< Isaías 4 >
1 En ese tiempo, siete mujeres se agarrarán a un solo hombre y le dirán: “Comeremos nuestra propia comida y podemos proporcionarnos nuestra propia ropa. Sólo déjanos tomar tu nombre al casarnos contigo. Por favor, quita nuestra desgracia”.
Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi, nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu, ndi kuvala zovala zathu; inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu. Tichotseni manyazi aumbeta!”
2 Pero en ese momento, “el retoño del Señor” será atractivo y glorioso; el fruto que produzca la tierra será el orgullo y la gloria de los supervivientes que queden en Israel.
Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli.
3 Todos los que permanezcan en Sión serán llamados santos – todos los que estén registrados entre los vivos de Jerusalén –
Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu.
4 una vez que el Señor haya lavado los excrementos de las hijas de Sión y haya limpiado las manchas de sangre de Jerusalén con un espíritu de juicio y un espíritu de fuego.
Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto.
5 Entonces el Señor creará sobre todo el monte Sión y sobre la asamblea de los que allí se reúnan una nube de humo durante el día y una llama de fuego ardiente durante la noche; sobre todo habrá este dosel glorioso.
Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova.
6 Será un lugar para estar a la sombra del calor diurno, y un refugio para esconderse de la tormenta y la lluvia.
Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.