< Jeremías 14 >
1 Esta es la palabra de Yahvé que llegó a Jeremías en relación con la sequía:
Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:
2 “Judá está de luto, y sus puertas languidecen. Se sientan en negro en el suelo. El grito de Jerusalén se eleva.
“Yuda akulira, mizinda yake ikuvutika; anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni, kulira kwa Yerusalemu kwakula.
3 Sus nobles envían a sus pequeños a las aguas. Llegan a las cisternas, y no encontraremos agua. Vuelven con los vasos vacíos. Están decepcionados y confundidos, y cubrir sus cabezas.
Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi. Apita ku zitsime osapezako madzi. Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi. Amanyazi ndi othedwa nzeru adziphimba kumaso.
4 Por el suelo que se agrieta, porque no ha llovido en la tierra, los aradores están decepcionados. Se cubren la cabeza.
Popeza pansi pawumiratu chifukwa kulibe madzi, alimi ali ndi manyazi ndipo amphimba nkhope zawo.
5 Sí, también la cierva en el campo pare y abandone a sus crías, porque no hay hierba.
Ngakhale mbawala yayikazi ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo chifukwa kulibe msipu.
6 Los asnos salvajes se paran en las alturas desnudas. Jadean por aire como chacales. Sus ojos fallan, porque no hay vegetación.
Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe; maso awo achita chidima chifukwa chosowa msipu.”
7 Aunque nuestras iniquidades testifiquen contra nosotros, trabajar por tu nombre, Yahvé; porque nuestras rebeliones son muchas. Hemos pecado contra ti.
Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa, koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu. Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu; ife takuchimwirani.
8 Tú, esperanza de Israel, su salvador en el momento de la dificultad, por qué deberías estar como un extranjero en la tierra, y como un caminante que se aparta para pasar la noche?
Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso, chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno? Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
9 Por qué debes ser como un hombre asustado, como un hombre poderoso que no puede salvar? Sin embargo, tú, Yahvé, estás en medio de nosotros, y nos llamamos por tu nombre. No nos dejes.
Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa, kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa? Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu, ndipo tikudziwika ndi dzina lanu; musatitaye ife!”
10 Yahvé dice a este pueblo: “Aun así, les ha gustado vagar. No han frenado sus pies. Por lo tanto, Yahvé no los acepta. Ahora se acordará de su iniquidad, y castigarlos por sus pecados”.
Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi: “Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri; samatha kudziretsa. Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire, ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
11 El Señor me dijo: “No reces por este pueblo para su bien.
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.
12 Cuando ayunen, no escucharé su clamor; y cuando ofrezcan holocaustos y ofrendas, no los aceptaré, sino que los consumiré con la espada, el hambre y la peste.”
Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”
13 Entonces dije: “¡Ah, Señor Yahvé! He aquí que los profetas les dicen: ‘No veréis la espada, ni tendréis hambre, sino que os daré una paz segura en este lugar’”.
Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”
14 Entonces el Señor me dijo: “Los profetas profetizan mentiras en mi nombre. Yo no los envié. Yo no les ordené. Yo no les hablé. Te profetizan una visión mentirosa, una adivinación y una cosa de nada, y el engaño de su propio corazón.
Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo.
15 Por eso dice el Señor acerca de los profetas que profetizan en mi nombre, pero yo no los envié, y sin embargo dicen: ‘La espada y el hambre no estarán en esta tierra’. Esos profetas serán consumidos por la espada y el hambre.
Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala.
16 El pueblo al que profetizan será expulsado por las calles de Jerusalén a causa del hambre y de la espada. No tendrán quien los entierre, ni a ellos, ni a sus esposas, ni a sus hijos, ni a sus hijas, porque derramaré sobre ellos su maldad.
Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.
17 “Les dirás esta palabra: “‘Que mis ojos corran con lágrimas noche y día, y que no cesen; porque la hija virgen de mi pueblo está rota con una gran brecha, con una herida muy grave.
“Awuze mawu awa: “‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza usana ndi usiku; chifukwa anthu anga okondedwa apwetekeka kwambiri, akanthidwa kwambiri.
18 Si salgo al campo, ¡entonces he aquí, los muertos con la espada! Si entro en la ciudad, entonces, ¡mira a los que están enfermos de hambre! Porque tanto el profeta como el sacerdote van por la tierra, y no tienen conocimiento”.
Ndikapita kuthengo, ndikuona amene aphedwa ndi lupanga; ndikapita mu mzinda, ndikuona amene asakazidwa ndi njala. Ngakhale aneneri pamodzi ndi ansembe onse atengedwa.’”
19 ¿Has rechazado por completo a Judá? ¿Tu alma ha aborrecido a Sión? ¿Por qué nos has golpeado, y no hay curación para nosotros? Buscamos la paz, pero no llegó nada bueno; y por un tiempo de curación, y he aquí, ¡desconsuelo!
Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu? Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni? Chifukwa chiyani mwatikantha chotere kuti sitingathenso kuchira? Ife tinayembekezera mtendere koma palibe chabwino chomwe chabwera, tinayembekezera kuchira koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
20 Reconocemos, Yahvé, nuestra maldad, y la iniquidad de nuestros padres; porque hemos pecado contra ti.
Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu ndiponso kulakwa kwa makolo athu; ndithu ife tinakuchimwiranidi.
21 No nos aborrezcas, por tu nombre. No deshonres el trono de tu gloria. Recuerda, y no rompas tu pacto con nosotros.
Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe; musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero. Kumbukirani pangano lanu ndi ife ndipo musachiphwanye.
22 ¿Hay alguno entre las vanidades de las naciones que pueda hacer llover? ¿O el cielo puede dar duchas? ¿No eres tú, Yahvé, nuestro Dios? Por lo tanto, te esperaremos; porque tú has hecho todas estas cosas.
Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina, kodi pali mulungu amene angagwetse mvula? Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu, popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu amene mukhoza kuchita zimenezi.