< Izaija 42 >
1 Glej, moj služabnik, ki ga podpiram; moj izvoljeni, v katerem se moja duša razveseljuje; svojega duha sem položil nanj. Oznanil bo sodbo poganom.
“Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza, amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye. Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
2 Ne bo vpil, niti povzdignil [glasu], niti svojemu glasu ne bo povzročil, da bi bil slišan na ulici.
Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu, kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.
3 Poškodovanega trsta ne bo zlomil in kadečega stenja ne bo ugasnil. Sodbo bo privedel k resnici.
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa. Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;
4 Ne bo opešal niti ne bo izgubil poguma, dokler ne postavi sodbe na zemlji in otoki bodo čakali na njegovo postavo.
sadzafowoka kapena kukhumudwa mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi, ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
5 Tako govori Gospod Bog, ki je ustvaril nebesa in jih razpel; ki je razprostrl zemljo in to, kar prihaja iz nje; on, ki daje dih ljudstvu na njej in duha tem, ki hodijo po njej:
Yehova Mulungu amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika, amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka, amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo, ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
6 »Jaz, Gospod, sem te poklical v pravičnosti in držal bom tvojo roko in te varoval in dam te za zavezo ljudstvu, za svetlobo poganom,
“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama; ndikugwira dzanja ndipo ndidzakuteteza. Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
7 da odpreš slepe oči, da privedeš jetnike iz ječe in te, ki sedijo v temi, ven iz jetnišnice.
Udzatsekula maso a anthu osaona, udzamasula anthu a mʼndende ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
8 Jaz sem Gospod. To je moje ime in svoje slave ne bom dal drugemu niti svoje hvale rezanim podobam.
“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.
9 Glej, prejšnje stvari so se zgodile in razglašam nove stvari. Preden vzbrstijo ti povem o njih.«
Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi, ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano; zinthuzo zisanaonekere Ine ndakudziwitsani.”
10 Zapojte Gospodu novo pesem in njegovo hvalo s konca zemlje, vi, ki greste dol do morja in vse, kar je v njem, otoki in njegovi prebivalci.
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi, inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo. Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.
11 Naj divjina in njena mesta dvignejo svoj glas, vasi, ki jih naseljuje Kedár. Naj skalni prebivalci pojejo, naj zavpijejo z vrhov gora.
Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo; midzi ya Akedara ikondwere. Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe; afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri.
12 Naj dajo slavo Gospodu in razglašajo njegovo hvalo na otokih.
Atamande Yehova ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse.
13 Gospod bo šel naprej kakor mogočen mož, ljubosumnost bo razvnel kakor bojevnik. Vpil bo, da, rjovel, prevladal bo zoper svoje sovražnike.
Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu, adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo; akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo ndipo adzagonjetsa adani ake.
14 »Dolgo časa sem zadrževal svoj mir, bil sem tiho in se zadrževal. Sedaj [pa] bom vpil kakor ženska v porodnih mukah; hkrati bom uničil in požrl.
Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali, ndakhala ndili phee osachita kanthu. Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira, ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.
15 Opustošil bom gore in hribe in posušil vsa njihova zelišča in reke bom naredil otoke in posušil bom ribnike.
Ndidzawononga mapiri ndi zitunda ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse; ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba ndipo ndidzawumitsa maiwe.
16 Privedel bom slepe po poti, ki je niso poznali, vodil jih bom po stezah, ki jih niso poznali. Temo pred njimi bom naredil svetlobo in skrivljene stvari ravne. Te stvari jim bom storil in ne bom jih zapustil.
Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe, ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo; ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala ndipo ndidzasalaza malo osalala. Zimenezi ndizo ndidzachite; sindidzawataya.
17 Obrnjeni bodo nazaj, silno bodo osramočeni tisti, ki zaupajo v rezane podobe, ki ulitim podobam pravijo: ›Vi ste naši bogovi.‹
Koma onse amene amadalira mafano amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ ndidzawachititsa manyazi kotheratu.
18 Poslušajte, vi gluhi, in glejte, vi slepi, da boste lahko videli.
“Imvani, agonthi inu; yangʼanani osaona inu, kuti muone!
19 Kdo je slep, razen mojega služabnika? Ali gluh kakor moj poslanec, ki sem ga poslal? Kdo je slep, kakor kdor je popoln in slep kakor Gospodov služabnik?
Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi? Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma? Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano, kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?
20 Gleda mnoge stvari, toda ti jih ne obeležuješ; odpira ušesa, toda on ne sliši.
Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale; makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”
21 Gospod je zelo zadovoljen zaradi svoje pravičnosti; poveličeval bo postavo in jo naredil častitljivo.
Chinamukomera Yehova chifukwa cha chilungamo chake, kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.
22 Toda to je ljudstvo, oropano in oplenjeno; vsi izmed njih so ujeti v luknje in skriti v jetnišnicah. Za plen so in nihče ne osvobaja; za ukradeno blago in nihče ne reče: ›Povrni.‹
Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo, onsewa anawakola mʼmaenje kapena akuwabisa mʼndende. Tsono asanduka chofunkha popanda wina wowapulumutsa kapena kunena kuti, “Abwezeni kwawo.”
23 Kdo izmed vas bo temu pazljivo prisluhnil? Kdo bo prisluhnil in slišal za čas, ki pride?
Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo?
24 Kdo je Jakoba izročil v plen in Izraela roparjem? Mar ne Gospod, on, zoper katerega smo grešili? Kajti niso želeli hoditi po njegovih poteh niti niso bili poslušni njegovi postavi.
Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha, ndi Israeli kwa anthu akuba? Kodi si Yehova, amene ife tamuchimwirayu? Pakuti sanathe kutsatira njira zake; ndipo sanamvere malangizo ake.
25 Zato je nanj izlil razjarjenost svoje jeze in moč bitke. To ga je vžgalo vsenaokoli, vendar ni vedel. To ga je žgalo, vendar si tega ni vzel k srcu.«
Motero anawakwiyira kwambiri, nawavutitsa ndi nkhondo. Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse; motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.