< Jeremías 22 >

1 Yahvé dijo: “Baja a la casa del rey de Judá y di allí esta palabra:
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti,
2 ‘Escucha la palabra de Yahvé, rey de Judá, que se sienta en el trono de David: tú, tus siervos y tu pueblo que entran por estas puertas.
‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi.
3 Yahvé dice: “Ejecuta el derecho y la justicia, y libera al despojado de la mano del opresor. No hagas ningún mal. No hagas violencia al extranjero, al huérfano o a la viuda. No derrames sangre inocente en este lugar.
Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.
4 Porque si hacéis esto, los reyes que se sientan en el trono de David entrarán por las puertas de esta casa, montados en carros y en caballos: ellos, sus siervos y su pueblo.
Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo.
5 Pero si no escuchan estas palabras, juro por mí mismo — dice el Señor — que esta casa se convertirá en una desolación”.
Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’”
6 Porque Yahvé dice sobre la casa del rey de Judá: “Tú eres Gilead para mí, el jefe del Líbano. Sin embargo, ciertamente te convertiré en un desierto, ciudades que no están habitadas.
Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi: “Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine, ngati msonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, ngati mizinda yopanda anthu.
7 Prepararé destructores contra ti, todos con sus armas, y cortarán sus cedros preferidos, y los echó al fuego.
Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge, munthu aliyense ali ndi zida zake, ndipo adzadula mikungudza yako yokongola nadzayiponya pa moto.
8 “Muchas naciones pasarán por esta ciudad, y cada una de ellas preguntará a su vecino: “¿Por qué ha hecho esto Yahvé a esta gran ciudad?”
“Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’
9 Entonces responderán: “Porque abandonaron la alianza de Yahvé, su Dios, adoraron a otros dioses y les sirvieron.”
Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’”
10 No llores por los muertos. No lo lamentes; pero llora amargamente por el que se va, porque no volverá más, y no ver su país natal.
Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo; mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo, chifukwa sadzabwereranso kapena kuonanso dziko lake lobadwira.
11 Porque el Señor dice tocando a Salum, hijo de Josías, rey de Judá, que reinó en lugar de su padre Josías, y que salió de este lugar “No volverá más allí.
Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso.
12 Pero morirá en el lugar donde lo han llevado cautivo. No volverá a ver esta tierra”.
Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”
13 “Ay del que construye su casa con la injusticia, y sus habitaciones por la injusticia; que utiliza el servicio de su vecino sin cobrar, y no le da su alquiler;
“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake zosanja monyenga, pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata, osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
14 que dice: “Voy a construirme una casa amplia y habitaciones espaciosas”. y recorta las ventanas para sí mismo, con un techo de cedro, y pintado de rojo.
Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’ Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.
15 “¿Debes reinar porque te esfuerzas por sobresalir en el cedro? ¿Tu padre no comía y bebía? y hacer justicia y rectitud? Entonces le fue bien.
“Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri zingachititse iwe kukhala mfumu? Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa. Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera, ndipo zonse zinkawayendera bwino.
16 Juzgó la causa de los pobres y necesitados; así que entonces estaba bien. ¿No era esto para conocerme?” dice Yahvé.
Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?” akutero Yehova.
17 Pero tus ojos y tu corazón son sólo para tu codicia, por derramar sangre inocente, para la opresión, y para hacer violencia”.
“Koma maso ako ndi mtima sizili penanso, koma zili pa phindu lachinyengo, pa zopha anthu osalakwa ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”
18 Por lo tanto, Yahvé dice respecto a Joacim, hijo de Josías, rey de Judá “No se lamentarán por él, diciendo: “¡Ah, mi hermano!” o “¡Ah, hermana! No se lamentarán por él, diciendo “¡Ah señor!” o, “¡Ah su gloria!
Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti, “Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti, ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga! Anthu ake sadzamulira maliro kuti, Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
19 Será enterrado con la sepultura de un burro, arrastrados y expulsados más allá de las puertas de Jerusalén”.
Adzayikidwa ngati bulu, kuchita kumuguguza ndi kukamutaya kunja kwa zipata za Yerusalemu.”
20 “Sube al Líbano y grita. Alza tu voz en Basán, y claman desde Abarim; porque todos tus amantes han sido destruidos.
“Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko, mawu anu akamveke mpaka ku Basani. Mulire mofuwula muli ku Abarimu chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
21 Te hablé en tu prosperidad, pero tú dijiste: “No voy a escuchar”. Este ha sido tu camino desde tu juventud, que no obedeciste mi voz.
Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere. Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’ Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono. Simunandimvere Ine.
22 El viento alimentará a todos tus pastores, y tus amantes irán al cautiverio. Seguramente entonces te avergonzarás y confundido por toda tu maldad.
Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo. Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa chifukwa cha zoyipa zanu zonse.
23 Habitante del Líbano, que hace su nido en los cedros, que se compadecerá de ti cuando te lleguen los dolores, ¡el dolor como el de una mujer de parto!
Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni, amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza, mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani, zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!
24 “Vivo yo — dice el Señor — que aunque Conías, hijo de Joacim, rey de Judá, fuera el sello de mi mano derecha, te arrancaría de allí.
“Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya.
25 Te entregaría a la mano de los que buscan tu vida, y a la mano de los que te dan miedo, a la mano de Nabucodonosor, rey de Babilonia, y a la mano de los caldeos.
Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake.
26 Te echaré con tu madre que te dio a luz a otro país, donde no naciste, y allí morirás.
Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko.
27 Pero a la tierra a la que su alma anhela regresar, allí no volverán”.
Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”
28 ¿Es este hombre, Conías, un vaso roto y despreciado? ¿Es un recipiente en el que nadie se deleita? Por qué son expulsados, él y su descendencia, y arrojados a una tierra que no conocen?
Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka imene anthu sakuyifunanso? Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake, achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
29 Oh, tierra, tierra, tierra, ¡escuchen la palabra de Yahvé!
Iwe dziko, dziko, dziko, Imva mawu a Yehova!
30 Dice Yahvé, “Registra a este hombre como sin hijos, un hombre que no prosperará en sus días; porque ya no prosperará el hombre de su descendencia, sentado en el trono de David y gobernando en Judá”.
Yehova akuti, “Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino. Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide ndi kulamulira Yuda.”

< Jeremías 22 >