< 2 Reyes 8 >

1 Eliseo habló a aquella mujer, cuyo hijo resucitó, y le dijo: Levántate y vete, tú y tu casa, y vive donde puedas. Porque Yavé llamó al hambre, la cual vendrá también sobre esta tierra por siete años.
Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.”
2 La mujer se levantó e hizo conforme a la palabra del varón de ʼElohim. Se fue con los de su casa, y vivió como extranjera en tierra de los filisteos durante siete años.
Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
3 Sucedió al terminar los siete años que la mujer volvió de la tierra de los filisteos, y salió para implorar al rey que le entregara su casa y su tierra.
Zitatha zaka zisanu ndi ziwirizo anabwera kuchokera ku dziko la Afilisti ndipo anapita kwa mfumu kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake.
4 El rey habló a Giezi, esclavo del varón de ʼElohim: Cuéntame ahora todos los prodigios que Eliseo hizo.
Ndipo mfumu inkayankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu kuti, “Tandiwuza zinthu zikuluzikulu zimene Elisa wachita.”
5 Sucedió que, mientras él contaba al rey cómo resucitó al muerto, llegó allí la mujer cuyo hijo resucitó, a implorar al rey que le devolviera su casa y su tierra. Entonces dijo Giezi: Rey, ʼadón mío, ésta es la mujer y este es su hijo, al cual Eliseo dio vida.
Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.”
6 Entonces el rey preguntó a la mujer, y ella le contó. Así que el rey le asignó un funcionario, y le dijo: Restituye todo lo que era de ella, y todo el producto del campo desde el día cuando salió del país hasta ahora.
Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo. Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.”
7 Eliseo fue a Damasco. Ben-adad, rey de Siria, estaba enfermo y le dijeron: El varón de ʼElohim vino aquí.
Elisa anapita ku Damasiko, ndipo Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu ankadwala. Mfumuyo itawuzidwa kuti, “Munthu wa Mulungu wabwera kuno kuchokera kutali,”
8 Y el rey dijo a Hazael: Toma en tu mano un presente, y vé a encontrar al varón de ʼElohim. Consulta a Yavé por medio de él y pregunta: ¿Sanaré de esta enfermedad?
inawuza Hazaeli kuti, “Tenga mphatso ndipo pita ukakumane ndi munthu wa Mulungu. Ukandifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’”
9 Hazael fue a encontrarse con él y llevó consigo un presente de lo mejor de Damasco: una carga de 40 camellos. Se detuvo ante él y le dijo: Tu hijo Ben-adad, rey de Siria, me envía a ti para preguntar: ¿Sanaré de esta enfermedad?
Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’”
10 Eliseo le respondió: Vé y dile: Ciertamente te recuperarás, pero Yavé me mostró que realmente morirás.
Elisa anayankha kuti, “Pita ndipo ukamuwuze kuti, ‘Udzachira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa kuti adzafabe.”
11 El varón de ʼElohim lo miró fijamente hasta que aquél se ruborizó. Entonces el varón de ʼElohim lloró.
Elisa anamuyangʼana kwambiri Hazaeli mpaka anachita manyazi. Pamenepo munthu wa Mulungu anayamba kulira.
12 Y Hazael preguntó: ¿Por qué llora mi ʼadon? Y él contestó: Porque sé el mal que harás a los hijos de Israel: pondrás fuego a sus fortalezas, matarás a espada a sus jóvenes, estrellarás a sus niños y abrirás el vientre a sus mujeres embarazadas.
Hazaeli anafunsa kuti, “Mbuye wanga mukulira chifukwa chiyani?” Elisa anayankha kuti, “Chifukwa ndikudziwa choyipa chimene udzachitira Aisraeli. Udzatentha mizinda yawo ya chitetezo, udzapha anyamata awo ndi lupanga, udzaphwanyitsa pansi makanda awo ndiponso udzatumbula mimba za akazi awo oyembekezera.”
13 Hazael preguntó: ¿Qué es tu esclavo, sino un perro, para que haga cosas tan grandes? Y Eliseo respondió: Yavé me mostró que tú serás rey de Siria.
Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?” Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”
14 [Hazael] se alejó de Eliseo y fue a su ʼadón, quien le preguntó: ¿Qué te dijo Eliseo? Y él dijo: Me dijo que ciertamente te recuperarás.
Choncho Hazaeli anasiyana ndi Elisa ndi kubwerera kwa mbuye wake. Beni-Hadadi atafunsa kuti, “Elisa wakuwuza chiyani?” Hazaeli anayankha kuti, “Elisa wandiwuza kuti inu mudzachira ndithu.”
15 Sucedió al día siguiente que [Ben-adad] tomó un paño grueso, lo empapó en agua, lo extendió sobre su cara y murió. Y Hazael reinó en su lugar.
Koma mmawa mwake Hazaeli anatenga nsalu yokhuthala ndi kuyiviyika mʼmadzi ndipo anaphimba nayo nkhope ya mfumu, kotero mfumuyo inafa. Hazaeli analowa ufumu mʼmalo mwake.
16 El año quinto de Joram, hijo de Acab, rey de Israel cuando Josafat era rey de Judá, comenzó a reinar Joram, hijo de Josafat, rey de Judá.
Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israeli, Yehosafati ali mfumu ya ku Yuda, Yehoramu mwana wake anakhala mfumu ya Ayuda.
17 Tenía 32 años cuando comenzó a reinar, y reinó ocho años en Jerusalén.
Yehoramu analowa ufumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.
18 Anduvo en el camino de los reyes de Israel, como la casa de Acab, pues su esposa fue una hija de Acab, e hizo lo malo ante Yavé.
Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
19 Pero Yavé no quiso destruir a Judá a causa de su esclavo David, pues prometió darle a él y a sus hijos una lámpara para siempre.
Komabe, chifukwa cha mtumiki wake Davide, Yehova sanafune kuwononga Yuda popeza Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa nyale pamodzi ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
20 En sus días Edom se rebeló contra el dominio de Judá y decidieron que un rey reinara sobre ellos.
Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira ulamuliro wa Yuda ndipo anadzisankhira mfumu.
21 Entonces Joram, [hijo de Josafat, ] fue a Zaír con todos los carruajes. Se levantó de noche y atacó a los de Edom, quienes lo rodearon junto con los jefes de los carruajes. La tropa huyó a sus tiendas.
Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndipo iye anakantha Aedomu amene anamuzungulira pamodzi ndi oyendetsa magaleta ake usiku. Koma ankhondo ake anathawa napita ku misasa yawo.
22 Pero Edom siguió en rebelión contra el dominio de Judá hasta hoy. En aquel tiempo también se rebeló Libna.
Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira Yuda. Nthawi yomweyo mzinda wa Libina unawukiranso.
23 Los demás hechos y cosas de Joram, ¿no están escritos en el rollo de las Crónicas de los reyes de Judá?
Ndipo ntchito zina za Yehoramu ndi zonse zomwe anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
24 Joram descansó con sus antepasados y fue sepultado con sus antepasados en la Ciudad de David. Su hijo Ocozías reinó en su lugar.
Choncho Yehoramu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
25 El año 12 de Joram, hijo de Acab, rey de Israel, comenzó a reinar Ocozías, hijo de Joram, rey de Judá.
Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
26 Ocozías tenía 22 años cuando comenzó a reinar, y reinó un año en Jerusalén. El nombre de su madre fue Atalía, hija de Omri, rey de Israel.
Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake anali Ataliya, chidzukulu cha Omiri mfumu ya Israeli.
27 Anduvo en el camino de la casa de Acab e hizo lo malo ante Yavé como la casa de Acab, porque era su yerno.
Iye anatsatira makhalidwe a banja la Ahabu ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga linachitira banja la Ahabu, pakuti anali mkamwini wa banja la Ahabu.
28 Ocozías fue a la guerra con el rey Joram, hijo de Acab, contra Hazael, rey de Siria, en Ramot de Galaad, pero los sirios derrotaron a Joram.
Ahaziya anapita pamodzi ndi Yoramu mwana wa Ahabu kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yoramu.
29 El rey Joram regresó a Jezreel para ser curado de las heridas que los sirios le infligieron cuando combatía contra Hazael, rey de Siria, en Ramá. Entonces Ocozías, hijo de Joram, rey de Judá, bajó a Jezreel para ver a Joram, hijo de Acab, porque éste estaba enfermo.
Choncho mfumu Yoramu inabwerera ku Yezireeli kuti ikachire mabala ake amene Aaramu anamuvulaza ku Rama pa nkhondo yake ndi Hazaeli mfumu ya Aramu. Tsono Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda anapita ku Yezireeli kuti akamuone Yoramu mwana wa Ahabu, popeza nʼkuti akudwala.

< 2 Reyes 8 >