< Oseas 7 >

1 Cuando Yo curaba a Israel se descubrió la iniquidad de Efraín y salieron a la luz las maldades de Samaria. Porque obran con engaño. El ladrón se mete por dentro, y la pandilla despoja por fuera.
Pamene ndichiritsa Israeli, machimo a Efereimu amaonekera poyera ndiponso milandu ya Samariya sibisika. Iwo amachita zachinyengo, mbala zimathyola nyumba, achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
2 No reflexionan en su corazón que Yo tengo presentes todas sus perversidades. Sus propias acciones los cercaron y están delante de Mí.
Koma sazindikira kuti Ine ndimakumbukira zoyipa zawo zonse. Azunguliridwa ndi zolakwa zawo; ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.
3 Alegran al rey con sus maldades, y a los príncipes con sus mentiras.
“Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo, akalonga amasekerera mabodza awo.
4 Todos ellos son adúlteros. Son como horno encendido que el panadero solo deja de atizar desde el amasado hasta la fermentación.
Onsewa ndi anthu azigololo, otentha ngati moto wa mu uvuni, umene wophika buledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
5 El día de nuestro rey, al calor del vino, los príncipes lo contaminaron. Él extendió su mano a los escarnecedores,
Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu akalonga amaledzera ndi vinyo, ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
6 Porque como a un horno acercaron su corazón a la intriga. Toda la noche dormita su ira. Por la mañana arde como llama de fuego.
Mitima yawo ili ngati uvuni; amayandikira Mulungu mwachiwembu. Ukali wawo umanyeka usiku wonse, mmawa umayaka ngati malawi a moto.
7 Todos arden como un horno, devoran a sus gobernantes. Todos sus reyes van a la caída. Pero entre ellos no hay quien clame a Mí.
Onsewa ndi otentha ngati uvuni, amapha olamulira awo. Mafumu awo onse amagwa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.
8 Efraín se mezcló con los pueblos. Efraín es una torta no volteada.
“Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena; Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
9 Le socavan su fuerza los extraños, pero él no se da cuenta. El cabello cano se esparce en él, pero él no se da cuenta.
Alendo atha mphamvu zake, koma iye sakuzindikira. Tsitsi lake layamba imvi koma iye sakudziwa.
10 La propia soberbia de Israel testifica en contra suya, pero ellos no se vuelven a Yavé su ʼElohim. A pesar de todo, no lo buscan.
Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa, koma pa zonsezi iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake kapena kumufunafuna.
11 Efraín es una paloma ingenua y atolondrada. Claman a Egipto, acuden a Asiria.
“Efereimu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru. Amayitana Igupto namapita ku Asiriya.
12 Tan pronto como Yo eche mi red sobre ellos, y como a pájaros los haré caer. Los atraparé tan pronto como escuche la bandada.
Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga; ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga. Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi ndidzawakola.
13 ¡Ay de ellos, porque se apartaron de Mí! ¡Destrucción sobre ellos, porque se rebelaron contra Mí! ¿Los redimiré cuando ellos me calumnian?
Tsoka kwa iwo, chifukwa andisiya Ine! Chiwonongeko kwa iwo, chifukwa andiwukira! Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa koma amayankhula za Ine monama.
14 Aun cuando gimen en sus camas no claman a Mí de corazón. Se apartan de Mí y se reúnen para el trigo y para el vino.
Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima, koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo. Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano, koma amandifulatira.
15 Aunque Yo adiestré y fortalecí sus brazos, ellos piensan mal contra Mí.
Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa, koma amandikonzera chiwembu.
16 Se vuelven, pero no a ʼElyón. Son como arco que yerra. Sus príncipes pues caerán a espada por la ira de su propia lengua. Esto será su escarnio en la tierra de Egipto.
Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba; ali ngati uta woonongeka. Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mawu awo achipongwe. Motero iwo adzasekedwa mʼdziko la Igupto.

< Oseas 7 >