< Ezekiel 24 >

1 V devetem letu, v desetem mesecu, na deseti dan meseca je ponovno prišla k meni Gospodova beseda, rekoč:
Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti:
2 »Človeški sin, zapiši si ime dneva, celó tega istega dne. Babilonski kralj se je ta isti dan nameril zoper [prestolnico] Jeruzalem.
“Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino.
3 In izreci prispodobo uporni hiši ter jim reci: ›Tako govori Gospod Bog: ›Pristavi lonec, pristavi ga in prav tako vanj nalij vodo.
Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti, “‘Ikani mʼphika pa moto, ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi.
4 Zberi vanj kose, celó vsak dober kos, stegno in pleče; napolni ga z izbranimi kostmi.
Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama, nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba. Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri.
5 Vzemi izbrano od tropa in pod njim prav tako sežgi kosti in naredi, da bo dobro vrelo in v njem naj prevrejo njegove kosti.‹
Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri. Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo. Madzi awire. Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’
6 Zato tako govori Gospod Bog: ›Gorje krvoločnemu mestu, loncu, čigar plast umazanije je v njem in katerega plast umazanije ni odšla od njega! Prinesi to ven, kos za kosom; naj noben žreb ne pade na to.
“‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti, “‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi, tsoka kwa mʼphika wadzimbiri; dzimbiri lake losachoka! Mutulutsemo nthuli imodzimodzi osasankhulapo.
7 Kajti njena kri je v njeni sredi; postavljala jo je na vrh skale; ni je izlivala na tla, da jo pokrije s prahom;
“‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo. Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala. Sanawakhutulire pa dothi kuopa kuti fumbi lingawafotsere.
8 da bi lahko povzročila razjarjenosti, da pride gor, da se maščuje; njeno kri sem postavil na vrh skale, da ne bi bila pokrita.‹
Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalala kuti asafotseredwe ndi fumbi chifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.
9 Zato tako govori Gospod Bog: ›Gorje krvoločnemu mestu! Naredil bom celo grmado za velik ogenj.
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: “‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi! Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni.
10 Nakopičite les, zanetite ogenj, použijte meso in ga dobro začinite in naj bodo kosti sežgane.
Choncho wonjeza nkhuni ndipo muyatse moto. Phikani nyamayo bwinobwino, muthiremo zokometsera, mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo.
11 Potem ga praznega postavite na ognjeno oglje, da njegov bron lahko razbeli in lahko zagori in da bo njegova umazanost lahko v njem stopljena, da bo plast umazanije v njem lahko použita.
Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwo mpaka utenthe kuchita kuti psuu kuti zonyansa zake zisungunuke ndi kuti dzimbiri lake lichoke.
12 Samo sebe je izmučila z lažmi in njena velika plast umazanije ni šla ven iz nje. Njena plast umazanije bo v ognju.
Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa. Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchoka ngakhale ndi moto womwe.
13 V tvoji umazanosti je nespodobnost. Ker sem te očistil, ti pa nisi bila očiščena, ne boš več očiščena svoje umazanosti, dokler svoji razjarjenosti ne storim, da počiva na tebi.
“‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe.
14 Jaz, Gospod, sem to govoril. To se bo zgodilo in jaz bom to storil; ne bom šel nazaj niti ne bom prizanašal niti se ne bom kesal; glede na tvoje poti in glede na tvoja početja te bodo sodili, ‹ govori Gospod Bog.«
“‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’”
15 Prav tako je prišla k meni Gospodova beseda, rekoč:
Yehova anandiyankhula kuti:
16 »Človeški sin, glej, z udarcem vzamem od tebe željo tvojih oči. Vendar ne boš žaloval niti jokal niti tvoje solze ne bodo tekle.
“Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
17 Zadrži se jokanja, nobenega žalovanja za mrtvimi ne opravljaj, nad svojo glavo si zaveži ruto in nadeni si svoje čevlje na svoja stopala in ne pokrivaj svojih ustnic in ne jej kruha od ljudi.«
Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.”
18 Tako sem ljudstvu govoril zjutraj, zvečer pa je moja žena umrla; in zjutraj sem storil, kakor mi je bilo ukazano.
Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira.
19 In ljudstvo mi je reklo: »Ali nam ne boš povedal kaj so nam te stvari, da jih tako počneš?«
Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?”
20 Potem sem jim odgovoril: »K meni je prišla Gospodova beseda, rekoč:
Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti,
21 ›Govori Izraelovi hiši: ›Tako govori Gospod Bog: ›Glejte, oskrunil bom svoje svetišče, odličnost vaše moči, željo vaših oči in to, kar vaša duša pomiluje; in vaši sinovi in vaše hčere, ki ste jih pustili, bodo padli pod mečem.
‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga.
22 In storili boste, kakor sem jaz storil: ne boste pokrili svojih ustnic niti jedli kruha od ljudi.
Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa.
23 In vaše rute bodo na vaših glavah in vaši čevlji na vaših stopalih. Ne boste niti žalovali niti jokali; temveč boste hirali zaradi svojih krivičnosti in žalovali drug proti drugemu.
Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu.
24 Tako vam je Ezekiel znamenje: glede na vse, kar je storil, boste vi storili. In ko to pride, boste spoznali, da jaz sem Gospod Bog.
Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’
25 Tudi ti, človeški sin, ali ne bo to na dan, ko jim odvzamem njihovo moč, radost njihove slave, željo njihovih oči in to, na kar so naravnali svoje ume, njihove sinove in njihove hčere,
“Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi.
26 da bo tisti, ki pobegne na ta dan, prišel k tebi, da ti povzroči, da to slišiš s svojimi lastnimi ušesi?
Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo.
27 Na tisti dan se bodo tvoja usta odprla k tistemu, ki je pobegnil in govoril boš in ne boš več nem. Ti jim boš znamenje. In spoznali bodo, da jaz sem Gospod.‹«
Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

< Ezekiel 24 >