< 2 Мојсијева 35 >
1 Потом сабра Мојсије сав збор синова Израиљевих, и рече им: Ово је заповедио Господ да чините:
Mose anasonkhanitsa gulu lonse la Aisraeli ndipo anawawuza kuti, “Zinthu zimene Yehova wakulamulirani kuti muzichite ndi izi:
2 Шест дана да се ради, а седми да вам је свет, субота почивања Господњег; ко би радио у тај дан, да се погуби.
Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa.
3 Ватре не ложите по становима својим у дан суботни.
Pa tsiku la Sabata musakoleze moto paliponse pamene mukhala.”
4 Још рече Мојсије свему збору синова Израиљевих говорећи: Ово је заповедио Господ и рекао:
Mose ananena kwa gulu lonse la Aisraeli kuti, “Zimene Yehova wakulamulirani ndi izi:
5 Скупите између себе прилог Господу; ко год хоће драге воље, нека донесе прилог Господу: злато и сребро и бронзу,
Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa;
6 И порфиру и скерлет и црвац и танко платно и кострет,
nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi;
7 И коже овнујске црвене обојене и коже јазавичије и дрво ситим,
zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha,
8 И уље за видело, и мирисе за уље помазања и за кад мирисни,
mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira;
9 И камење онихово, и камење за укивање по оплећку и по напрснику.
miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa Efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.
10 И који су год вешти међу вама нека дођу да раде шта је заповедио Господ:
“Anthu onse aluso pakati panu abwere ndi kupanga zonse zimene Yehova walamula:
11 Шатор, и наслон његов, и покривач његов, и куке његове, и даске његове, преворнице његове, ступове његове и стопице његове,
Chihema ndi tenti yake ndiponso chophimba chake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake;
12 Ковчег, и полуге његове, и заклопац, и завес,
Bokosi la Chipangano pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake cha bokosilo ndi nsalu zophimba bokosilo;
13 Сто, и полуге његове и све справе његове, и хлеб за постављање,
tebulo pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira pamodzi ndi zipangizo zake zonse ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova;
14 И свећњак за видело са справама његовим, и жишке његове, и уље за видело,
choyikapo nyale yowunikira pamodzi ndi zipangizo zake, nyale ndi mafuta anyalezo;
15 И олтар кадиони, и полуге његове, и уље помазања, и кад мирисни, и завес на врата од шатора,
guwa lofukizira lubani pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi lubani onunkhira; nsalu yotchinga pa khomo lolowera mʼchihema;
16 Олтар за жртву паљеницу, и решетку његову од бронзе, полуге његове и све справе његове, умиваоницу и подножје њено,
guwa lansembe yopsereza pamodzi ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni losambira lamkuwa ndi miyendo yake;
17 Завесе за трем, ступове његове и стопице његове, и завес на врата од трема,
nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake, ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo;
18 Коље за шатор, и коље за трем с ужима њиховим.
zikhomo za tenti ya chihema ndiponso za bwalo, ndi zingwe zake;
19 Хаљине службене за службу у светињи, и хаљине свете Арону свештенику, и хаљине синовима његовим за службу свештеничку.
zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.”
20 Тада отиде сав збор синова Израиљевих од Мојсија;
Kenaka gulu lonse la Aisraeli linachoka pamaso pa Mose,
21 И вратише се, сваки ког подиже срце његово и кога год дух покрете драговољно, и донесоше прилог Господу за грађење шатора од састанка и за сву службу у њему и за хаљине свете.
ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika.
22 Долазише људи и жене, ко год беше драговољног срца, и доносише споне и обоце и прстење и наруквице и свакојаке наките златне; и сваки донесе прилог злата Господу.
Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
23 Ко год имаше порфире, скерлета, црвца, танког платна, кострети, кожа овнујских црвених обојених и кожа јазавичијих, сваки доношаше.
Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa.
24 И ко год прилагаше сребро или бронзу, доношаше у прилог Господу; и у кога год беше дрвета ситима, за сваку употребу у служби доношаше.
Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa.
25 И све жене веште предоше својим рукама, и доносише шта напредоше за порфиру, скерлет, црвац и танко платно.
Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala.
26 И све жене које подиже срце њихово и беху веште, предоше кострет.
Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi.
27 А главари доносише камење онихово и камење за укивање по оплећку и по напрснику,
Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa.
28 И мирисе и уље за видело и уље за помазање и за кад мирисни.
Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira.
29 Сви људи и жене, које подиже драговољно срце да доносе шта треба за све дело које Господ заповеди преко Мојсија да се начини, донесоше синови Израиљеви драговољни прилог Господу.
Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite.
30 Тада рече Мојсије синовима Израиљевим: Видите, Господ позва по имену Веселеила сина Урије сина Оровог од племена Јудиног,
Kenaka Mose anati kwa Aisraeli, “Taonani, Yehova wasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda,
31 И напуни га духа Божијег, мудрости, разума и знања и вештине за сваки посао,
ndipo wamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi:
32 Да вешто измишља како се шта ради од злата и сребра и од бронзе,
Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,
33 Да уме резати камење и укивати, да уме тесати дрво и радити сваки посао врло вешто.
kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja.
34 И даде му у срце, њему и Елијаву сину Ахисамаховом од племена Дановог, да могу учити друге.
Ndipo Iye wapereka kwa Bezaleli pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani luso lophunzitsa ena.
35 Напуни их вештине да раде сваки посао, да кују, тешу, везу, и ткају порфиру, скерлет, црвац и танко платно, и да раде свакојаке послове вешто измишљајући.
Mulungu wawapatsa maluso osiyanasiyana, maluso ogoba, olemba ndondomeko, opeta zokometsera pa nsalu zamtundu wamtambo, zapepo ndi zofiira ndiponso zofewa zosalala ndi zoluka. Onsewa ndi amisiri a ntchito zamanja ndi zokonza ndondomeko.