< Génesis 46 >

1 Israel viajó con todo lo que tenía, llegó a Beerseba y ofreció sacrificios al Dios de su padre, Isaac.
Israeli anasonkhanitsa zonse anali nazo napita ku Beeriseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa abambo ake Isake.
2 Dios habló a Israel en las visiones de la noche, y dijo: “¡Jacob, Jacob!” Dijo: “Aquí estoy”.
Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!” Iye anayankha, “Ee, Ambuye.”
3 Dijo: “Yo soy Dios, el Dios de tu padre. No tengas miedo de bajar a Egipto, porque allí haré de ti una gran nación.
Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu.
4 Yo bajaré contigo a Egipto. También te haré subir con toda seguridad. La mano de José cerrará tus ojos”.
Ine ndidzapita ku Igupto pamodzi ndi iwe ndipo mosakayika konse zidzukulu zako ndidzazibweretsa konkuno. Yosefe adzakhalapo pa nthawi yako yomwalira.”
5 Jacob se levantó de Beerseba, y los hijos de Israel llevaron a Jacob, a su padre, a sus hijos y a sus mujeres, en los carros que el faraón había enviado para transportarlo.
Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo.
6 Tomaron su ganado y sus bienes, que habían adquirido en la tierra de Canaán, y entraron en Egipto: Jacob, y toda su descendencia con él,
Iwo anatenganso ziweto zawo ndi katundu wawo amene anali naye ku Kanaani, ndipo Yakobo pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake anapita ku Igupto.
7 sus hijos, y los hijos de sus hijos con él, sus hijas y las hijas de sus hijos, y llevó toda su descendencia con él a Egipto.
Ndiye kuti popita ku Igupto Yakobo anatenga ana aamuna, zidzukulu zazimuna, ana aakazi ndi zidzukulu zazikazi.
8 Estos son los nombres de los hijos de Israel que entraron en Egipto, Jacob y sus hijos: Rubén, primogénito de Jacob.
Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto: Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.
9 Los hijos de Rubén: Hanoc, Falu, Esrom y Carmi.
Ana aamuna a Rubeni ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.
10 Los hijos de Simeón: Jemuel, Jamín, Ohad, Jaquin, Zohar y Saul, hijo de una cananea.
Ana aamuna a Simeoni ndi awa: Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani.
11 Los hijos de Leví: Gersón, Coat y Merari.
Ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
12 Los hijos de Judá: Er, Onán, Sala, Fares y Zéraj; pero Er y Onán murieron en la tierra de Canaán. Los hijos de Fares fueron Esrom y Hamul.
Ana aamuna a Yuda ndi awa: Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani. Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.
13 Los hijos de Isacar: Tola, Puvah, Iob y Shimron.
Ana aamuna a Isakara ndi awa: Tola, Puwa, Yobi ndi Simironi.
14 Los hijos de Zabulón: Sered, Elón y Jahleel.
Ana aamuna a Zebuloni ndi awa: Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.
15 Estos son los hijos de Lea, que dio a luz a Jacob en Padan Aram, además de su hija Dina. Todas las almas de sus hijos e hijas fueron treinta y tres.
Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33.
16 Los hijos de Gad: Zifón, Haggi, Suni, Ezbón, Eri, Arodi y Areli.
Ana aamuna a Gadi ndi awa: Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.
17 Los hijos de Aser: Imna, Ishva, Ishvi, Beriá y su hermana Sera. Los hijos de Beriá: Heber y Malquiel.
Ana aamuna a Aseri ndi awa: Imuna, Isiva, Isivi, Beriya ndi Sera mlongo wawo. Ana aamuna a Beriya ndi awa: Heberi ndi Malikieli.
18 Estos son los hijos de Zilpá, que Labán dio a su hija Lea, y que ella dio a luz a Jacob, dieciséis almas.
Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16.
19 Los hijos de Raquel, mujer de Jacob José y Benjamín.
Ana aamuna a Rakele mkazi wa Yakobo anali: Yosefe ndi Benjamini.
20 A José le nacieron en la tierra de Egipto Manasés y Efraín, que le dio a luz Asenat, hija de Potifera, sacerdote de On.
Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.
21 Los hijos de Benjamín: Bela, Bequer, Asbel, Gera, Naamán, Ehi, Ros, Mupim, Hupim y Ard.
Ana aamuna a Benjamini ndi awa: Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi.
22 Estos son los hijos de Raquel que le nacieron a Jacob: todos fueron catorce.
Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa mkazi wake Rakele. Onse analipo khumi ndi anayi.
23 El hijo de Dan: Hushim.
Mwana wa mwamuna wa Dani anali: Husimu.
24 Los hijos de Neftalí: Jahzeel, Guni, Jezer y Silem.
Ana aamuna a Nafutali ndi awa: Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu.
25 Estos son los hijos de Bilhá, que Labán dio a su hija Raquel, y éstos fueron los que ella dio a luz a Jacob: todas las almas fueron siete.
Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Biliha amene Labani anapereka kwa mwana wake Rakele. Onse pamodzi analipo asanu ndi awiri.
26 Todas las almas que vinieron con Jacob a Egipto, que fueron su descendencia directa, además de las mujeres de los hijos de Jacob, todas las almas fueron sesenta y seis.
Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66.
27 Los hijos de José, que le nacieron en Egipto, fueron dos almas. Todas las almas de la casa de Jacob, que llegaron a Egipto, fueron setenta.
Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.
28 Jacob envió a Judá delante de José para que le mostrara el camino a Gosén, y llegaron a la tierra de Gosén.
Tsopano Yakobo anatumiza Yuda kwa Yosefe kukamupempha kuti akakumane naye ku Goseni. Iwo atafika ku chigawo cha Goseni,
29 José preparó su carro y subió a recibir a Israel, su padre, en Gosén. Se presentó ante él, y se echó sobre su cuello, y lloró sobre su cuello un buen rato.
Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.
30 Israel dijo a José: “Ahora déjame morir, ya que he visto tu rostro, que aún estás vivo”.
Israeli anati kwa Yosefe, “Tsopano ndikhoza kumwalira poti ndaona nkhope yako kuti ukanali ndi moyo.”
31 José dijo a sus hermanos y a la casa de su padre: “Subiré y hablaré con el Faraón y le diré: ‘Mis hermanos y la casa de mi padre, que estaban en la tierra de Canaán, han venido a mí.
Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, ‘Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine.
32 Estos hombres son pastores, pues han sido cuidadores de ganado, y han traído sus rebaños, sus manadas y todo lo que tienen.’
Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’
33 Sucederá que cuando el Faraón os llame y os diga: “¿A qué os dedicáis?
Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’
34 que diréis: ‘Tus siervos han sido cuidadores de ganado desde nuestra juventud hasta ahora, tanto nosotros como nuestros padres’, para que podáis habitar en la tierra de Gosén; porque todo pastor es una abominación para los egipcios.”
Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”

< Génesis 46 >