< လူကး 24 >

1 အထ သပ္တာဟပြထမဒိနေ'တိပြတျူၐေ တာ ယောၐိတး သမ္ပာဒိတံ သုဂန္ဓိဒြဝျံ ဂၖဟီတွာ တဒနျာဘိး ကိယတီဘိး သ္တြီဘိး သဟ ၑ္မၑာနံ ယယုး၊
Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda.
2 ကိန္တု ၑ္မၑာနဒွါရာတ် ပါၐာဏမပသာရိတံ ဒၖၐ္ဋွာ
Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika
3 တား ပြဝိၑျ ပြဘော ရ္ဒေဟမပြာပျ
ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu.
4 ဝျာကုလာ ဘဝန္တိ ဧတရှိ တေဇောမယဝသ္တြာနွိတော် ဒွေါ် ပုရုၐော် တာသာံ သမီပေ သမုပသ္ထိတော်
Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo.
5 တသ္မာတ္တား ၑင်္ကာယုက္တာ ဘူမာဝဓောမုချသျသ္ထုး၊ တဒါ တော် တာ ဦစတု ရ္မၖတာနာံ မဓျေ ဇီဝန္တံ ကုတော မၖဂယထ?
Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa?
6 သောတြ နာသ္တိ သ ဥဒသ္ထာတ်၊
Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya:
7 ပါပိနာံ ကရေၐု သမရ္ပိတေန ကြုၑေ ဟတေန စ မနုၐျပုတြေဏ တၖတီယဒိဝသေ ၑ္မၑာနာဒုတ္ထာတဝျမ် ဣတိ ကထာံ သ ဂလီလိ တိၐ္ဌန် ယုၐ္မဘျံ ကထိတဝါန် တာံ သ္မရတ၊
‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’”
8 တဒါ တသျ သာ ကထာ တာသာံ မနးသု ဇာတာ၊
Ndipo anakumbukira mawu ake.
9 အနန္တရံ ၑ္မၑာနာဒ် ဂတွာ တာ ဧကာဒၑၑိၐျာဒိဘျး သရွွေဘျသ္တာံ ဝါရ္တ္တာံ ကထယာမာသုး၊
Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse.
10 မဂ္ဒလီနီမရိယမ်, ယောဟနာ, ယာကူဗော မာတာ မရိယမ် တဒနျား သင်္ဂိနျော ယောၐိတၑ္စ ပြေရိတေဘျ ဧတား သရွွာ ဝါရ္တ္တား ကထယာမာသုး
Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi.
11 ကိန္တု တာသာံ ကထာမ် အနရ္ထကာချာနမာတြံ ဗုဒ္ဓွာ ကောပိ န ပြတျဲတ်၊
Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru.
12 တဒါ ပိတရ ဥတ္ထာယ ၑ္မၑာနာန္တိကံ ဒဓာဝ, တတြ စ ပြဟွော ဘူတွာ ပါရ္ၑွဲကသ္ထာပိတံ ကေဝလံ ဝသ္တြံ ဒဒရ္ၑ; တသ္မာဒါၑ္စရျျံ မနျမာနော ယဒဃဋတ တန္မနသိ ဝိစာရယန် ပြတသ္ထေ၊
Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
13 တသ္မိန္နေဝ ဒိနေ ဒွေါ် ၑိယျော် ယိရူၑာလမၑ္စတုၐ္ကြောၑာန္တရိတမ် ဣမ္မာယုဂြာမံ ဂစ္ဆန္တော်
Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu.
14 တာသာံ ဃဋနာနာံ ကထာမကထယတာံ
Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo.
15 တယောရာလာပဝိစာရယေား ကာလေ ယီၑုရာဂတျ တာဘျာံ သဟ ဇဂါမ
Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi;
16 ကိန္တု ယထာ တော် တံ န ပရိစိနုတသ္တဒရ္ထံ တယော ရ္ဒၖၐ္ဋိး သံရုဒ္ဓါ၊
koma iwo sanamuzindikire.
17 သ တော် ပၖၐ္ဋဝါန် ယုဝါံ ဝိၐဏ္ဏော် ကိံ ဝိစာရယန္တော် ဂစ္ဆထး?
Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?” Iwo anayima ndi nkhope zakugwa.
18 တတသ္တယေား က္လိယပါနာမာ ပြတျုဝါစ ယိရူၑာလမပုရေ'ဓုနာ ယာနျဃဋန္တ တွံ ကေဝလဝိဒေၑီ ကိံ တဒွၖတ္တာန္တံ န ဇာနာသိ?
Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?”
19 သ ပပြစ္ဆ ကာ ဃဋနား? တဒါ တော် ဝက္တုမာရေဘာတေ ယီၑုနာမာ ယော နာသရတီယော ဘဝိၐျဒွါဒီ ဤၑွရသျ မာနုၐာဏာဉ္စ သာက္ၐာတ် ဝါကျေ ကရ္မ္မဏိ စ ၑက္တိမာနာသီတ္
Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?” Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
20 တမ် အသ္မာကံ ပြဓာနယာဇကာ ဝိစာရကာၑ္စ ကေနာပိ ပြကာရေဏ ကြုၑေ ဝိဒ္ဓွာ တသျ ပြာဏာနနာၑယန် တဒီယာ ဃဋနား;
Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye;
21 ကိန္တု ယ ဣသြာယေလီယလောကာန် ဥဒ္ဓါရယိၐျတိ သ ဧဝါယမ် ဣတျာၑာသ္မာဘိး ကၖတာ၊ တဒျထာ တထာသ္တု တသျာ ဃဋနာယာ အဒျ ဒိနတြယံ ဂတံ၊
koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi.
22 အဓိကန္တွသ္မာကံ သင်္ဂိနီနာံ ကိယတ္သ္တြီဏာံ မုခေဘျော'သမ္ဘဝဝါကျမိဒံ ၑြုတံ;
Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa
23 တား ပြတျူၐေ ၑ္မၑာနံ ဂတွာ တတြ တသျ ဒေဟမ် အပြာပျ ဝျာဃုဋျေတွာ ပြောက္တဝတျး သွရ္ဂီသဒူတော် ဒၖၐ္ဋာဝသ္မာဘိသ္တော် စာဝါဒိၐ္ဋာံ သ ဇီဝိတဝါန်၊
koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo.
24 တတောသ္မာကံ ကဲၑ္စိတ် ၑ္မၑာနမဂမျတ တေ'ပိ သ္တြီဏာံ ဝါကျာနုရူပံ ဒၖၐ္ဋဝန္တး ကိန္တု တံ နာပၑျန်၊
Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.”
25 တဒါ သ တာဝုဝါစ, ဟေ အဗောဓော် ဟေ ဘဝိၐျဒွါဒိဘိရုက္တဝါကျံ ပြတျေတုံ ဝိလမ္ဗမာနော်;
Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena!
26 ဧတတ္သရွွဒုးခံ ဘုက္တွာ သွဘူတိပြာပ္တိး ကိံ ခြီၐ္ဋသျ န နျာယျာ?
Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?”
27 တတး သ မူသာဂြန္ထမာရဘျ သရွွဘဝိၐျဒွါဒိနာံ သရွွၑာသ္တြေ သွသ္မိန် လိခိတာချာနာဘိပြာယံ ဗောဓယာမာသ၊
Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
28 အထ ဂမျဂြာမာဘျရ္ဏံ ပြာပျ တေနာဂြေ ဂမနလက္ၐဏေ ဒရ္ၑိတေ
Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira.
29 တော် သာဓယိတွာဝဒတာံ သဟာဝါဘျာံ တိၐ္ဌ ဒိနေ ဂတေ သတိ ရာတြိရဘူတ်; တတး သ တာဘျာံ သာရ္ဒ္ဓံ သ္ထာတုံ ဂၖဟံ ယယော်၊
Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
30 ပၑ္စာဒ္ဘေါဇနောပဝေၑကာလေ သ ပူပံ ဂၖဟီတွာ ဤၑွရဂုဏာန် ဇဂါဒ တဉ္စ ဘံက္တွာ တာဘျာံ ဒဒေါ်၊
Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira.
31 တဒါ တယော ရ္ဒၖၐ္ဋော် ပြသန္နာယာံ တံ ပြတျဘိဇ္ဉတုး ကိန္တု သ တယေား သာက္ၐာဒန္တရ္ဒဓေ၊
Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo.
32 တတသ္တော် မိထောဘိဓာတုမ် အာရဗ္ဓဝန္တော် ဂမနကာလေ ယဒါ ကထာမကထယတ် ၑာသ္တြာရ္ထဉ္စဗောဓယတ် တဒါဝယော ရ္ဗုဒ္ဓိး ကိံ န ပြာဇွလတ်?
Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”
33 တော် တတ္က္ၐဏာဒုတ္ထာယ ယိရူၑာလမပုရံ ပြတျာယယတုး, တတ္သ္ထာနေ ၑိၐျာဏာမ် ဧကာဒၑာနာံ သင်္ဂိနာဉ္စ ဒရ္ၑနံ ဇာတံ၊
Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi
34 တေ ပြောစုး ပြဘုရုဒတိၐ္ဌဒ် ဣတိ သတျံ ၑိမောနေ ဒရ္ၑနမဒါစ္စ၊
ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.”
35 တတး ပထး သရွွဃဋနာယား ပူပဘဉ္ဇနေန တတ္ပရိစယသျ စ သရွွဝၖတ္တာန္တံ တော် ဝက္တုမာရေဘာတေ၊
Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.
36 ဣတ္ထံ တေ ပရသ္ပရံ ဝဒန္တိ တတ္ကာလေ ယီၑုး သွယံ တေၐာံ မဓျ ပြောတ္ထယ ယုၐ္မာကံ ကလျာဏံ ဘူယာဒ် ဣတျုဝါစ,
Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.”
37 ကိန္တု ဘူတံ ပၑျာမ ဣတျနုမာယ တေ သမုဒွိဝိဇိရေ တြေၐုၑ္စ၊
Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa.
38 သ ဥဝါစ, ကုတော ဒုးခိတာ ဘဝထ? ယုၐ္မာကံ မနးသု သန္ဒေဟ ဥဒေတိ စ ကုတး?
Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu?
39 ဧၐောဟံ, မမ ကရော် ပၑျတ ဝရံ သ္ပၖၐ္ဋွာ ပၑျတ, မမ ယာဒၖၑာနိ ပၑျထ တာဒၖၑာနိ ဘူတသျ မာံသာသ္ထီနိ န သန္တိ၊
Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”
40 ဣတျုက္တွာ သ ဟသ္တပါဒါန် ဒရ္ၑယာမာသ၊
Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake.
41 တေ'သမ္ဘဝံ ဇ္ဉာတွာ သာနန္ဒာ န ပြတျယန်၊ တတး သ တာန် ပပြစ္ဆ, အတြ ယုၐ္မာကံ သမီပေ ခါဒျံ ကိဉ္စိဒသ္တိ?
Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”
42 တတသ္တေ ကိယဒ္ဒဂ္ဓမတ္သျံ မဓု စ ဒဒုး
Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika.
43 သ တဒါဒါယ တေၐာံ သာက္ၐာဒ် ဗုဘုဇေ
Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.
44 ကထယာမာသ စ မူသာဝျဝသ္ထာယာံ ဘဝိၐျဒွါဒိနာံ ဂြန္ထေၐု ဂီတပုသ္တကေ စ မယိ ယာနိ သရွွာဏိ ဝစနာနိ လိခိတာနိ တဒနုရူပါဏိ ဃဋိၐျန္တေ ယုၐ္မာဘိး သာရ္ဒ္ဓံ သ္ထိတွာဟံ ယဒေတဒွါကျမ် အဝဒံ တဒိဒါနီံ ပြတျက္ၐမဘူတ်၊
Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”
45 အထ တေဘျး ၑာသ္တြဗောဓာဓိကာရံ ဒတွာဝဒတ်,
Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba.
46 ခြီၐ္ဋေနေတ္ထံ မၖတိယာတနာ ဘောက္တဝျာ တၖတီယဒိနေ စ ၑ္မၑာနာဒုတ္ထာတဝျဉ္စေတိ လိပိရသ္တိ;
Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu.
47 တန္နာမ္နာ ယိရူၑာလမမာရဘျ သရွွဒေၑေ မနးပရာဝရ္တ္တနသျ ပါပမောစနသျ စ သုသံဝါဒး ပြစာရယိတဝျး,
Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.
48 ဧၐု သရွွေၐု ယူယံ သာက္ၐိဏး၊
Inu ndinu mboni za zimenezi.
49 အပရဉ္စ ပၑျတ ပိတြာ ယတ် ပြတိဇ္ဉာတံ တတ် ပြေၐယိၐျာမိ, အတဧဝ ယာဝတ္ကာလံ ယူယံ သွရ္ဂီယာံ ၑက္တိံ န ပြာပ္သျထ တာဝတ္ကာလံ ယိရူၑာလမ္နဂရေ တိၐ္ဌတ၊
Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”
50 အထ သ တာန် ဗဲထနီယာပရျျန္တံ နီတွာ ဟသ္တာဝုတ္တောလျ အာၑိၐ ဝက္တုမာရေဘေ
Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa.
51 အာၑိၐံ ဝဒန္နေဝ စ တေဘျး ပၖထဂ် ဘူတွာ သွရ္ဂာယ နီတော'ဘဝတ်၊
Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba.
52 တဒါ တေ တံ ဘဇမာနာ မဟာနန္ဒေန ယိရူၑာလမံ ပြတျာဇဂ္မုး၊
Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.
53 တတော နိရန္တရံ မန္ဒိရေ တိၐ္ဌန္တ ဤၑွရသျ ပြၑံသာံ ဓနျဝါဒဉ္စ ကရ္တ္တမ် အာရေဘိရေ၊ ဣတိ။
Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.

< လူကး 24 >