< Job 37 >

1 Por lo cual también se estremece mi corazón y salta fuera de su lugar.
“Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso ndipo ukuchoka mʼmalo mwake.
2 ¡Escuchen atentamente el trueno de su voz y el estruendo que sale de su boca!
Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake, kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake.
3 Suelta sus relámpagos por debajo de todo el cielo, que llegan hasta los confines de la tierra.
Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse ndipo amachitumiza ku dziko lapansi.
4 Tras ellos ruge su voz. Truena ʼEL con voz majestuosa, y aunque sea oída su voz, no los detiene.
Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka. Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero. Pamene wabangula, palibe chimene amalephera kuchita.
5 ʼEL truena con voz maravillosa y hace cosas que no podemos comprender.
Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.
6 A la nieve dice: Cae a la tierra. También a la lluvia y al aguacero torrencial.
Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’ ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’
7 Así hace que todo hombre se retire, para que todos los hombres reconozcan su obra.
Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake. Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo.
8 Las bestias se meten en lugar de descanso y permanecen en sus guaridas.
Zirombo zimakabisala ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo.
9 De su cámara viene la tormenta y el frío de los vientos del norte.
Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake, kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo.
10 Por el soplo de ʼEL se forma el hielo y se congelan las amplias aguas.
Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa.
11 Carga de humedad la densa nube. Dispersa las nubes con sus relámpagos,
Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula, amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo.
12 que giran según su designio para cumplir sus órdenes sobre la superficie de la tierra habitada.
Mulungu amayendetsa mitamboyo mozungulirazungulira dziko lonse lapansi kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.
13 Las hace venir, unas veces como azote, otras, a favor de su tierra y otras por misericordia.
Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu, kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake.
14 Oh Job, escucha esto. Detente y considera las maravillas de ʼEL.
“Abambo Yobu, tamvani izi; imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.
15 ¿Sabes cuándo ʼEloah las establece y hace fulgurar la luz de su nube?
Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani?
16 ¿Conoces tú el equilibrio de las nubes, las obras prodigiosas de Aquél que es perfecto en conocimiento?
Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo, ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro?
17 ¿Por qué están calientes tus ropas cuando la tierra está tranquila a causa del viento del sur?
Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera,
18 ¿Extendiste con Él la bóveda celeste, sólida como un espejo fundido?
kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo limene ndi lolimba ngati chitsulo?
19 Muéstranos qué le diremos. Porque no podemos ordenar nuestras ideas a causa de las tinieblas.
“Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye; sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife.
20 ¿Será necesario informarle lo que yo digo? ¿O debe un hombre desear que sea tragado?
Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu? Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?
21 Ciertamente no es posible mirar la luz oscurecida por las nubes, pero un viento pasa, y la despeja.
Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa, ndi kunyezimira mlengalenga, kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse.
22 Del norte asoma un dorado resplandor. ¡En ʼEloha hay una asombrosa majestad!
Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto; Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.
23 ¡ʼEL-Shadday, a Quien no alcanzamos! Exaltado en poder, Él no hará violencia a la equidad. Es abundante en justicia.
Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa; pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika.
24 Por tanto, los hombres le temen. Él no estima a alguno que cree en su corazón ser sabio.
Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri, kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?”

< Job 37 >