< ပြကာၑိတံ 4 >
1 တတး ပရံ မယာ ဒၖၐ္ဋိပါတံ ကၖတွာ သွရ္ဂေ မုက္တံ ဒွါရမ် ဧကံ ဒၖၐ္ဋံ မယာ သဟဘာၐမာဏသျ စ ယသျ တူရီဝါဒျတုလျော ရဝး ပူရွွံ ၑြုတး သ မာမ် အဝေါစတ် သ္ထာနမေတဒ် အာရောဟယ, ဣတး ပရံ ယေန ယေန ဘဝိတဝျံ တဒဟံ တွာံ ဒရ္ၑယိၐျေ၊
Kenaka, nditayangʼana patsogolo panga ndinaona khomo lotsekuka la kumwamba. Ndipo liwu lija ndinalimva poyamba lokhala ngati lipenga linati, “Bwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene zichitike zikatha izi.”
2 တေနာဟံ တတ္က္ၐဏာဒ် အာတ္မာဝိၐ္ဋော ဘူတွာ 'ပၑျံ သွရ္ဂေ သိံဟာသနမေကံ သ္ထာပိတံ တတြ သိံဟာသနေ ဧကော ဇန ဥပဝိၐ္ဋော 'သ္တိ၊
Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo.
3 သိံဟာသနေ ဥပဝိၐ္ဋသျ တသျ ဇနသျ ရူပံ သူရျျကာန္တမဏေး ပြဝါလသျ စ တုလျံ တတ် သိံဟာသနဉ္စ မရကတမဏိဝဒြူပဝိၑိၐ္ဋေန မေဃဓနုၐာ ဝေၐ္ဋိတံ၊
Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo.
4 တသျ သိံဟာသနေ စတုရ္ဒိက္ၐု စတုရွိံၑတိသိံဟာသနာနိ တိၐ္ဌန္တိ တေၐု သိံဟာသနေၐု စတုရွိံၑတိ ပြာစီနလောကာ ဥပဝိၐ္ဋာသ္တေ ၑုဘြဝါသးပရိဟိတာသ္တေၐာံ ၑိရာံသိ စ သုဝရ္ဏကိရီဋဲ ရ္ဘူၐိတာနိ၊
Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu.
5 တသျ သိံဟာသနသျ မဓျာတ် တဍိတော ရဝါး သ္တနိတာနိ စ နိရ္ဂစ္ဆန္တိ သိံဟာသနသျာန္တိကေ စ သပ္တ ဒီပါ ဇွလန္တိ တ ဤၑွရသျ သပ္တာတ္မာနး၊
Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu.
6 အပရံ သိံဟာသနသျာန္တိကေ သ္ဖဋိကတုလျး ကာစမယော ဇလာၑယော ဝိဒျတေ, အပရမ် အဂြတး ပၑ္စာစ္စ ဗဟုစက္ၐုၐ္မန္တၑ္စတွာရး ပြာဏိနး သိံဟသနသျ မဓျေ စတုရ္ဒိက္ၐု စ ဝိဒျန္တေ၊
Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo. Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.
7 တေၐာံ ပြထမး ပြာဏီ သိံဟာကာရော ဒွိတီယး ပြာဏီ ဂေါဝါတ္သာကာရသ္တၖတီယး ပြာဏီ မနုၐျဝဒွဒနဝိၑိၐ္ဋၑ္စတုရ္ထၑ္စ ပြာဏီ ဥဍ္ဍီယမာနကုရရောပမး၊
Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka.
8 တေၐာံ စတုရ္ဏာမ် ဧကဲကသျ ပြာဏိနး ၐဋ် ပက္ၐား သန္တိ တေ စ သရွွာင်္ဂေၐွဘျန္တရေ စ ဗဟုစက္ၐုရွိၑိၐ္ဋား, တေ ဒိဝါနိၑံ န ဝိၑြာမျ ဂဒန္တိ ပဝိတြး ပဝိတြး ပဝိတြး သရွွၑက္တိမာန် ဝရ္တ္တမာနော ဘူတော ဘဝိၐျံၑ္စ ပြဘုး ပရမေၑွရး၊
Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti,
9 ဣတ္ထံ တဲး ပြာဏိဘိသ္တသျာနန္တဇီဝိနး သိံဟာသနောပဝိၐ္ဋသျ ဇနသျ ပြဘာဝေ ဂေါ်ရဝေ ဓနျဝါဒေ စ ပြကီရ္တ္တိတေ (aiōn )
Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. (aiōn )
10 တေ စတုရွိံၑတိပြာစီနာ အပိ တသျ သိံဟာသနောပဝိၐ္ဋသျာန္တိကေ ပြဏိနတျ တမ် အနန္တဇီဝိနံ ပြဏမန္တိ သွီယကိရီဋာံၑ္စ သိံဟာသနသျာန္တိကေ နိက္ၐိပျ ဝဒန္တိ, (aiōn )
Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati: (aiōn )
11 ဟေ ပြဘော ဤၑွရာသ္မာကံ ပြဘာဝံ ဂေါ်ရဝံ ဗလံ၊ တွမေဝါရှသိ သမ္ပြာပ္တုံ ယတ် သရွွံ သသၖဇေ တွယာ၊ တဝါဘိလာၐတၑ္စဲဝ သရွွံ သမ္ဘူယ နိရ္မ္မမေ။
“Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”