< Второе послание к Коринфянам 4 >
1 Сего ради имуще служение сие, якоже помиловани быхом, не стужаем си:
Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima.
2 но отрекохомся тайных срама, не в лукавствии ходяще, ни льстяще словесе Божия, но явлением истины представляюще себе ко всяцей совести человечестей, пред Богом.
Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake.
3 Аще ли же есть покровено благовествование наше, в гибнущих есть покровено,
Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika.
4 в нихже бог века сего ослепи разумы неверных, во еже не возсияти им свету благовествования славы Христовы, Иже есть образ Бога невидимаго. (aiōn )
Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu. (aiōn )
5 Не себе бо проповедаем, но Христа Иисуса Господа: себе же самех рабов вам Иисуса Господа ради:
Choncho sitilalikira za ife eni, koma Yesu Khristu monga Ambuye, ife ndife atumiki anu chifukwa cha Yesu.
6 яко Бог рекий из тмы свету возсияти, иже возсия в сердцах наших, к просвещению разума славы Божия о лицы Иисус Христове.
Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
7 Имамы же сокровище сие в скудельных сосудех, да премножество силы будет Божия, а не от нас:
Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.
8 во всем скорбяще, но не стужающе си: нечаеми, но не отчаяваеми:
Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima;
9 гоними, но не оставляеми: низлагаеми, но не погибающе:
tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka.
10 всегда мертвость Господа Иисуса в теле носяще, да и живот Иисусов в теле нашем явится.
Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu.
11 Присно бо мы живии в смерть предаемся Иисуса ради, да и живот Иисусов явится в мертвенней плоти нашей:
Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa.
12 темже смерть убо в нас действует, а живот в вас.
Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.
13 Имуще же тойже дух веры, по писанному: веровах, темже возглаголах: и мы веруем, темже и глаголем,
Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula,
14 ведяще, яко Воздвигий Господа Иисуса, и нас со Иисусом воздвигнет, и предпоставит с вами.
chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake.
15 Вся бо вас ради, да благодать умножившаяся, множайшими благодарении избыточествит в славу Божию.
Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.
16 Темже не стужаем си: но аще и внешний наш человек тлеет, обаче внутренний обновляется по вся дни.
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
17 Еже бо ныне легкое печали нашея, по преумножению в преспеяние тяготу вечныя славы соделовает нам, (aiōnios )
Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. (aiōnios )
18 не смотряющым нам видимых, но невидимых: видимая бо временна, невидимая же вечна. (aiōnios )
Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya. (aiōnios )