< Књига пророка Јеремије 2 >

1 Опет ми дође реч Господња говорећи:
Yehova anandiwuza kuti,
2 Иди и вичи Јерусалиму да чује и говори: Овако вели Господ: Опомињем те се по милости у младости твојој и по љубави о веридби твојој, кад иђаше за мном по пустињи, и по земљи где се не сеје.
“Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti, “‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako, mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi, mmene unkanditsata mʼchipululu muja; mʼdziko losadzalamo kanthu.
3 Израиљ беше светиња Господу и првина од родова Његових; који је јеђаху сви беху криви, зло долажаше на њих, вели Господ.
Israeli anali wopatulika wa Yehova, anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola; onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa ndipo mavuto anawagwera,’” akutero Yehova.
4 Чујте реч Господњу, доме Јаковљев и све породице дома Израиљевог.
Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo, inu mafuko onse a Israeli.
5 Овако вели Господ: Какву неправду нађоше оци ваши у мене, те одступише од мене, и присташе за ништавилом, и посташе ништави?
Yehova akuti, “Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji, kuti andithawe? Iwo anatsata milungu yachabechabe, nawonso nʼkusanduka achabechabe.
6 И не рекоше: Где је Господ који нас је извео из земље мисирске, који нас је водио по пустињи, по земљи пустој и пуној пропасти, по земљи сувој и где је сен смртни, по земљи преко које нико није ходио и у којој нико није живео?
Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti, amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma ndi lokumbikakumbika, mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima, dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’
7 И кад вас доведох у земљу родну да једете род њен и добра њена, дошавши оскврнисте земљу моју и од наследства мог начинисте гад.
Ndinakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.
8 Свештеници не рекоше: Где је Господ? И који се баве законом не познаше ме, и пастири одусташе ме, и пророци пророковаше Валом и идоше за стварима залудним.
Ansembe nawonso sanafunse kuti, ‘Yehova ali kuti?’ Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe; atsogoleri anandiwukira. Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala, ndi kutsatira mafano achabechabe.
9 За то ћу се још прети с вама, вели Господ, и са синовима синова ваших прећу се.
“Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.
10 Јер прођите острва китимска и видите и пошљите у Кидар, и разгледајте добро, и видите, је ли било такво шта:
Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone, tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino; ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:
11 Је ли који народ променио богове, ако и нису богови? А мој народ промени славу своју на ствар залудну.
Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake? (Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe). Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemerero ndi mafano achabechabe.
12 Чудите се томе, небеса, и згрозите се и упропастите се! Вели Господ.
Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi, ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,” akutero Yehova.
13 Јер два зла учини мој народ: оставише мене, извор живе воде, и ископаше себи студенце, студенце испроваљиване, који не могу да држе воде.
“Popeza anthu anga achita machimo awiri: Andisiya Ine kasupe wa madzi a moyo, ndi kukadzikumbira zitsime zawo, zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.
14 Је ли Израиљ роб? Је ли роб у кући рођен? Зашто поста грабеж?
Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi. Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?
15 Рикаше на њ лавићи и дизаше глас свој, и обратише земљу његову у пустош; градови су му попаљени, те нема никога да живи у њима.
Adani ake abangulira ndi kumuopseza ngati mikango. Dziko lake analisandutsa bwinja; mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
16 И синови нофски и тафнески опасоше ти теме.
Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi akuphwanyani mitu.
17 Ниси ли то сам себи учинио оставивши Господа Бога свог кад те вођаше путем?
Zimenezitu zakuchitikirani chifukwa munasiya Yehova Mulungu wanu pamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?
18 А сада шта ће ти пут мисирски да пијеш воде сиорске? Шта ли ће ти пут асирски да пијеш воде из реке?
Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto, kukamwa madzi a mu Sihori? Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya, kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
19 Твоја ће те злоћа покарати и твоје ће те одметање прекорити. Познај дакле и види да је зло и горко што си оставио Господа Бога свог и што нема страха мог у теби, вели Господ Господ над војскама.
Kuyipa kwanuko kudzakulangani; kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani. Tsono ganizirani bwino, popeza ndi chinthu choyipa kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu; ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu. Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
20 Јер давно изломих јарам твој и раскидох свезе твоје, и ти рече: Нећу бити слуга; а на сваки високи хум и под свако зелено дрво идеш да се курваш.
“Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu ndi kudula msinga zanu; munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere. Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
21 Ја те посадих, лозу изабрану, све семе истинито; па како ми се промени и изметну се одвода од туђе лозе?
Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika; unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika. Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesa wachabechabe wonga wa kutchire?
22 Да се измијеш салитром и узмеш много сапуна, опет ће се познавати безакоње твоје преда мном, вели Господ Господ.
Ngakhale utasamba ndi soda kapena kusambira sopo wambiri, kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,” akutero Ambuye Yehova.
23 Како можеш рећи: Нисам се оскврнио, нисам ишао за Валима? Погледај пут свој по долу; познај шта си учинила, брза камило, која остављаш знаке на својим путевима.
“Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse; sindinatsatire Abaala’? Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja; zindikira bwino zomwe wachita. Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro yomangothamanga uku ndi uku,
24 Као дивља магарица, која је навикла на пустињу и по жељи душе своје вуче у се ветар, кад навали, ко ће је вратити? Који је траже неће се уморити, наћи ће је у месецу њеном.
wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu, yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika. Ndani angayiretse chilakolako chakecho? Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika. Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza.
25 Чувај ногу своју, да није боса, и грло своје, да не жедни. Али ти велиш: Од тога нема ништа; не, јер љубим туђе, и за њима ћу ићи.
Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu. Koma unati, ‘Zamkutu! Ine ndimakonda milungu yachilendo, ndipo ndidzayitsatira.’
26 Као што се лупеж посрами кад се ухвати, тако ће се посрамити дом Израиљев, они, цареви њихови, кнезови њихови, и свештеници њихови и пророци њихови,
“Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa, moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi; Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo, ansembe ndi aneneri awo.
27 Који говоре дрвету: Ти си отац мој; и камену: Ти си ме родио; јер ми окренуше леђа, а не лице; а кад су у невољи говоре: Устани и избави нас.
Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’ Iwo andifulatira Ine, ndipo safuna kundiyangʼana; Koma akakhala pa mavuto amati, ‘Bwerani mudzatipulumutse!’
28 А где су богови твоји које си начинио себи? Нека устану, ако те могу избавити кад си у невољи, јер имаш, Јуда, богова колико градова.
Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha? Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani pamene muli pamavuto! Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.
29 Зашто хоћете да се правдате са мном? Ви сте се сви одметнули од мене, вели Господ.
“Kodi mukundizengeranji mlandu? Nonse mwandiwukira,” akutero Yehova.
30 Узалуд бих синове ваше, не примише науке; мач ваш прождре пророке ваше као лав који дави.
“Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu; iwo sanaphunzirepo kanthu. Monga mkango wolusa, lupanga lanu lapha aneneri anu.
31 О роде! Видите реч Господњу; бејах ли пустиња Израиљу или мрачна земља? Зашто говори мој народ: Господари смо, нећемо више доћи к теби?
“Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova: “Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda; sitidzabweranso kwa Inu’?
32 Заборавља ли девојка свој накит и невеста урес свој? А народ мој заборави ме толико дана да им нема броја.
Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake, kapena kuyiwala zovala zake za ukwati? Komatu anthu anga andiyiwala masiku osawerengeka.
33 Зашто говориш да је добар твој пут тражећи шта љубиш? Па си и неваљале жене научио својим путевима.
Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi! Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu.
34 И још на скутовима твојим налази се крв сиромаха правих; не налазим копајући, него је на свима њима.
Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo magazi a anthu osauka osalakwa. Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba. Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,
35 А ти говориш: Нисам крив, гнев се Његов одвратио од мене. Ево ја ћу се прети с тобом што говориш: Нисам згрешио.
inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa, sadzatikwiyira.’ Ndidzakuyimbani mlandu chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’
36 Зашто трчкаш тако мењајући свој пут? Посрамићеш се од Мисирца како си се посрамио од Асирца.
Chifukwa chiyani mukunkabe nimusinthasintha njira zanu? Aigupto adzakukhumudwitsani monga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi.
37 Отићи ћеш и одатле с рукама над главом својом, јер Господ одбацује узданице твоје, и нећеш бити срећан у њима.
Mudzachokanso kumeneko manja ali kunkhongo. Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira, choncho sadzakuthandizani konse.

< Књига пророка Јеремије 2 >