< Левит 20 >
1 И рече Господь к Моисею, глаголя:
Yehova anawuza Mose kuti,
2 рцы сыном Израилевым, глаголя: аще кто от сынов Израилевых, или от прибывших пришелцев во Израили, иже аще даст от семене своего Молоху, смертию да умрет: людие земли да побиют его камением:
“Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala.
3 и Аз утвержу лице Мое на человека того и погублю его от людий его, яко от семене своего даде Молоху, да осквернит святыню Мою и осквернит имя освященных Мне.
Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera.
4 Аще же презрением презрят туземцы земли очима своима от человека того, внегда дати ему от семене своего Молоху, еже не убити его:
Ngati anthu a mʼderalo achita ngati sakumuona munthuyo pamene akupereka mwana wake kwa Moleki ndi kusamupha,
5 и утвержу лице Мое на человека того и на сродники его, и погублю его и всех единомыслящих с ним, еже соблуждати ему со идолы от людий своих.
Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”
6 И душа яже аще последует утробным баснем или волхвом, яко соблудити вслед их, утвержу лице Мое на душу ту и погублю ю от людий ея.
“‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake.
7 И будете святи, яко Аз свят Господь Бог ваш.
“‘Chifukwa chake dzipatuleni ndi kukhala woyera popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
8 И сохраните повеления Моя и сотворите я: Аз Господь освящаяй вас.
Ndipo sungani malangizo anga ndi kuwatsata. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani.
9 Человек человек, иже аше зло речет отцу своему или матери своей, смертию да умрет: отцу своему или матери своей зле рече, повинен будет.
“‘Munthu aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. Magazi ake adzakhala pamutu pake chifukwa iye watemberera abambo kapena amayi ake.
10 Человек человек, иже аще прелюбы содеет с мужнею женою, или кто прелюбы содеет с женою ближняго своего, смертию да умрут прелюбодей и прелюбодейца.
“‘Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa.
11 И иже аще пребудет с женою отца своего, срамоту отца своего открыл есть, смертию да умрут оба, повинни суть.
“‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa abambo ake, wachititsa manyazi abambo ake. Munthuyo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. Magazi awo adzakhala pa mitu pake.
12 И аще кто будет с невесткою своею, смертию да умрут оба, нечествоваша бо, повинни суть.
“‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
13 И аще кто будет с мужеским полом ложем женским, гнусность сотвориша оба, смертию да умрут, повинни суть:
“‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
14 иже аще поймет жену и матерь ея, беззаконие есть, огнем да сожгут его и оныя, и не будет беззаконие в вас.
“‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu.
15 И иже аще даст ложе свое четвероножному, смертию да умрет, четвероножное же убиете.
“‘Ngati mwamuna agonana ndi nyama, iye ayenera kuphedwa, ndipo muyeneranso kupha nyamayo.
16 И жена яже аше приступит ко всякому скоту, еже быти с ним, да убиете жену и скот, смертию да умрут, повинни суть.
“‘Ngati mkazi agonana ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Mkaziyo ndi nyamayo ayenera kuphedwa, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
17 Иже аще поймет сестру свою от отца своего или от матере своея, и увидит срамоту ея, и она увидит срамоту его, укоризна есть, да потребятся пред сыны рода их: срамоту сестры своея откры, грех приимут.
“‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango.
18 И муж иже будет с женою сквернавою и открыет срамоту ея, течение ея откры, и она откры течение крове своея, да потребятся оба от рода их.
“‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo.
19 И срамоту сестры отца твоего и сестры матере твоея да не открыеши: ужичество бо откры, грех понесут.
“‘Musagonane ndi mchemwali wa amayi anu kapena abambo anu, pakuti kutero ndi kuchititsa manyazi mʼbale wanu. Nonse mudzalipira mlandu wanu.
20 Иже аще будет со сродницею своею, срамоту сродства своего откры, безчадни измрут.
“‘Ngati munthu agonana ndi azakhali ake, munthuyo wachititsa manyazi a malume ake. Onse adzalipira mlandu wawo. Onsewo adzafa wopanda mwana.
21 И человек иже аще поймет жену брата своего, нечистота есть: срамоту брата своего открыл есть, безчадни измрут.
“‘Munthu akakwatira mkazi wa mchimwene wake ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wachititsa manyazi mʼbale wakeyo. Onse awiriwo adzakhala wopanda mwana.
22 И сохраните вся повеления Моя и вся судбы Моя и сотворите я, и не вознегодует на вас земля, в нюже Аз введу вы тамо вселитися на ней.
“‘Nʼchifukwa chake muzisunga malangizo anga onse ndi malamulo anga ndipo muwatsatire kuti ku dziko limene Ine ndikupita nanu kuti mukakhalemo lisakakusanzeni.
23 И не ходите в законы языческия, ихже Аз изгоню от вас: яко сия вся сотвориша, и возгнушахся ими.
Musatsanzire miyambo ya mitundu ya anthu imene ndi kuyipirikitsa inu mukufika. Chifukwa iwo anachita zinthu zonsezi, ndipo Ine ndinanyansidwa nawo.
24 И рех к вам: вы наследите землю их, и Аз дам вам ю в притяжание, землю текущую медом и млеком, Аз Господь Бог ваш, отлучивый вас от всех язык.
Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.
25 И отлучите себе между скоты чистыми и между скоты нечистыми, и между птицами чистыми и нечистыми: и не оскверните душ ваших в скотех и в птицах и во всех гадех земных, яже Аз отлучих вам в нечистоте,
“‘Chifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoyeretsedwa ndi nyama zodetsedwa ndiponso pakati pa mbalame zoyeretsedwa ndi mbalame zodetsedwa. Musadzidetse pakudya nyama iliyonse kapena mbalame, kapena chilichonse chimene chimakwawa pansi, chimene Ine ndachipatula kuti chikhale chodetsedwa kwa inu.
26 и будете Ми святи, яко Аз свят есмь Господь Бог ваш, отлучивый вас от всех язык быти Моими.
Muzikhala woyera pamaso panga chifukwa Ine Yehova, ndine woyera ndipo ndakupatulani pakati pa anthu a mitundu yonse kuti mukhale anthu anga.
27 И муж или жена иже аще будет от них чревобасник или волшебник, смертию да умрут оба: камением да побиете их, повинни суть.
“‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’”