< Книга Иисуса Навина 11 >

1 Егда же услыша Иавин царь Асорск, посла ко Иоваву царю Мадонску, и к царю Семеронску и к царю Ахиавску,
Yabini, mfumu ya Hazori, inamva zimene zinachitikazi. Tsono inatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu.
2 и к царем иже в Сидоне велицем и в горней, и в Араву прямо Хенерефу, и на поляну, и в Нафеддор,
Inatumizanso uthenga kwa mafumu a kumpoto, kumapiri, ndi mʼchigwa cha Yorodani kummwera kwa nyanja ya Kinereti, ndiponso kumadzulo mʼmbali mwa nyanja pafupi ndi Dori.
3 и к приморским Хананеам от восток, и к приморским Аморреом и Хеттеом, и Ферезеом и Иевусеом, иже на горе, и Евеом, и иже под Аермоном, в землю Массифа.
Inatumizanso uthenga kwa Akanaani amene ankakhala kummawa ndi kumadzulo kwa Yorodani. Uthenga unapitanso kwa Aamori, Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi amene amakhala mʼdziko la ku mapiri ndiponso kwa Ahivi amene ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni ku chigwa cha Mizipa.
4 И изыдоша сии и царие их с ними, людие мнози, яко песок иже при краи моря множеством, и кони и колесницы многи зело.
Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri.
5 И снидошася вси царие сии, и приидоша вкупе, и ополчишася при воде Маррон воевати на Израиля.
Mafumu onsewa anasonkhana pamodzi ndipo anamanga misasa yawo ku mtsinje wa Meromu, kuti amenyane ndi Israeli.
6 И рече Господь ко Иисусу: не убойся от лица их, яко заутра в сей час Аз предам их язвенных пред сыны Израилевы: конем их жилы пресечеши и колесницы их да сожжеши огнем.
Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.”
7 И прииде Иисус и вси людие воинстии с ним на них к воде Марронстей внезапу, и нападоша на ня в горней.
Kotero Yoswa pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo anafika kwa adani awo aja ku mtsinje wa Meromu modzidzimutsa ndi kuwathira nkhondo.
8 И предаде их Господь под руце Израилевы: и секуще их, прогнаша даже до Сидона великаго и до Масрефоф-Маима и до поль Массифских к востоком: и изсекоша их, дондеже не остася в них ни един цел и избегший.
Yehova anawapereka mʼmanja mwa Israeli mwakuti anawagonjetseratu ndi kuwapirikitsa njira yonse mpaka ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti Maimu, ndiponso kummawa ku chigwa cha Mizipa. Onse anaphedwa popanda wopulumuka.
9 И сотвори им Иисус, якоже заповеда ему Господь: конем их жилы пресече и колесницы их сожже огнем.
Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo.
10 И обратися Иисус в то время, и взя Асор, и царя его уби мечем: Асор бо бе прежде обладающий всеми царствы сими:
Pambuyo pake Yoswa anabwera nalanda mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. (Nthawi imeneyo mzinda wa Hazori unali wopambana mizinda ina yonse).
11 и изби все дышущее, еже в нем бысть, острием меча, и потребиша вся, и не остася в нем все дышущее: и Асор запалиша огнем.
Anapha aliyense wa mu mzindamo popanda wotsala wamoyo, ndipo mzinda wa Hazori anawutentha ndi moto.
12 И вся грады царств сих и вся цари их взя Иисус и изби я мечем, и потреби их, якоже повеле им Моисей раб Господень.
Yoswa analanda mizinda yonse ndi mafumu ake. Anthu onse anaphedwa ndi lupanga monga momwe analamulira Mose, mtumiki wa Yehova.
13 Но вся грады крепки не запали Израиль, точию Асор един запали Иисус.
Israeli sanatenthe mizinda yomangidwa pa zitunda, kupatula mzinda wa Hazori, umene Yoswa anawutentha.
14 И вся корысти их и вся скоты их плениша себе сынове Израилевы: людий же всех потребиша мечем, дондеже погубиша их, и не оставиша от них ни единаго дышущаго.
Aisraeli anatenga zinthu zonse za mʼmizindayi pamodzi ndi ziweto kuti zikhale zawo, koma anapha anthu onse ndi lupanga osasiyako ndi mmodzi yemwe wamoyo.
15 Якоже повеле Господь Моисею рабу Своему, тако Моисей заповеда Иисусу: и тако сотвори Иисус, не преступи ни единаго же от всех, яже заповеда Господь Моисею.
Monga momwe Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamulira Yoswa ndipo Yoswa anachita chilichonse chimene Yehova analamulira Mose.
16 И взя Иисус всю землю горную и всю землю нагев, и всю землю Госомску, и равную, и яже на запад, и гору Израилеву, и поля яже при горе,
Kotero Yoswa analanda dziko lonse: dziko la ku mapiri, dera lonse la Negevi, chigawo chonse cha Goseni, ndi chigwa chake chonse, chigwa cha Yorodani, dziko lonse la lamapiri la Israeli pamodzi ndi chigwa chake chomwe.
17 от горы Хелха, и яже восходит к Сеиру, и даже до Валгада, и поле Ливана под горою Аермон: и вся цари их взя и изби.
Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo
18 И многи дни сотвори Иисус с цари сими брань:
atachita nawo nkhondo kwa nthawi yayitali.
19 и не бе ни единаго града, егоже не предаде Господь сыном Израилевым, кроме Евеа обитающаго в Гаваоне: всех взяша бранию:
Palibe ngakhale ndi mfumu imodzi yomwe imene inachita mgwirizano wa mtendere ndi Aisraeli kupatula Ahivi okhala ku Gibiyoni. Koma mizinda ina yonse anachita kuyigonjetsa pa nkhondo.
20 яко Господем бысть укрепитися их сердцу, сопротивитися на брани противу Израиля, да потребят их, яко да не дастся им милость, но да потребятся, якоже глагола Господь к Моисею.
Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe.
21 И прииде Иисус в то время, и потреби (вся) Енакимы от горныя, от Хеврона и от Давира и от Анова, и от всея горы Израилевы и от всея горы Иудины, с грады их, и потреби я Иисус:
Pa nthawi imeneyi Yoswa anapita kukawononga Aanaki okhala mʼdziko lija la ku mapiri ku Hebroni, Debri, Anabu komanso madera onse a ku mapiri a Yuda ndi Israeli. Yoswa anawawononga onse pamodzi ndi mizinda yawo.
22 не остася ни един Енаким от сынов Израилевых, но точию в Газе и в Гефе и во Асидофе осташася.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsalako mʼdziko lonse la Israeli; komabe ku Gaza, ku Gati ndi Asidodi kokha ndi kumene anatsalako pangʼono.
23 И взя Иисус всю землю, якоже заповеда Господь Моисею: и даде ю Иисус в наследие Израилю, разделением по племеном их. И преста земля воюема быти.
Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake. Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo.

< Книга Иисуса Навина 11 >