< လူကး 23 >
1 တတး သဘာသ္ထား သရွွလောကာ ဥတ္ထာယ တံ ပီလာတသမ္မုခံ နီတွာပြောဒျ ဝက္တုမာရေဘိရေ,
Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato.
2 သွမဘိၐိက္တံ ရာဇာနံ ဝဒန္တံ ကဲမရရာဇာယ ကရဒါနံ နိၐေဓန္တံ ရာဇျဝိပရျျယံ ကုရ္တ္တုံ ပြဝရ္တ္တမာနမ် ဧန ပြာပ္တာ ဝယံ၊
Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
3 တဒါ ပီလာတသ္တံ ပၖၐ္ဋဝါန် တွံ ကိံ ယိဟူဒီယာနာံ ရာဇာ? သ ပြတျုဝါစ တွံ သတျမုက္တဝါန်၊
Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
4 တဒါ ပီလာတး ပြဓာနယာဇကာဒိလောကာန် ဇဂါဒ်, အဟမေတသျ ကမပျပရာဓံ နာပ္တဝါန်၊
Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”
5 တတသ္တေ ပုနး သာဟမိနော ဘူတွာဝဒန်, ဧၐ ဂါလီလ ဧတတ္သ္ထာနပရျျန္တေ သရွွသ္မိန် ယိဟူဒါဒေၑေ သရွွာလ္လောကာနုပဒိၑျ ကုပြဝၖတ္တိံ ဂြာဟီတဝါန်၊
Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”
6 တဒါ ပီလာတော ဂါလီလပြဒေၑသျ နာမ ၑြုတွာ ပပြစ္ဆ, ကိမယံ ဂါလီလီယော လောကး?
Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya.
7 တတး သ ဂါလီလ္ပြဒေၑီယဟေရောဒြာဇသျ တဒါ သ္ထိတေသ္တသျ သမီပေ ယီၑုံ ပြေၐယာမာသ၊
Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.
8 တဒါ ဟေရောဒ် ယီၑုံ ဝိလောကျ သန္တုတောၐ, ယတး သ တသျ ဗဟုဝၖတ္တာန္တၑြဝဏာတ် တသျ ကိဉိစဒါၑ္စရျျကရ္မ္မ ပၑျတိ ဣတျာၑာံ ကၖတွာ ဗဟုကာလမာရဘျ တံ ဒြၐ္ဋုံ ပြယာသံ ကၖတဝါန်၊
Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa.
9 တသ္မာတ် တံ ဗဟုကထား ပပြစ္ဆ ကိန္တု သ တသျ ကသျာပိ ဝါကျသျ ပြတျုတ္တရံ နောဝါစ၊
Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe.
10 အထ ပြဓာနယာဇကာ အဓျာပကာၑ္စ ပြောတ္တိၐ္ဌန္တး သာဟသေန တမပဝဒိတုံ ပြာရေဘိရေ၊
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri.
11 ဟေရောဒ် တသျ သေနာဂဏၑ္စ တမဝဇ္ဉာယ ဥပဟာသတွေန ရာဇဝသ္တြံ ပရိဓာပျ ပုနး ပီလာတံ ပြတိ တံ ပြာဟိဏောတ်၊
Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato.
12 ပူရွွံ ဟေရောဒ္ပီလာတယေား ပရသ္ပရံ ဝဲရဘာဝ အာသီတ် ကိန္တု တဒ္ဒိနေ ဒွယော ရ္မေလနံ ဇာတမ်၊
Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.
13 ပၑ္စာတ် ပီလာတး ပြဓာနယာဇကာန် ၑာသကာန် လောကာံၑ္စ ယုဂပဒါဟူယ ဗဘာၐေ,
Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu,
14 ရာဇျဝိပရျျယကာရကောယမ် ဣတျုက္တွာ မနုၐျမေနံ မမ နိကဋမာနဲၐ္ဋ ကိန္တု ပၑျတ ယုၐ္မာကံ သမက္ၐမ် အသျ ဝိစာရံ ကၖတွာပိ ပြောက္တာပဝါဒါနုရူပေဏာသျ ကောပျပရာဓး သပြမာဏော န ဇာတး,
ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu.
15 ယူယဉ္စ ဟေရောဒး သန္နိဓော် ပြေၐိတာ မယာ တတြာသျ ကောပျပရာဓသ္တေနာပိ န ပြာပ္တး၊ ပၑျတာနေန ဝဓဟေတုကံ ကိမပိ နာပရာဒ္ဓံ၊
Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe.
16 တသ္မာဒေနံ တာဍယိတွာ ဝိဟာသျာမိ၊
Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.”
17 တတြောတ္သဝေ တေၐာမေကော မောစယိတဝျး၊
(Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).
18 ဣတိ ဟေတောသ္တေ ပြောစ္စဲရေကဒါ ပြောစုး, ဧနံ ဒူရီကၖတျ ဗရဗ္ဗာနာမာနံ မောစယ၊
Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!”
19 သ ဗရဗ္ဗာ နဂရ ဥပပ္လဝဝဓာပရာဓာဘျာံ ကာရာယာံ ဗဒ္ဓ အာသီတ်၊
(Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).
20 ကိန္တု ပီလာတော ယီၑုံ မောစယိတုံ ဝါဉ္ဆန် ပုနသ္တာနုဝါစ၊
Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo.
21 တထာပျေနံ ကြုၑေ ဝျဓ ကြုၑေ ဝျဓေတိ ဝဒန္တသ္တေ ရုရုဝုး၊
Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22 တတး သ တၖတီယဝါရံ ဇဂါဒ ကုတး? သ ကိံ ကရ္မ္မ ကၖတဝါန်? နာဟမသျ ကမပိ ဝဓာပရာဓံ ပြာပ္တး ကေဝလံ တာဍယိတွာမုံ တျဇာမိ၊
Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
23 တထာပိ တေ ပုနရေနံ ကြုၑေ ဝျဓ ဣတျုက္တွာ ပြောစ္စဲရ္ဒၖဎံ ပြာရ္ထယာဉ္စကြိရေ;
Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira.
24 တတး ပြဓာနယာဇကာဒီနာံ ကလရဝေ ပြဗလေ သတိ တေၐာံ ပြာရ္ထနာရူပံ ကရ္တ္တုံ ပီလာတ အာဒိဒေၑ၊
Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo.
25 ရာဇဒြောဟဝဓယောရပရာဓေန ကာရာသ္ထံ ယံ ဇနံ တေ ယယာစိရေ တံ မောစယိတွာ ယီၑုံ တေၐာမိစ္ဆာယာံ သမာရ္ပယတ်၊
Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.
26 အထ တေ ယီၑုံ ဂၖဟီတွာ ယာန္တိ, ဧတရှိ ဂြာမာဒါဂတံ ၑိမောနနာမာနံ ကုရီဏီယံ ဇနံ ဓၖတွာ ယီၑေား ပၑ္စာန္နေတုံ တသျ သ္ကန္ဓေ ကြုၑမရ္ပယာမာသုး၊
Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu.
27 တတော လောကာရဏျမဓျေ ဗဟုသ္တြိယော ရုဒတျော ဝိလပန္တျၑ္စ ယီၑေား ပၑ္စာဒ် ယယုး၊
Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira.
28 ကိန္တု သ ဝျာဃုဋျ တာ ဥဝါစ, ဟေ ယိရူၑာလမော နာရျျော ယုယံ မဒရ္ထံ န ရုဒိတွာ သွာရ္ထံ သွာပတျာရ္ထဉ္စ ရုဒိတိ;
Yesu anatembenuka nati kwa iwo, “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu.
29 ပၑျတ ယး ကဒါပိ ဂရ္ဘဝတျော နာဘဝန် သ္တနျဉ္စ နာပါယယန် တာဒၖၑီ ရွန္ဓျာ ယဒါ ဓနျာ ဝက္ၐျန္တိ သ ကာလ အာယာတိ၊
Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’
30 တဒါ ဟေ ၑဲလာ အသ္မာကမုပရိ ပတတ, ဟေ ဥပၑဲလာ အသ္မာနာစ္ဆာဒယတ ကထာမီဒၖၑီံ လောကာ ဝက္ၐျန္တိ၊
Kenaka, “adzawuza mapiri kuti tigwereni ife; zitunda kuti tiphimbeni ife.
31 ယတး သတေဇသိ ၑာခိနိ စေဒေတဒ် ဃဋတေ တရှိ ၑုၐ္ကၑာခိနိ ကိံ န ဃဋိၐျတေ?
Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”
32 တဒါ တေ ဟန္တုံ ဒွါဝပရာဓိနော် တေန သာရ္ဒ္ဓံ နိနျုး၊
Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa.
33 အပရံ ၑိရးကပါလနာမကသ္ထာနံ ပြာပျ တံ ကြုၑေ ဝိဝိဓုး; တဒ္ဒွယောရပရာဓိနောရေကံ တသျ ဒက္ၐိဏော တဒနျံ ဝါမေ ကြုၑေ ဝိဝိဓုး၊
Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere.
34 တဒါ ယီၑုရကထယတ်, ဟေ ပိတရေတာန် က္ၐမသွ ယတ ဧတေ ယတ် ကရ္မ္မ ကုရွွန္တိ တန် န ဝိဒုး; ပၑ္စာတ္တေ ဂုဋိကာပါတံ ကၖတွာ တသျ ဝသ္တြာဏိ ဝိဘဇျ ဇဂၖဟုး၊
Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35 တတြ လောကသံဃသ္တိၐ္ဌန် ဒဒရ္ၑ; တေ တေၐာံ ၑာသကာၑ္စ တမုပဟသျ ဇဂဒုး, ဧၐ ဣတရာန် ရက္ၐိတဝါန် ယဒီၑွရေဏာဘိရုစိတော 'ဘိၐိက္တသ္တြာတာ ဘဝတိ တရှိ သွမဓုနာ ရက္ၐတု၊
Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
36 တဒနျး သေနာဂဏာ ဧတျ တသ္မဲ အမ္လရသံ ဒတွာ ပရိဟသျ ပြောဝါစ,
Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa,
37 စေတ္တွံ ယိဟူဒီယာနာံ ရာဇာသိ တရှိ သွံ ရက္ၐ၊
ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38 ယိဟူဒီယာနာံ ရာဇေတိ ဝါကျံ ယူနာနီယရောမီယေဗြီယာက္ၐရဲ ရ္လိခိတံ တစ္ဆိရသ ဦရ္ဒ္ဓွေ'သ္ထာပျတ၊
Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39 တဒေါဘယပါရ္ၑွယော ရွိဒ္ဓေါ် ယာဝပရာဓိနော် တယောရေကသ္တံ ဝိနိန္ဒျ ဗဘာၐေ, စေတ္တွမ် အဘိၐိက္တောသိ တရှိ သွမာဝါဉ္စ ရက္ၐ၊
Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”
40 ကိန္တွနျသ္တံ တရ္ဇယိတွာဝဒတ်, ဤၑွရာတ္တဝ ကိဉ္စိဒပိ ဘယံ နာသ္တိ ကိံ? တွမပိ သမာနဒဏ္ဍောသိ,
Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi?
41 ယောဂျပါတြေ အာဝါံ သွသွကရ္မ္မဏာံ သမုစိတဖလံ ပြာပ္နုဝး ကိန္တွနေန ကိမပိ နာပရာဒ္ဓံ၊
Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”
42 အထ သ ယီၑုံ ဇဂါဒ ဟေ ပြဘေ ဘဝါန် သွရာဇျပြဝေၑကာလေ မာံ သ္မရတု၊
Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”
43 တဒါ ယီၑုး ကထိတဝါန် တွာံ ယထာရ္ထံ ဝဒါမိ တွမဒျဲဝ မယာ သာရ္ဒ္ဓံ ပရလောကသျ သုခသ္ထာနံ ပြာပ္သျသိ၊
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”
44 အပရဉ္စ ဒွိတီယယာမာတ် တၖတီယယာမပရျျန္တံ ရဝေသ္တေဇသောန္တရှိတတွာတ် သရွွဒေၑော'န္ဓကာရေဏာဝၖတော
Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi,
45 မန္ဒိရသျ ယဝနိကာ စ ဆိဒျမာနာ ဒွိဓာ ဗဘူဝ၊
pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati.
46 တတော ယီၑုရုစ္စဲရုဝါစ, ဟေ ပိတ ရ္မမာတ္မာနံ တဝ ကရေ သမရ္ပယေ, ဣတျုက္တွာ သ ပြာဏာန် ဇဟော်၊
Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.
47 တဒဲတာ ဃဋနာ ဒၖၐ္ဋွာ ၑတသေနာပတိရီၑွရံ ဓနျမုက္တွာ ကထိတဝါန် အယံ နိတာန္တံ သာဓုမနုၐျ အာသီတ်၊
Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.”
48 အထ ယာဝန္တော လောကာ ဒြၐ္ဋုမ် အာဂတာသ္တေ တာ ဃဋနာ ဒၖၐ္ဋွာ ဝက္ၐးသု ကရာဃာတံ ကၖတွာ ဝျာစုဋျ ဂတား၊
Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka.
49 ယီၑော ရ္ဇ္ဉာတယော ယာ ယာ ယောၐိတၑ္စ ဂါလီလသ္တေန သာရ္ဒ္ဓမာယာတာသ္တာ အပိ ဒူရေ သ္ထိတွာ တတ် သရွွံ ဒဒၖၑုး၊
Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.
50 တဒါ ယိဟူဒီယာနာံ မန္တြဏာံ ကြိယာဉ္စာသမ္မနျမာန ဤၑွရသျ ရာဇတွမ် အပေက္ၐမာဏော
Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama.
51 ယိဟူဒိဒေၑီယော 'ရိမထီယနဂရီယော ယူၐဖ္နာမာ မန္တြီ ဘဒြော ဓာရ္မ္မိကၑ္စ ပုမာန္
Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu.
52 ပီလာတာန္တိကံ ဂတွာ ယီၑော ရ္ဒေဟံ ယယာစေ၊
Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu.
53 ပၑ္စာဒ် ဝပုရဝရောဟျ ဝါသသာ သံဝေၐ္ဋျ ယတြ ကောပိ မာနုၐော နာသ္ထာပျတ တသ္မိန် ၑဲလေ သွာတေ ၑ္မၑာနေ တဒသ္ထာပယတ်၊
Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo.
54 တဒ္ဒိနမာယောဇနီယံ ဒိနံ ဝိၑြာမဝါရၑ္စ သမီပး၊
Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.
55 အပရံ ယီၑုနာ သာရ္ဒ္ဓံ ဂါလီလ အာဂတာ ယောၐိတး ပၑ္စာဒိတွာ ၑ္မၑာနေ တတြ ယထာ ဝပုး သ္ထာပိတံ တစ္စ ဒၖၐ္ဋွာ
Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira.
56 ဝျာဃုဋျ သုဂန္ဓိဒြဝျတဲလာနိ ကၖတွာ ဝိဓိဝဒ် ဝိၑြာမဝါရေ ဝိၑြာမံ စကြုး၊
Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.