< Génesis 24 >
1 Abraham era anciano, entrado en días, y Yavé lo había bendecido en todo.
Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita.
2 Y Abraham dijo al esclavo más antiguo de su casa, el cual administraba todo lo que aquél tenía: Coloca ahora tu mano debajo de mi muslo
Tsiku lina Abrahamu anawuza wantchito wake wamkulu amene ankayangʼanira zonse anali nazo, kuti “Ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.
3 y jurarás por Yavé, ʼElohim de los cielos y de la tierra, que no tomarás para mi hijo esposa de las hijas de los cananeos en medio de los cuales yo vivo,
Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Yehova, Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamupezera mwana wanga mkazi pakati pa atsikana Achikanaani a kuno kumene ndikukhala,
4 sino que irás a mi tierra y a mi parentela y tomarás esposa para mi hijo Isaac.
koma kuti udzapita ku dziko la kwathu ndi kukamupezera mkazi mwana wanga Isake pakati pa abale anga.”
5 Y el esclavo le respondió: Quizás la mujer no consienta en venir conmigo a esta tierra. ¿Llevaré a tu hijo a la tierra de donde saliste?
Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?”
6 Entonces Abraham le contestó: Guárdate de no llevar a mi hijo allá.
Abrahamu anati, “Uwonetsetse kuti usadzabwerere naye mwana wanga kumeneko.
7 Yavé, el ʼElohim del cielo, Quien me tomó de la casa de mi padre y de la tierra de mi parentela, y Quien me habló y me juró: A tu descendencia daré esta tierra, Él mismo enviará su Ángel delante de ti y de allá tomarás esposa para mi hijo.
Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi.
8 Si la mujer no consiente en venir contigo, entonces quedarás desligado de mi juramento, pero no hagas que mi hijo vaya allá.
Ngati mkaziyo adzakana kubwerera nawe ndiye kuti udzakhala womasuka ku lumbiro langa. Koma usadzamutenge mwana wanga ndi kubwerera naye kumeneko.”
9 Entonces el esclavo puso su mano debajo del muslo de su ʼadón Abraham y le juró sobre este asunto.
Choncho wantchitoyo anayika dzanja lake pansi pa ntchafu ya mbuye wake Abrahamu nalumbira kwa iye kuti adzachitadi monga mwa mawu a Abrahamu.
10 El esclavo tomó diez de los camellos de su ʼadón, y salió con una variedad de cosas buenas de su ʼadón en su mano. Se levantó y fue a Mesopotamia, a la ciudad de Nacor.
Tsono wantchito uja anatengapo ngamira khumi mwa ngamira za mbuye wake pamodzi ndi zinthu zabwino za mitundumitundu. Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda wa Nahori, mʼdziko la Mesopotamiya.
11 En las afueras de la ciudad hizo arrodillar los camellos junto a un pozo de agua al tiempo de llegar la tarde, en el momento cuando salen las jóvenes a sacar agua.
Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.
12 Y dijo: ¡Yavé, ʼElohim de mi ʼadón Abraham, haz que hoy me suceda, te ruego, haz misericordia a mi ʼadón Abraham!
Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika.
13 Aquí estoy yo junto a una fuente de agua y las hijas de los habitantes de la ciudad salen a sacar agua.
Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi.
14 Sea que la joven a quien yo diga: Baja tu cántaro, te ruego, para que yo beba, y ella responda: Bebe, y también abrevaré tus camellos, ésa sea la que designaste para tu esclavo Isaac. Y por esto sabré que hiciste misericordia con mi ʼadón.
Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.
15 Aconteció que antes que él acabara de hablar, ahí llegaba Rebeca, la cual le nació a Betuel, hijo de Milca, esposa de Nacor, hermano de Abraham, llegaba con su cántaro al hombro.
Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu.
16 La muchacha era de apariencia muy hermosa, virgen, a la que ningún varón se unió. Y al bajar a la fuente, llenó su cántaro y salió.
Mtsikanayo anali wokongola kwambiri, namwali amene sanadziwe mwamuna. Iye anatsikira ku chitsime nadzaza mtsuko nakweranso ku mtunda.
17 Entonces el esclavo corrió a su encuentro y le dijo: Te ruego que me des a beber un poco de agua de tu cántaro.
Wantchito uja anathamanga kukakumana naye nati, “Chonde patseko madzi pangʼono a mu mtsuko wakowo kuti ndimwe.”
18 Ella respondió: Bebe, mi ʼadón. Y se apresuró a bajar el cántaro sobre su mano y le dio de beber.
Mtsikanayo anati, “Imwani mbuye wanga.” Ndipo mofulumira anatsitsa mtsuko uja nawuyika mʼmanja ndi kumupatsa kuti amwe.
19 Cuando acabó de darle de beber dijo: También sacaré agua para tus camellos hasta que acaben de beber.
Atatha kupereka madzi akumwa kwa mlendo uja, mtsikanayo anati, “Ndikatungiranso ngamira madzi kuti zimwe mpaka zitakwana.”
20 Se apresuró y vació su cántaro en el abrevadero. Corrió otra vez al pozo para sacar agua y sacó para todos sus camellos.
Choncho anafulumira kukhuthula madzi a mu mtsuko aja momwera ziweto, nathamanga kubwerera ku chitsime kukatunga madzi ena, ndipo anatunga okwanira ngamira zake zonse.
21 El hombre, con la vista fija en ella, callaba para saber si Yavé había prosperado o no su camino.
Modekha, munthu uja anayangʼanitsitsa kwambiri mtsikana uja kuti adziwedi ngati Yehova anamutsogolera pa ulendo wake uja kapena ayi.
22 Aconteció que cuando los camellos acabaron de beber, el hombre le dio un pendiente de oro que pesaba 5,5 gramos, y dos brazaletes de oro que pesaban 110 gramos.
Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100.
23 Y le preguntó: ¿De quién eres hija? Dime te ruego: ¿Hay lugar en casa de tu padre para que nosotros pasemos la noche?
Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?”
24 Ella le respondió: Yo soy hija de Betuel, el hijo que Milca dio a luz a Nacor.
Anamuyankha kuti, “Ine ndine mwana wa Betueli, mwana amene Milika anaberekera Nahori.”
25 Y añadió: También hay en nuestra casa pasto, mucho forraje y lugar para pasar la noche.
Ndipo anapitiriza kunena kuti, “Chakudya chodyetsa nyamazi chilipo kwathu ndipo malo woti mugone aliponso.”
26 Entonces el hombre hizo reverencia, se postró ante Yavé
Kenaka munthuyo anawerama pansi napembedza Yehova,
27 y dijo: Bendito sea Yavé, ʼElohim de mi ʼadón Abraham, que no apartó su misericordia y su fidelidad hacia mi ʼadón, y cuando yo tomé camino, me condujo Yavé a casa de los hermanos de mi ʼadón.
nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.”
28 Entonces la muchacha corrió y contó estas cosas en casa de su madre.
Mtsikana uja anathamanga nakafotokozera zimenezi anthu a kwa amayi ake.
29 Rebeca tenía un hermano llamado Labán, el cual corrió hacia el que estaba fuera, junto a la fuente.
Tsono Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani.
30 Cuando Labán vio el [pendiente] y los brazaletes en las muñecas de su hermana y oyó las palabras de su hermana Rebeca, quien decía: Este hombre me habló así, él corrió hacia el hombre, quien, por cierto, permanecía con los camellos junto a la fuente.
Iyeyu atangoona chipini pa mphuno ndi zibangiri pa mikono ya mlongo wake komanso kumva zimene mlendo uja ananena kwa Rebekayo, anathamangira kwa mlendo uja, ndipo anamupeza atangoyima ndi ngamira zake pafupi ndi chitsime.
31 [Labán] le dijo: Entra, bendito de Yavé. ¿Por qué te quedas afuera? Pues yo preparé la casa y lugar para los camellos.
Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.”
32 Entonces el hombre entró en la casa, y Labán le desató los camellos y les dio pasto y forraje. También le dio agua para lavar sus pies y los pies de los hombres que estaban con él.
Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse.
33 También le sirvió comida, pero el esclavo dijo: No comeré hasta cuando diga mis palabras. Y [Labán] le dijo: ¡Habla!
Chakudya chitabwera mlendo uja anati, “Sindidya mpaka nditakuwuzani zimene ndadzera kuno.” Labani anati, “Yankhulani.”
34 Contestó: Yo soy esclavo de Abraham.
Motero iye anati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu.
35 Yavé ha bendecido mucho a mi ʼadón, y se engrandeció, pues le dio ovejas y ganado vacuno, plata y oro, esclavos y esclavas, y camellos y asnos.
Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu.
36 Sara, esposa de mi ʼadón, dio a luz un hijo en su vejez a mi ʼadón, quien le dio todo lo que posee.
Sara, mkazi wa mbuye wanga anamubalira iye mwana wamwamuna ngakhale kuti Sarayo anali wokalamba. Tsono mbuye wanga wamupatsa mwanayo chuma chonse.
37 Y mi ʼadón me juramentó: No tomarás para mi hijo esposa de las hijas del cananeo en cuya tierra yo vivo,
Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, ‘Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani,
38 sino irás a casa de mi padre y a mi familia, y tomarás esposa para mi hijo.
koma upite ku banja la abambo anga ndi kwa abale anga kuti ukamupezere mkazi mwana wanga.’”
39 Yo dije a mi ʼadón: Quizás la mujer no quiera venir conmigo.
“Ndipo ine ndinati kwa mbuye wanga, ‘Nanga mkaziyo akakapanda kubwera nane pamodzi?’
40 Me contestó: Yavé, en cuya presencia he andado, enviará a su Ángel contigo, prosperará tu camino y podrás tomar esposa para mi hijo de entre mi familia y de la casa de mi padre.
“Iye anayankha, ‘Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa.
41 Entonces, cuando llegues a mi familia, quedarás desligado de mi juramento. Así que, si no quieren dártela, quedarás libre de mi juramento.
Ukadzachita zimenezi udzakhala mfulu wosamangidwa ndi lumbiro langali. Koma tsono ukadzafika kwa fuko langa, ndipo ngati sadzalola kukupatsa mbeta ya mwana wanga, aponso udzamasuka ku lumbiro langali.’”
42 Así, pues, llegué hoy a la fuente y dije: Yavé, ʼElohim de mi ʼadón Abraham, te ruego que hagas prosperar mi camino en el cual ando.
“Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu,
43 Aquí estoy junto a la fuente del agua. Sea, pues, que la joven que salga a sacar agua, a quien yo le diga: Te ruego que me des de beber un poco de agua de tu cántaro
taonani ndayima pambali pa chitsime ichi; ndipo ndidzati kwa namwali amene atabwere kudzatunga kuti, chonde nditamwako madzi a mu mtsuko wakowu,’
44 y me conteste: Bebe tú mismo, y también sacaré para tus camellos, sea ésta la esposa que Yavé destinó para el hijo de mi ʼadón.
ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.”
45 Antes que yo acabara de hablar en mi corazón, ahí estaba Rebeca con su cántaro al hombro quien bajaba a la fuente. Cuando sacó agua le dije: Te ruego que me des de beber.
“Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’
46 Y se apresuró, bajó su cántaro de encima de ella y respondió: Bebe, y también abrevaré tus camellos. Y bebí, y ella abrevó los camellos.
“Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, ‘Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo.
47 Le pregunté: ¿De quién eres hija? Y respondió: Soy hija de Betuel, el hijo que Milca le dio a luz a Nacor. Entonces le puse el pendiente en la nariz y los brazaletes en sus manos.
“Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake,
48 E hice reverencia, me postré ante Yavé. Bendije a Yavé, ʼElohim de mi ʼadón Abraham, Quien me condujo por camino recto a fin de tomar a la hija del hermano de mi ʼadón para su hijo.
kenaka ndinawerama pansi ndi kupembedza Yehova. Ndipo ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene anandilondolera mokhulupirika njira yanga. Iye wandifikitsa kwa mʼbale wake kumene ndapezera mbeta mwana wa mbuye wanga.
49 Ahora, pues, si ustedes hacen misericordia y verdad con mi ʼadón, declárenmelo. Y si no, declárenmelo también, y me encaminaré a la derecha o a la izquierda.
Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.”
50 Y al responder Labán y Betuel, dijeron: De parte de Yavé salió esto. No podemos decirte algo malo o bueno.
Labani ndi Betueli anayankha nati, “Izi ndi zochokera kwa Yehova, ndipo ife sitinganenepo kanthu.
51 Ahí está Rebeca delante de ti. Tómala y vete, y sea la esposa del hijo de tu ʼadón, como lo dijo Yavé.
Nayu Rebeka, mutengeni muzipita naye kuti akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu, monga Yehova wanenera.”
52 Cuando el esclavo de Abraham oyó sus palabras, se postró en tierra delante de Yavé.
Wantchito wa Abrahamu uja atamva zimene anawerama pansi pamaso pa Yehova.
53 Después el esclavo sacó alhajas de plata, objetos de oro y ropa, y se los dio a Rebeca. También dio valiosos regalos a su hermano y a su madre.
Kenaka wantchitoyo anatulutsa ziwiya zagolide ndi zasiliva ndi zovala nazipereka kwa Rebeka. Anaperekanso mphatso zina za mtengowapatali kwa mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka.
54 Después comieron y bebieron, él y los que lo acompañaban, y pasaron la noche. Al levantarse de mañana, dijo: Envíenme a mi ʼadón.
Tsono wantchito uja ndi anthu amene anali naye anadya, kumwa nagona komweko. Kutacha mmawa wake, wantchito uja anati, “Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”
55 Entonces el hermano de ella y su madre respondieron: Permanezca la doncella con nosotros algunos días, por lo menos diez, y después se irá.
Koma mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka anayankha kuti, “Muloleni mtsikanayu abakhala nafe masiku khumi kapena kupyolerapo, kenaka mukhoza kupita.”
56 Pero él les dijo: No me retrasen ya que Yavé hizo prosperar mi camino. Despáchenme para que me vaya a mi ʼadón.
Koma iye anawawuza kuti, “Chonde musandichedwetse. Yehova wandithandiza kale pa ulendo wanga. Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”
57 Y ellos contestaron: Llamemos a la joven y preguntémosle cuál es su deseo.
Koma iwo anati, “Bwanji timuyitane mtsikanayo ndipo timufunse ngati afuna kupita nanu panopa.”
58 Llamaron a Rebeca y le dijeron: ¿Irás tú con este varón? Y ella respondió: Iré.
Choncho iwo anamuyitana Rebeka uja namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita ndi munthuyu panopa?” Iye anayankha kuti, “Ndipita.”
59 Entonces despidieron a su hermana Rebeca, a su madre de crianza, al esclavo de Abraham y a sus hombres.
Kotero anamulola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu pamodzi ndi anthu amene anali naye.
60 Bendijeron a Rebeca y le dijeron: ¡Hermana nuestra, sé madre de miles de millares y que tus descendientes posean la puerta de sus enemigos!
Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti, “Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale mayi wa anthu miyandamiyanda; ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo.”
61 Rebeca se levantó con sus doncellas, montaron sobre los camellos y siguieron al hombre. Y el esclavo tomó a Rebeca y salió.
Kenaka Rebeka ndi antchito ake ananyamuka kukakwera ngamira zawo ndipo anapita naye pamodzi munthu uja. Choncho wantchito uja anatenga Rebeka nʼkumapita.
62 Mientras tanto, Isaac regresaba del pozo del Viviente-que-me-ve, pues él habitaba en la región del Neguev.
Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi.
63 Isaac había salido a meditar al campo al llegar la tarde. Cuando levantó sus ojos, miró y ahí llegaban unos camellos.
Tsiku lina chakumadzulo, Isake anatuluka kukayendayenda ku munda, ndipo atakweza maso anaona ngamira zikubwera.
64 Rebeca también levantó sus ojos, y cuando vio a Isaac, desmontó del camello,
Rebeka nayenso anatukula maso naona Isake. Ndipo anatsika pa ngamira yake
65 porque había preguntado al esclavo: ¿Quién es ese varón que viene por el campo a nuestro encuentro? El esclavo respondió: Es mi ʼadón. Entonces ella tomó el velo y se cubrió.
nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?” Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.
66 El esclavo le contó a Isaac todas las cosas que hizo.
Tsono wantchito uja anawuza Isake zonse zimene anazichita.
67 Isaac la introdujo en la tienda de su madre Sara, tomó a Rebeca como esposa y la amó. E Isaac se consoló después de [la muerte de] su madre.
Isake analowa naye Rebeka mu tenti ya amayi ake Sara, ndipo anakhala mkazi wake. Isake anamukonda kwambiri Rebeka mkazi wake motero kuti zimenezi zinamutonthoza imfa ya amayi ake.