< Откровение ап. Иоанна Богослова 19 >
1 И по сих слышах глас велий народа многа на небеси, глаголющаго: аллилуиа: спасение и слава, и честь и сила Господу нашему,
Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti, “Haleluya! Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
2 яко истинни и прави суди Его: яко судил есть любодейцу велику, яже посмради землю любодеянием своим, и отмстил кровь рабов Своих от руки ея.
pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”
3 И второе реша: аллилуиа. И дым ея восхождаше во веки веков. (aiōn )
Ndipo anafuwulanso kuti, “Haleluya! Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.” (aiōn )
4 И падоша двадесять и четыри старцы и четыри животна и поклонишася Богови седящему на престоле, глаголюще: аминь, аллилуиа.
Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti, “Ameni, Haleluya!”
5 И глас изыде от престола глаголющь: пойте Богу нашему, вси раби Его и боящиися Его, и малии и велицыи.
Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti, “Lemekezani Mulungu wathu inu nonse atumiki ake, inu amene mumamuopa, nonse angʼono ndi akulu!”
6 И слышах яко глас народа многа, и яко глас вод многих, и яко глас громов крепких, глаголющих: аллилуиа, яко воцарися Господь Бог Вседержитель:
Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati, “Haleluya! Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.
7 радуимся и веселимся, и дадим славу Ему: яко прииде брак Агнчий, и жена Его уготовила есть себе.
Tiyeni tisangalale ndi kukondwera ndi kumutamanda! Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika, ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.
8 И дано бысть ей облещися в виссон чист и светел: виссон бо оправдания святых есть.
Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada kuti avale.” (Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).
9 И глагола ми: напиши: блажени званнии на вечерю брака Агнча. И глагола ми: сия словеса истинна Божия суть.
Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”
10 И пад пред ногама его, поклонихся ему: и глагола ми: виждь, ни: клеврет ти есмь и братий твоих имущих свидетелство Иисусово: Богу поклонися: свидетелство бо Иисусово есть дух пророчествия.
Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”
11 И видех небо отверсто, и се, конь бел, и седяй на нем Верен и Истинен, и Правосудный и Воинственный:
Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama.
12 очи же Ему (еста) яко пламень огнен, и на главе Его венцы мнози: имый имя написано, еже никтоже весть, токмо Он Сам:
Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense.
13 и облечен в ризу червлену кровию. И нарицается имя Его Слово Божие.
Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu.
14 И воинства небесная идяху вслед Его на конех белых, облечени в виссон бел и чист.
Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada.
15 И из уст Его изыде оружие остро, да тем избиет языки: и Той упасет я жезлом железным, и Той перет точило вина ярости и гнева Божия Вседержителева.
Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse.
16 И имать на ризе и на стегне Своем имя написано: Царь царем и Господь господем.
Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili: MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.
17 И видех единаго Ангела стояща на солнце: и возопи гласом велиим, глаголя всем птицам парящым посреде небесе: приидите и соберитеся на вечерю великую Божию,
Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu.
18 да снесте плоти царей и плоти крепких и плоти тысящников, и плоти коней и седящих на них, и плоти всех свободных и рабов, и малых и великих.
Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”
19 И видех зверя и цари земныя и вои их собраны сотворити брань с Седящим на кони и с воинствы Его.
Kenaka ndinaona chirombo chija ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu ankhondo atasonkhana pamodzi kuti achite nkhondo ndi wokwera pa kavalo ndi ankhondo ake.
20 И ят бысть зверь и с ним лживый пророк, сотворивый знамения пред ним, имиже прельсти приемшыя начертание зверино и покланяющыяся иконе его: жива ввержена быста оба в езеро огненное горящее жупелом: (Limnē Pyr )
Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. (Limnē Pyr )
21 а прочии убиени быша оружием Седящаго на кони, изшедшим из уст Его: и вся птицы насытишася от плотей их.
Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.