< Ezequiel 26 >

1 El año 11, el día primero del mes, aconteció que la Palabra de Yavé vino a mí:
Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti:
2 Hijo de hombre, por cuanto Tiro dijo con respecto a Jerusalén: ¡Qué bueno! ¡La puerta de los pueblos está quebrada! ¡Se me abrió! Yo seré llena y ella quedará desolada.
“Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’
3 ʼAdonay Yavé dice: ¡Aquí estoy contra ti, oh Tiro! Como el mar levanta sus olas, Yo levanto contra ti muchas naciones.
Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja.
4 Destruirán los muros de Tiro. Derribarán sus torres, barreré de ella hasta su polvo. La dejaré como una roca lisa.
Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala.
5 Será tendedero de redes en medio del mar, porque Yo hablé, dice ʼAdonay Yavé. Será despojo para las naciones.
Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina.
6 Sus hijas que están en el campo morirán a espada. Y sabrán que Yo soy Yavé.
Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Porque ʼAdonay Yavé dice: Ciertamente traigo del norte contra Tiro a Nabucodonosor, rey de Babilonia, rey de reyes, con caballos, carruajes, caballería y una multitud de guerreros.
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo.
8 Matará a espada a tus hijas en el campo. Armará contra ti torres de asedio. Levantará contra ti empalizadas de defensa, y alzará su escudo contra ti.
Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe.
9 Lanzará contra tus muros vigas largas y pesadas muy reforzadas. Con hachas destruirá tus torres.
Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake.
10 A causa de numerosos caballos te cubrirá el polvo de ellos. Con el estruendo de su caballería y de las ruedas de sus carruajes, tus muros temblarán cuando entre por tus puertas como se entra por portillos en una ciudad destruida.
Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa.
11 Pisoteará todas tus calles con los cascos de sus caballos. Matará a filo de espada tu pueblo. Tus fuertes columnas caerán a tierra.
Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa.
12 Tomarán tus riquezas como despojo, saquearán tus mercaderías, destruirán tus muros y demolerán tus casas lujosas. Tus piedras, tu madera y tus escombros los lanzarán a las aguas.
Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja.
13 Silenciaré el sonido de tus canciones. No se oirá más el sonido de tus arpas.
Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso.
14 Te dejaré como una roca lisa y serás tendedero de redes. Nunca más serás edificada, porque Yo Yavé hablé, dice ʼAdonay Yavé.
Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.
15 ʼAdonay Yavé dice a Tiro: ¿No se estremecerán las costas ante el estruendo de tu caída, con el gemido de tus heridos y la matanza que ocurra en ti?
“Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako.
16 Todos los oficiales marinos bajarán de sus asientos y se despojarán sus mantos. Se quitarán sus ropas bordadas y se vestirán de terror. Se estremecerán consternados al sentarse en el suelo, asombrados a causa de ti.
Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera.
17 Levantarán una lamentación sobre ti: ¡Cómo pereciste, oh ciudad poblada por gente del mar! Ella con sus habitantes infundían terror en todos los que la rodeaban.
Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe: “‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka, wodzaza ndi anthu a ku nyanja! Unali wamphamvu pa nyanja, iwe ndi nzika zako; unkaopseza anthu onse amene ankakhala kumeneko.
18 Ahora, las costas tiemblan por el día de tu caída. Las costas marinas se aterran al ver tu fin.
Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera chifukwa cha kugwa kwako; okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu chifukwa cha kugwa kwako.’
19 Porque ʼAdonay Yavé dice: Cuando Yo te convierta en ciudad asolada, como las ciudades que no son habitadas, lanzaré el océano sobre ti. Las muchas aguas te cubrirán.
“Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize.
20 Te hundiré con los que descienden al sepulcro para que nunca más seas poblada, y daré gloria en la tierra de los vivientes.
Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo.
21 Te convertiré en terror y dejarás de ser. Serás buscada. Nunca más serás hallada, dice ʼAdonay Yavé.
Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”

< Ezequiel 26 >