< Откривење 5 >
1 И видех у десници Оног што сеђаше на престолу књигу написану изнутра и споља, запечаћену са седам печата.
Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri.
2 И видех анђела јаког где проповеда гласом великим: Ко је достојан да отвори књигу и да разломи печате њене?
Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?”
3 И нико не могаше ни на небу ни на земљи, ни под земљом да отвори књиге ни да загледа у њу.
Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zamʼkati mwake.
4 И ја плаках много што се нико не нађе достојан да отвори и да прочита књигу, нити да загледа у њу.
Ndinalira kwambiri chifukwa panalibe amene anapezeka woyenera kufutukula bukuli kapena kuona zamʼkati mwake.
5 И један од старешина рече ми: Не плачи, ево је надвладао лав, који је од колена Јудиног, корен Давидов, да отвори књигу и разломи седам печата њених.
Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”
6 И видех, и гле, насред престола и четири животиње, и посред старешина Јагње стајаше као заклано, и имаше седам рогова, и седам очију, које су седам духова Божијих посланих по свему свету.
Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi.
7 И дође и узе књигу из деснице Оног што сеђаше на престолу.
Iye anabwera natenga buku lija limene linali mʼdzanja lamanja la wokhala pa mpando waufumuyo.
8 И кад узе књигу, четири животиње и двадесет и четири старешине падоше пред Јагњетом, имајући сваки гусле, и златне чаше пуне тамјана, које су молитве светих.
Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima.
9 И певаху песму нову говорећи: Достојан си да узмеш књигу, и да отвориш печате њене; јер си се заклао, и искупио си нас Богу крвљу својом од сваког колена и језика и народа и племена,
Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti, “Inu ndinu woyenera kulandira bukuli ndi kumatula zomatira zake, chifukwa munaphedwa, ndipo magazi anu munagulira Mulungu anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.
10 И учинио си нас Богу нашем цареве и свештенике, и цароваћемо на земљи.
Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu, ndipo adzalamulira dziko lapansi.”
11 И видех, и чух глас анђела многих око престола и животиња и старешина, и беше број њихов хиљада хиљада.
Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja.
12 Говорећи гласом великим: Достојно је Јагње заклано да прими силу и богатство и премудрост и јачину и част и славу и благослов.
Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti, “Mwana Wankhosa amene anaphedwayu ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu, ulemerero ndi mayamiko.”
13 И свако створење, што је на небу, и на земљи, и под земљом, и што је на мору, и што је у њима, све чух где говоре: Ономе што седи на престолу, и Јагњету благослов и част и слава и држава ва век века. (aiōn )
Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti, “Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa, kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu (aiōn )
14 И четири животиње говораху: Амин. И двадесет и четири старешине падоше и поклонише се Ономе што живи ва век века.
Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.