< Números 2 >

1 El Señor les dijo a Moisés y Aarón:
Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni:
2 “Los israelitas deben establecer su campamento alrededor del Tabernáculo de Reunión pero a cierta distancia de él. Cada miembro de cada tribu acampará bajo su propia bandera y estandarte familiar.
“Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.”
3 La tribu de Judá acampará bajo su bandera en el lado este. Su líder es Naasón, hijo de Aminadab,
Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu.
4 tiene 74.600 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.
5 La tribu de Isacar acampará junto a ellos. Su líder es Natanael, hijo de Zuar,
Fuko la Isakara lidzamanga pafupi ndi Yuda. Mtsogoleri wa gulu la Isakara ndi Netanieli mwana wa Zuwara.
6 y tiene 54.400 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 54,400.
7 La siguiente es la tribu de Zabulón. Su líder es Eliab, hijo de Helón,
Lotsatira lidzakhala fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa gulu la Zebuloni ndi Eliabu mwana wa Heloni.
8 y tiene 57.400 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400.
9 Así que el total de hombres en el territorio de Judá e de 186.400. Y cuando llegue la hora de marcharse, ellos irán a la cabeza.
Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka.
10 “La tribu de Rubén acampará bajo su bandera en el lado sur. Su líder es Elisur, hijo de Sedeúr,
Kummwera kudzakhala magulu a msasa wa Rubeni pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri.
11 cuenta con 46.500 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500.
12 La tribu de Simeón acampará junto a ellos. Su líder es Selumiel, hijo de Zurisadai,
Fuko la Simeoni lidzamanga pafupi ndi Rubeni. Mtsogoleri wa gulu la Simeoni ndi Selumieli mwana wa Zurisadai.
13 y cuenta con 59.300 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 59,300.
14 La siguiente es la tribu de Gad. Su líder es Eliasaph, hijo de Deuel,
Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli.
15 y cuenta con 45.650 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650.
16 Así que el número total de hombres en el área del campamento de Rubén es de 151.450. Ellos marcharán en segundo lugar.
Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka.
17 “El Tabernáculo de Reunión que está en el centro del campamento acompañará a los levitas. Deben marchar en el mismo orden en que levantaron el campamento, cada uno en el lugar que le corresponde, bajo su bandera.
Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake.
18 “La tribu de Efraín acampará bajo su bandera en el lado oeste. Su líder es Elisama, hijo de Amiud,
Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi.
19 y cuenta con 40.500 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500.
20 La tribu de Manasés acampará junto a ellos. Su líder es Gamaliel, hijo de Pedasur,
Fuko la Manase lidzakhala pafupi ndi Efereimu. Mtsogoleri wa Amanase ndi Gamalieli mwana wa Pedazuri.
21 y cuenta con 32.200 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 32,200.
22 La siguiente es la tribu de Benjamín. Su líder es Abidán, hijo de Gedeoni,
Lotsatira lidzakhala fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa Abenjamini ndi Abidani mwana wa Gideoni.
23 y cuenta con 35.400 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400.
24 Así que el número total de hombres en el área del campamento de Efraín es de 108.100. Ellos marcharán en tercer lugar.
Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka.
25 “La tribu de Dan acampará bajo su bandera en el lado norte. Su líder es Ajiezer, hijo de Amisadai,
Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
26 y cuenta con 62.700 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700.
27 La tribu de Aser acampará junto a ellos. Su líder es Pagiel, hijo de Ocrán,
Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani.
28 y cuenta con 41.500 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500.
29 A continuación estará la tribu de Neftalí. Su líder es Ajirá, hijo de Enán,
Lotsatira lidzakhala fuko la Nafutali. Mtsogoleri wa Anafutali ndi Ahira mwana wa Enani.
30 y cuenta con 53.400 hombres.
Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400.
31 Así que el total de hombres en el área del campamento de Dan es de 157.600. Ellos marcharán en último lugar, con sus banderas”.
Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo.
32 Este es un resumen del censo de los israelitas, hecho por familia. El total final de los contados en los campamentos por tribus fue de 603.550.
Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo.
33 Sin embargo, los levitas no fueron contados entre los demás israelitas, siguiendo las instrucciones que el Señor le dio a Moisés.
Koma Alevi sanawawerenge pamodzi ndi Aisraeli enawo monga momwe Yehova analamulira Mose.
34 Los israelitas hicieron todo lo que el Señor le ordenó a Moisés. Establecieron sus campamentos bajo sus banderas en sus posiciones asignadas, y marchaban en el mismo orden, cada uno con su propia tribu y familia.
Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo.

< Números 2 >