< Јован 3 >

1 Беше пак човек међу фарисејима, по имену Никодим, кнез јеврејски.
Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda.
2 Овај дође к Исусу ноћу и рече Му: Рави! Знамо да си ти учитељ од Бога дошао; јер нико не може чудеса ових чинити која ти чиниш ако није Бог с њим.
Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.”
3 Одговори Исус и рече му: Заиста, заиста ти кажем: ако се ко наново не роди, не може видети царство Божије.
Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”
4 Рече Никодим Њему: Како се може човек родити кад је стар? Еда ли може по други пут ући у утробу матере своје и родити се?
Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?”
5 Одговори Исус: Заиста, заиста ти кажем: ако се ко не роди водом и Духом, не може ући у царство Божије.
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.
6 Шта је рођено од тела, тело је; а шта је рођено од Духа, дух је.
Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu.
7 Не чуди се што ти рекох; ваља вам се наново родити.
Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’
8 Дух дише где хоће, и глас његов чујеш, а не знаш откуда долази и куда иде; тако је сваки човек који је рођен од Духа.
Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”
9 Одговори Никодим и рече Му: Како може то бити?
Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?”
10 Исус одговори и рече му: Ти си учитељ Израиљев, и то ли не знаш?
Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi?
11 Заиста, заиста ти кажем да ми говоримо шта знамо, и сведочимо шта видесмо, и сведочанство наше не примате.
Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu.
12 Кад вам казах земаљско па не верујете, како ћете веровати ако вам кажем небеско?
Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba?
13 И нико се не попе на небо осим који сиђе с неба, Син човечији који је на небу.
Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu.
14 И као што Мојсије подиже змију у пустињи, тако треба Син човечији да се подигне.
Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa,
15 Да ниједан који Га верује не погине, него да има живот вечни: (aiōnios g166)
kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha. (aiōnios g166)
16 Јер Богу тако омиле свет да је и Сина свог Јединородног дао, да ниједан који Га верује не погине, него да има живот вечни. (aiōnios g166)
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. (aiōnios g166)
17 Јер Бог не посла Сина свог на свет да суди свету, него да се свет спасе кроза Њ.
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi.
18 Који Њега верује не суди му се, а који не верује већ је осуђен, јер не верова у име Јединородног Сина Божијег.
Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.
19 А суд је овај што видело дође на свет, и људима омиле већма тама неголи видело; јер њихова дела беху зла.
Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa.
20 Јер сваки који зло чини мрзи на на видело и не иде к виделу да не покарају дела његова, јер су зла.
Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere.
21 А ко истину чини иде к виделу, да се виде дела његова, јер су у Богу учињена.
Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”
22 А потом дође Исус и ученици Његови у јудејску земљу, и онде живљаше с њима и крштаваше.
Zitatha izi, Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼmadera a ku midzi ya ku Yudeya, kumene Iye anakhala kanthawi akubatiza.
23 А Јован крштаваше у Енону близу Салима, јер онде беше много воде; и долажаху те их крштаваше.
Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa.
24 Јер још не беше Јован бачен у тамницу.
(Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende).
25 Тада постаде распра међу ученицима Јовановим и Јеврејима око чишћења.
Mkangano unabuka pakati pa ophunzira ena a Yohane ndi Ayuda ena pa zamwambo wodziyeretsa wa Ayuda.
26 И дођоше к Јовану и рекоше му: Рави! Онај што беше с тобом преко Јордана, за кога си ти сведочио, ево он крштава, и сви иду к њему.
Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.”
27 Јован одговори и рече: Не може човек ништа примити ако му не буде дано с неба.
Atamva zimenezi, Yohane anayankha kuti, “Munthu amalandira chokhacho chapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba.
28 Ви сами мени сведочите да рекох: Ја нисам Христос, него сам послан пред Њим.
Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’
29 Ко има невесту женик је, а пријатељ жеников стоји и слуша га, и радошћу радује се гласу жениковом. Ова дакле радост моја испуни се.
Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri.
30 Онај треба да расте, а ја да се умањујем.
Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe.
31 Који одозго долази над свима је; који је са земље од земље је, и говори од земље; који долази с неба над свима је.
“Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse.
32 И шта виде и чу оно сведочи; и сведочанство Његово нико не прима.
Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake.
33 Који прими Његово сведочанство, потврди да је Бог истинит.
Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona.
34 Јер кога Бог посла, онај речи Божије говори: јер Бог Духа не даје на меру.
Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire.
35 Јер Отац љуби Сина, и све даде у руке Његове.
Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake.
36 Ко верује Сина, има живот вечни; а ко не верује Сина, неће видети живот, него гнев Божји остаје на њему. (aiōnios g166)
Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.” (aiōnios g166)

< Јован 3 >