficiales y jueces, estaban en pie a ambos lados del Arca, ante los sacerdotes levitas que cargaban el Arca del Pacto de Yavé. Tanto extranjeros como naturales, la mitad estaba frente a la montaña Gerizim, y la otra mitad frente a la montaña Ebal, tal como Moisés esclavo de Yavé ordenó la primera vez para que bendijeran al pueblo de Israel.
Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli.
34 Después de esto, [Josué] leyó todas las Palabras de la Ley: la bendición y la maldición, conforme a todo lo que está escrito en el Rollo de la Ley.
Pambuyo pake Yoswa anawerenga mawu onse a malamulo, madalitso ndi matemberero monga momwe zinalembedwera mʼbuku la malamulo a Mose.
35 No hubo palabra de todo lo que Moisés ordenó, que Josué no leyera frente a toda la congregación de Israel, tanto a mujeres como a pequeños, y al extranjero que andaba en medio de ellos.
Yoswa anawerenga mawu onse amene Mose analamula, gulu lonse la Israeli limene linasonkhana likumva. Amayi, ana ndi alendo omwe okhala pakati pawo anali pomwepo.