< 1 Reyes 10 >
1 Cuando la reina de Sabá oyó la fama de Salomón, que se debió al Nombre de Yavé, vino para probarlo con preguntas difíciles.
Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima.
2 Llegó a Jerusalén con un gran séquito, camellos cargados de especias aromáticas, oro en gran abundancia y piedras preciosas. Cuando llegó a Salomón, habló con él de todo lo que tenía en su corazón.
Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.
3 Salomón respondió todas sus preguntas, y no hubo cosa difícil que el rey no le pudiera responder.
Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo.
4 La reina de Sabá, al escuchar toda la sabiduría de Salomón y ver el palacio que edificó,
Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga,
5 los manjares de su mesa, los asientos de sus esclavos, la presentación y las ropas de sus esclavos y coperos, y los holocaustos que él ofrecía en la Casa de Yavé, quedó sin aliento,
chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.
6 y dijo al rey: ¡Es verdad lo que oí en mi tierra acerca de tus hechos y de tu sabiduría!
Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona.
7 No creía lo que me decían hasta que vine y mis ojos lo ven. Ciertamente no se me dijo ni aun la mitad. Tú superas en sabiduría y bienes lo que oí de tu fama.
Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva.
8 ¡Dichosos tus hombres, dichosos estos esclavos tuyos que están de continuo delante te ti y oyen tu sabiduría!
Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu!
9 ¡Bendito sea Yavé tu ʼElohim, Quien se agradó de ti para establecerte en el trono de Israel! Por causa del eterno amor que Yavé tiene a Israel, te constituyó rey para que practiques la equidad y la justicia.
Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
10 Ella [le] dio al rey cuatro toneladas de oro, gran cantidad de especias aromáticas y piedras preciosas. Nunca más llegó tanta abundancia de especias aromáticas como las que la reina de Sabá llevó al rey Salomón.
Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni.
11 También la flota de Hiram llevaba oro de Ofir y transportaba gran cantidad de madera de sándalo y piedras preciosas de Ofir.
(Ndiponso sitima zapamadzi za Hiramu zinabweretsa golide wochokera ku Ofiri. Ndipo kuchokera kumeneko kunabweranso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yokongola.
12 El rey hizo columnas con la madera de sándalo para la Casa de Yavé, la casa real y arpas y liras para los músicos. Tal clase de madera de sándalo no ha entrado [más], ni se ha vuelto a ver hasta hoy.
Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).
13 El rey Salomón dio a la reina de Sabá cuanto ella quiso pedirle, además de lo que Salomón le dio según su espléndida generosidad. Entonces ella se regresó a su tierra con sus esclavos.
Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.
14 El peso del oro que le llegaba a Salomón cada año era 22 toneladas,
Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000,
15 sin contar lo de los mercaderes, del negocio de especias, de todos los reyes de Arabia, ni lo de los gobernadores de la tierra.
osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo.
16 El rey Salomón hizo 200 escudos grandes de oro martillado de 6,6 kilogramos en cada escudo.
Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka.
17 Hizo además 300 escudos de oro martillado de 1,65 kilogramos de oro en cada escudo, los cuales el rey colocó en la casa del bosque del Líbano.
Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni.
18 También el rey hizo un gran trono de marfil y lo recubrió de oro refinado.
Mfumu inapangitsanso mpando waufumu waukulu wa minyanga ya njovu, ndipo inawukutira ndi golide wabwino kwambiri.
19 El trono tenía seis gradas y el respaldo tenía una cabeza de becerro. A ambos lados del asiento tenía soportes para los brazos, y junto a los brazos había dos leones en pie.
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse.
20 Había igualmente 12 leones en pie, uno a cada lado de las seis gradas. Jamás se hizo algo semejante para algún reino.
Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi limodziwo; mkango umodzi mbali iliyonse ya makwererowa. Mpando woterewu sunapangidwepo mu ufumu wina uliwonse.
21 Todos los vasos para beber el rey Salomón eran de oro. Toda la vajilla de la casa del bosque del Líbano eran de oro puro. Nada era de plata, pues en los días de Salomón ésta no era estimada en absoluto,
Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni.
22 porque el rey tenía la flota de Tarsis con la flota de Hiram en el mar. Una vez cada tres años llegaba la flota de Tarsis con oro, plata, marfil, monos y pavos reales.
Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi.
23 El rey Salomón fue más grande que todos los reyes de la tierra en riquezas y en sabiduría.
Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi.
24 Toda la tierra procuraba estar en presencia de Salomón para oír la sabiduría que ʼElohim puso en su corazón.
Anthu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuyankhulana ndi Solomoni kuti amve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake.
25 Cada año, todos ellos le llevaban su presente: objetos de plata y de oro, ropas, armas, perfumes, caballos y mulas.
Chaka ndi chaka aliyense amene amabwera ankabweretsa mphatso za siliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya, akavalo ndi abulu.
26 Salomón también acumuló carruajes de guerra y jinetes. Tuvo 1.400 carruajes y 12.000 jinetes, los cuales situó en las ciudades de los carruajes y en Jerusalén, cerca del rey.
Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu.
27 El rey logró que la plata en Jerusalén fuera tan común como las piedras y que el cedro fuera tan abundante como los sicómoros de la Sefela.
Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri.
28 Los caballos de Salomón procedían de Egipto y Coa. Los mercaderes del rey los adquirían en Coa al contado.
Akavalo a Solomoni ankachokera ku Igupto komanso ku Kuwe. Anthu a malonda a mfumu ankatengera akavalowo ku Kuwe.
29 Cada carruaje que entraba de Egipto costaba 6,6 kilogramos de plata, y cada caballo 1,65 kilogramos. Por medio de [los mercaderes del rey] todos los reyes de los heteos y los de Siria también los adquirían.
Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya.