< Послание к Колоссянам 1 >

1 Павел, Апостол Иисус Христов волею Божиею, и Тимофей брат,
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, ndi Timoteyo mʼbale wathu.
2 сущым в Колоссаех святым и верным братиям о Христе Иисусе:
Kulembera abale oyera mtima ndi okhulupirira a ku Kolose mwa Khristu. Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu.
3 благодать вам и мир от Бога Отца нашего, и Господа Иисуса Христа. Благодарим Бога и Отца Господа нашего Иисуса Христа, всегда о вас молящеся,
Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani.
4 слышавше веру вашу, яже о Христе Иисусе, и любовь, юже имате ко всем святым,
Timayamika chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse.
5 за упование отложенное вам на небесех, еже прежде слышасте в словеси истины благовествования,
Chikhulupiriro ndi chikondi, gwero lake ndi chiyembekezo chomwe muli nacho chodzalandira zimene anakusungirani kumwamba. Munamva kale za zimenezi kudzera mʼmawu a choonadi, Uthenga Wabwino
6 сущаго в вас, якоже и во всем мире: и есть плодоносно и растимо, якоже и в вас, от негоже дне слышасте и разуместе благодать Божию во истине:
umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse.
7 якоже и уведесте от Епафраса, возлюбленнаго соработника нашего, иже есть верен о вас служитель Христов,
Inu munaphunzira zimenezi kuchokera kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwathu.
8 иже и яви нам вашу любовь в дусе.
Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani.
9 Сего ради и мы, от негоже дне слышахом, не престаем о вас молящеся и просяще, да исполнитеся в разуме воли Его, во всяцей премудрости и разуме духовнем,
Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa.
10 яко ходити вам достоине Богу во всяцем угождении и всяком деле блазе, плодоносяще и возрастающе в разуме Божии,
Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu.
11 всякою силою возмогающе по державе славы Его, во всяцем терпении и долготерпении с радостию.
Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe
12 Благодаряще Бога и Отца, призвавшаго вас в причастие наследия святых во свете.
ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika.
13 Иже избави нас от власти темныя и престави в Царство Сына любве Своея,
Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa.
14 о Немже имамы избавление Кровию Его и оставление грехов.
Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
15 Иже есть образ Бога невидимаго, перворожден всея твари.
Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse.
16 Яко Тем создана быша всяческая, яже на небеси и яже на земли, видимая и невидимая, аще престоли, аще господствия, аще начала, аще власти: всяческая Тем и о Нем создашася.
Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo.
17 И Той есть прежде всех, и всяческая в Нем состоятся.
Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye.
18 И Той есть глава телу Церкве, Иже есть начаток, перворожден из мертвых, яко да будет во всех Той первенствуя.
Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse.
19 Яко в Нем благоизволи всему исполнению вселитися,
Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu.
20 и Тем примирити всяческая к Себе, умиротворив Кровию креста Его, чрез Него, аще земная, аще ли небесная.
Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.
21 И вас, иногда сущих отчужденных и врагов помышленьми в делех лукавых,
Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa.
22 ныне же примири в теле Плоти Его смертию Его, представити вас святых и непорочных и неповинных пред Собою,
Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho
23 аще убо пребываете в вере основани и тверди, и неподвижими от упования благовествования, еже слышасте, проповеданное всей твари поднебесней, емуже бых аз Павел служитель.
ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
24 Ныне радуюся во страданиих моих о вас, яко исполняю лишение скорбей Христовых во плоти моей за Тело Его, еже есть Церковь.
Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo.
25 Ейже бых аз служитель по смотрению Божию, данному мне в вас, исполнити слово Божие,
Ine ndakhala mtumiki wake mwa lamulo limene Mulungu anandipatsa kuti ndipereke Mawu a Mulungu athunthu,
26 тайну сокровенную от век и от родов: ныне же явися святым Его, (aiōn g165)
chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. (aiōn g165)
27 Имже восхоте Бог сказати, кое богатство славы тайны сея во языцех, иже есть Христос в вас, упование славы,
Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.
28 Егоже мы проповедуем, наказующе всякаго человека и учаще всяцей премудрости, да представим всякаго человека совершенна о Христе Иисусе:
Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu.
29 в немже и труждаюся и подвизаюся по действу Его действуемому во мне силою.
Ndi cholinga chimenechi, ine ndikugwira ntchito molimbika ndi mwamphamvu zonse zimene Iye anachita mwa ine.

< Послание к Колоссянам 1 >