< Матеј 23 >

1 Тада Исус рече к народу и ученицима својим
Pamenepo Yesu anati kwa magulu a anthu ndi ophunzira ake:
2 Говорећи: На Мојсијеву столицу седоше књижевници и фарисеји.
“Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi amakhala pa mpando wa Mose.
3 Све дакле што вам кажу да држите, држите и творите; али шта они чине не чините; јер говоре а не чине.
Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa.
4 Него вежу бремена тешка и незгодна за ношење, и товаре на плећа људска; а прстом својим неће да их прихвате.
Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula.
5 А сва дела своја чине да их виде људи: раширују своје амајлије, и граде велике скуте на хаљинама својим.
“Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo.
6 И траже зачеље на гозбама и прва места по зборницама,
Amakonda malo aulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri mʼmasunagoge.
7 И да им се клања по улицама, и да их људи зову: Рави! Рави!
Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’
8 А ви се не зовите Рави; јер је у вас један Рави Христос, а ви сте сви браћа.
“Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale.
9 И оцем не зовите никога на земљи; јер је у вас један Отац који је на небесима.
Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba.
10 Нити се зовите Учитељи; јер је у вас један учитељ Христос.
Komanso musamatchedwenso ‘Mtsogoleri,’ pakuti muli naye Mtsogoleri mmodzi amene ndi Khristu.
11 А највећи између вас да вам буде слуга.
Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani.
12 Јер који се подиже, понизиће се, а који се понижује, подигнуће се.
Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.
13 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери, што затварате царство небеско од људи; јер ви не улазите нити дате да улазе који би хтели.
“Tsoka kwa inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumatseka pa khomo la kumwamba kuti anthu asalowemo. Eni akenu simulowamo komanso simulola kuti ena amene akufuna kulowa kuti alowe.
14 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери, што једете куће удовичке, и лажно се Богу молите дуго; зато ћете већма бити осуђени.
Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera akazi amasiye chuma chawo, kwinaku nʼkumanamizira kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.
15 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери, што проходите море и земљу да би присвојили једног, и кад га присвојите, чините га сином пакленим, удвоје већим од себе. (Geenna g1067)
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumayenda maulendo ambiri pa mtunda ndi pa nyanja kuti mutembenuze munthu mmodzi, ndipo akatembenuka, mumamusandutsa kukhala mwana wa gehena kawiri kuposa inu. (Geenna g1067)
16 Тешко вама вође слепе који говорите: Ако се ко куне црквом ништа је; а ако се ко куне златом црквеним крив је.
“Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’
17 Будале слепе! Шта је веће, или злато, или црква која злато освети.
Inu akhungu opusa! Chopambana nʼchiyani: ndalama zagolide, kapena Nyumba imene imayeretsa golideyo?
18 И ако се ко куне олтаром ништа је то, а који се куне даром који је на њему крив је
Ndiponso mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula guwa lansembe, sizitanthauza kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula mphatso ya paguwa lansembe, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’
19 Будале слепе! Шта је веће, или дар, или олтар који дар освети?
Inu anthu akhungu! Chopambana nʼchiyani: mphatso, kapena guwa limene limayeretsa mphatsoyo?
20 Који се дакле куне олтаром, куне се њим и свим што је на њему.
Chifukwa chake, iye amene alumbira kutchula guwa alumbira pa ilo ndi pa chilichonse chili pamenepo.
21 И који се куне црквом, куне се њом и Оним што живи у њој.
Ndipo iye wolumbira potchula Nyumba ya Mulungu alumbira pa Nyumbayo ndi pa Iye amene amakhala mʼmenemo.
22 И који се куне небом, куне се престолом Божјим и Оним који седи на њему.
Ndipo iye wolumbira kutchula kumwamba alumbira kutchula mpando waufumu wa Mulungu ndi pa Iye wokhalapo.
23 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери, што дајете десетак од метвице и од копра и од кима, а остависте шта је најпретежније у закону: правду и милост и веру; а ово је требало чинити и оно не остављати.
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo.
24 Вође слепе који оцеђујете комарца а камилу прождирете.
Atsogoleri akhungu inu! Mumachotsa kantchentche mu chakumwa chanu koma mumameza ngamira.
25 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери што чистите споља чашу и зделу а изнутра су пуне грабежа и неправде.
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkatimo mwadzaza ndi dyera ndi kusadziretsa.
26 Фарисеју слепи! Очисти најпре изнутра чашу и зделу да буду и споља чисте.
Afarisi akhungu! Poyamba tsukani mʼkati mwa chikho ndi mbale, ndipo kunja kwake kudzakhalanso koyera.
27 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери, што сте као окречени гробови, који се споља виде лепи а унутра су пуни костију мртвачких и сваке нечистоте.
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Muli ngati ziliza pa manda zowala kunja zimene zimaoneka zokongola koma mʼkatimo mwadzaza mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zina zonse.
28 Тако и ви споља се показујете људима праведни, а изнутра сте пуни лицемерја и безакоња.
Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina.
29 Тешко вама књижевници и фарисеји, лицемери, што зидате гробове пророцима и красите раке праведника,
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumamanga ziliza za aneneri ndi kukongoletsa manda a olungama.
30 И говорите: Да смо ми били у време својих отаца, не бисмо с њима пристали у крв пророка.
Ndipo mumati, ‘Ngati tikanakhala mʼmasiku a makolo athu sitikanakhetsa nawo magazi a aneneri.’
31 Тим само сведочите за себе да сте синови оних који су побили пророке.
Potero mukutsimikiza kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.
32 И ви допуните меру отаца својих.
Dzazani inu muyeso wa uchimo wa makolo anu!
33 Змије, породи аспидини! Како ћете побећи од пресуде у огањ паклени? (Geenna g1067)
“Njoka inu! Ana amamba! Mudzachithawa bwanji chilango cha gehena? (Geenna g1067)
34 Зато ево ја ћу к вама послати пророке и премудре и књижевнике; и ви ћете једне побити и распети а једне бити по зборницама својим и гонити од града до града,
Choncho ndi kutumizirani aneneri ndi anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ena mudzawakwapula mʼmasunagoge anu ndi kuwafunafuna kuchokera mudzi wina kufikira wina.
35 Да дође на вас сва крв праведна што је проливена на земљи од крви Авеља праведног до крви Зарије сина Варахијиног, кога убисте међу црквом и олтаром.
Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu.
36 Заиста вам кажем да ће ово све доћи на род овај.
Zoonadi, ndikuwuzani kuti zonsezi zidzafika pa mʼbado uno.
37 Јерусалиме, Јерусалиме, који убијаш пророке и засипаш камењем послане к себи! Колико пута хтех да скупим чеда твоја као што кокош скупља пилиће своје под крила и не хтесте!
“Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune.
38 Ето ће вам се оставити ваша кућа пуста.
Taona, nyumba yako yasiyidwa ya bwinja.
39 Јер вам кажем: Нећете мене видети одселе док не кажете: Благословљен који иде у име Господње.
Chifukwa chake ndikuwuza kuti simudzandionanso kufikira pamene mudzati, ‘Wodala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye.’”

< Матеј 23 >