< Salmos 58 >
1 Para el director del coro. Según la melodía de “No destruir”. Un salmo (mictam) de David. Líderes, ¿hablan ustedes con rectitud? ¿Realmente juzgan a la gente de forma justa?
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama? Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?
2 No, porque en sus mentes planean el mal. ¡Causan violencia por todas partes!
Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama, ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.
3 Los malvados son pecadores desde el nacimiento; desde el momento en que son dados a luz dicen mentiras.
Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera; kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.
4 Tienen veneno como de una serpiente venenosa, y al igual que una cobra dejan de escuchar,
Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka, ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.
5 rehusándose a escuchar la voz de los encantadores y los hechiceros.
Imene simva liwu la munthu wamatsenga, ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.
6 Dios, rompe sus dientes, y quiebra los colmillos de estos leones, Señor.
Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu, Yehova khadzulani mano a mikango!
7 Que se desvanezcan como el agua que fluye lejos; que cuando disparan sus arcos pierdan su blanco.
Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.
8 Que sean como la baba de los caracoles que se disuelve, como un niño que no nació y nunca vio la luz del día.
Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda; ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.
9 Antes de que la olla de espinos ardientes se caliente, sea que estén frescos o secos, Dios los esparcirá.
Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku, kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.
10 Los que viven con rectitud se alegrarán cuando vean que hay un castigo; lavarán sus pies en la sangre de los malvados.
Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango, pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.
11 Dirán, “Definitivamente hay un premio para aquellos que viven haciendo el bien; ciertamente hay un Dios que juzga de forma justa sobre la tierra”.
Ndipo anthu adzanena kuti, “Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho; zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”