< 1 Crónicas 29 >

1 Entonces el rey David dijo a todos los allí reunidos: “Mi hijo Salomón, elegido sólo por Dios, es joven e inexperto, y el trabajo a realizar es grande porque este Templo no será para el hombre, sino para el Señor Dios.
Kenaka, mfumu Davide inati kwa gulu lonse: “Mwana wanga Solomoni amene Mulungu wamusankha ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Ntchitoyi ndi yayikulu chifukwa nyumba yaufumuyi si ya munthu, koma ndi ya Yehova Mulungu.
2 Con todos mis medios he provisto para la casa de mi Dios: oro para los artículos de oro, plata para la plata, bronce para el bronce, hierro para el hierro y madera para la madera; piedras de ónice y piedras para los engastes: turquesa, piedras de diferentes colores, toda clase de piedras preciosas; y mucho mármol.
Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka.
3 “Además, por mi devoción a la casa de mi Dios, ahora doy mi fortuna personal de oro y plata, además de todo lo que he provisto para esta santa casa.
Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu:
4 3.000 talentos de oro -el oro de Ofir- y 7.000 talentos de plata refinada irán a cubrir las paredes de los edificios,
Matani 100 agolide (golide wa ku Ofiri) ndi matani 240 a siliva woyengeka bwino wokutira makoma a nyumba,
5 el oro para la orfebrería, y la plata para la platería, y para todo el trabajo de los artesanos. ¿Quién quiere comprometerse de buen grado a dar hoy al Señor?”
zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?”
6 Dieron de buena gana: los jefes de familia, los responsables de las tribus de Israel, los comandantes de millares y de centenas, y los funcionarios encargados de la obra del rey.
Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu.
7 Dieron para el servicio de la casa de Dios 5.000 talentos y 10.000 dáricos de oro, 10.000 talentos de plata, 18.000 talentos de bronce y 100.000 talentos de hierro.
Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo.
8 Los que tenían piedras preciosas las entregaron al tesoro de la casa del Señor, bajo la supervisión de Jehiel el gersonita.
Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni.
9 El pueblo celebró porque sus líderes habían estado tan dispuestos a dar al Señor, libremente y de todo corazón. El rey David también se alegró mucho.
Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri.
10 Entonces David alabó al Señor ante toda la asamblea: “¡Alabado seas, Señor, Dios de Israel, nuestro padre, por los siglos de los siglos!
Davide anatamanda Yehova pamaso pa gulu lonse, ponena kuti, “Mutamandidwe Inu Yehova Mulungu wa kholo lathu Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya.
11 Señor, tuyos son la grandeza, el poder, la gloria, el esplendor y la majestad, porque todo lo que hay en el cielo y en la tierra es tuyo. Señor, tuyo es el reino, y eres admirado como gobernante de todo.
Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.
12 Las riquezas y el honor provienen de ti y tú reinas de forma suprema. Tú posees el poder y la fuerza, y tienes la capacidad de engrandecer a las personas y de dar fuerza a todos.
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.
13 “Ahora, nuestro Dios, te damos gracias y te alabamos a ti y a tu glorioso carácter.
Tsopano Mulungu wathu, ife tikukuthokozani ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.
14 Pero, ¿quién soy yo y quién es mi pueblo, para que seamos capaces de dar de tan buena gana? Porque todo lo que tenemos viene de ti; sólo te devolvemos lo que tú nos has dado.
“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu.
15 A tus ojos somos extranjeros y forasteros, como nuestros antepasados. Nuestro tiempo aquí en la tierra pasa como una sombra, no tenemos esperanza de quedarnos mucho tiempo.
Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo.
16 “Señor, Dios nuestro, incluso toda esta riqueza que hemos proporcionado para construirte una casa para tu santo nombre proviene de lo que tú das, y todo te pertenece.
Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu.
17 Yo sé, Dios mío, que tú miras por dentro y te alegras cuando vivimos bien. Todo lo he dado de buena gana y con un corazón honesto, y ahora he visto a tu pueblo aquí dando felizmente y de buena gana para ti.
Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu.
18 Señor, el Dios de Abraham, de Isaac, de Israel y de nuestros antepasados, por favor, mantén estos pensamientos y compromisos en la mente de tu pueblo para siempre, y haz que permanezcan leales a ti.
Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu.
19 Por favor, dale también a mi hijo Salomón el deseo de cumplir de todo corazón tus mandamientos, decretos y estatutos, y de hacer todo lo posible para construir tu Templo que yo he dispuesto”.
Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.”
20 Entonces David dijo a todos los presentes: “¡Alaben al Señor, su Dios!” Y todos alabaron al Señor, el Dios de sus padres. Se inclinaron en reverencia ante el Señor y ante el rey.
Kenaka mfumu Davide inati kwa gulu lonse, “Tamandani Yehova Mulungu wanu.” Kotero onse anatamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anawerama pansi ndi kugona chafufumimba pamaso pa Yehova ndi mfumu.
21 Al día siguiente presentaron sacrificios y holocaustos al Señor: mil toros, mil carneros y mil corderos, con sus libaciones y abundantes sacrificios para todo Israel.
Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse.
22 Entonces comieron y bebieron en presencia del Señor con gran alegría aquel día. Hicieron rey por segunda vez a Salomón, hijo de David, y lo ungieron como gobernante del Señor, y ungieron a Sadoc como sacerdote.
Tsiku limeneli, iwo anadya ndi kumwa mosangalala pamaso pa Yehova ndipo anavomereza Solomoni mwana wa Davide kukhala mfumu yawo kachiwiri. Anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala wolamulira wawo ndipo Zadoki anadzozedwa kukhala wansembe.
23 Así Salomón ocupó el trono del Señor como rey en lugar de David, su padre. Tuvo éxito, y todos los israelitas le obedecieron.
Ndipo Solomoni ankakhala pa mpando waufumu wa Yehova monga mfumu mʼmalo mwa Davide abambo ake. Iye analemera ndipo Aisraeli onse ankamumvera.
24 Todos los funcionarios y guerreros, así como todos los hijos del rey David, hicieron una promesa solemne de lealtad al rey Salomón.
Akuluakulu onse a ankhondo ndi anthu amphamvu, pamodzinso ndi ana onse aamuna a mfumu Davide, analonjeza kumvera mfumu Solomoni.
25 El Señor hizo que Salomón fuera muy respetado en todo Israel, y le dio mayor majestad real que la que se le había dado a cualquier otro rey de Israel antes de él.
Yehova anamukweza kwambiri Solomoni pamaso pa Aisraeli onse ndi kumupatsa ulemerero waufumu umene sunapatsidwepo kwa mfumu ina iliyonse ya Israeli.
26 Así, David, hijo de Isaí, gobernó sobre todo Israel.
Davide mwana wa Yese anali mfumu ya Aisraeli onse.
27 Gobernó sobre Israel cuarenta años: siete en Hebrón y treinta y tres en Jerusalén.
Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu.
28 David murió a una buena edad, habiendo vivido una larga vida bendecida con riquezas y honor. Entonces su hijo Salomón tomó el relevo y gobernó en su lugar.
Iye anamwalira atakalamba kwambiri, atakhala ndi moyo wautali, chuma ndi ulemu. Solomoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
29 Todo lo que hizo el rey David, desde el principio hasta el final, está escrito en las Actas de Samuel el Vidente, las Actas de Natán el Profeta y las Actas de Gad el Vidente.
Tsono zonse zimene mfumu Davide anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mneneri Samueli, mʼbuku la mneneri Natani ndi mʼbuku la mneneri Gadi,
30 Estos incluyen todos los detalles de su reinado, su poder y lo que le sucedió a él, a Israel y a todos los reinos de los países vecinos.
pamodzi ndi tsatanetsatane wa mbiri ya ulamuliro wake ndi mphamvu zake, ndi zonse zomwe zinamuzungulira iye ndi Israeli ndiponso mafumu a mayiko ena onse.

< 1 Crónicas 29 >