< Софония 3 >

1 Горе городу нечистому и оскверненному, притеснителю!
Tsoka kwa mzinda wa anthu opondereza, owukira ndi odetsedwa!
2 Не слушает голоса, не принимает наставления, на Господа не уповает, к Богу своему не приближается.
Sumvera aliyense, sulandira chidzudzulo. Sumadalira Yehova, suyandikira pafupi ndi Mulungu wake.
3 Князья его посреди него - рыкающие львы, судьи его - вечерние волки, не оставляющие до утра ни одной кости.
Akuluakulu ake ali ngati mikango yobuma, olamulira ake ndi olusa ngati mimbulu ya nthawi ya madzulo, zimene pofika mmawa sizisiya chilichonse.
4 Пророки его - люди легкомысленные, вероломные; священники его оскверняют святыню, попирают закон.
Aneneri ake ndi odzikuza; anthu achinyengo. Ansembe ake amadetsa malo opatulika ndipo amaphwanya lamulo.
5 Господь праведен посреди него, не делает неправды, каждое утро являет суд Свой неизменно; но беззаконник не знает стыда.
Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama; Iye salakwa. Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama, ndipo tsiku lililonse salephera, komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.
6 Я истребил народы, разрушены твердыни их; пустыми сделал улицы их, так что никто уже не ходит по ним; разорены города их: нет ни одного человека, нет жителей.
“Ndachotseratu mitundu ya anthu; ndagwetsa malinga awo. Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo, popanda aliyense wodutsa. Mizinda yawo yawonongedwa; palibe aliyense adzatsalemo.
7 Я говорил: “бойся только Меня, принимай наставление!”, и не будет истреблено жилище его, и не постигнет его зло, какое Я постановил о нем; а они прилежно старались портить все свои действия.
Ndinati, ‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa ndi kumvera kudzudzula kwanga!’ Ndipo sindidzawononga nyumba zawo, kapena kuwalanganso. Koma iwo anali okonzeka kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.
8 Итак, ждите Меня, говорит Господь, до того дня, когда Я восстану для опустошения, ибо Мною определено собрать народы, созвать царства, чтобы излить на них негодование Мое, всю ярость гнева Моего; ибо огнем ревности Моей пожрана будет вся земля.
Choncho mundidikire,” akutero Yehova, “chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni. Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu, kusonkhanitsa maufumu ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo; mkwiyo wanga wonse woopsa. Dziko lonse lidzatenthedwa ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.
9 Тогда опять Я дам народам уста чистые, чтобы все призывали имя Господа и служили Ему единодушно.
“Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova ndi kumutumikira Iye pamodzi.
10 Из заречных стран Ефиопии поклонники Мои, дети рассеянных Моих, принесут Мне дары.
Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi anthu anga ondipembedza, omwazikana, adzandibweretsera zopereka.
11 В тот день ты не будешь срамить себя всякими поступками твоими, какими ты грешил против Меня, ибо тогда Я удалю из среды твоей тщеславящихся твоею знатностью, и не будешь более превозноситься на святой горе Моей.
Tsiku limenelo simudzachita manyazi chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira, popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo. Simudzakhalanso odzikuza mʼphiri langa lopatulika.
12 Но оставлю среди тебя народ смиренный и простой, и они будут уповать на имя Господне.
Koma ndidzasiya pakati panu anthu ofatsa ndi odzichepetsa, amene amadalira dzina la Yehova.
13 Остатки Израиля не будут делать неправды, не станут говорить лжи, и не найдется в устах их языка коварного, ибо сами будут пастись и покоиться, и никто не потревожит их.
Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika; sadzayankhulanso zonama, ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo. Adzadya ndi kugona ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”
14 Ликуй, дщерь Сиона! торжествуй, Израиль! веселись и радуйся от всего сердца, дщерь Иерусалима!
Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni; fuwula mokweza, iwe Israeli! Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!
15 Отменил Господь приговор над тобою, прогнал врага твоего! Господь, царь Израилев, посреди тебя: уже более не увидишь зла.
Yehova wachotsa chilango chako, wabweza mdani wako. Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako; sudzaopanso chilichonse.
16 В тот день скажут Иерусалиму: “не бойся” - и Сиону: “да не ослабевают руки твои!”
Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti, “Usaope, iwe Ziyoni; usafowoke.
17 Господь Бог твой среди тебя, Он силен спасти тебя; возвеселится о тебе радостью, будет милостив по любви Своей, будет торжествовать о тебе с ликованием.
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”
18 Сетующих о торжественных празднествах Я соберу: твои они, на них тяготеет поношение.
“Ndidzakuchotserani zowawa za pa zikondwerero zoyikika; nʼzolemetsa ndi zochititsa manyazi.
19 Вот, Я стесню всех притеснителей твоих в то время и спасу хромлющее, и соберу рассеянное, и приведу их в почет и именитость на всей этой земле поношения их.
Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi onse amene anakuponderezani; ndidzapulumutsa olumala ndi kusonkhanitsa amene anamwazika. Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.
20 В то время приведу вас и тогда же соберу вас, ибо сделаю вас именитыми и почетными между всеми народами земли, когда возвращу плен ваш перед глазами вашими, говорит Господь.
Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani; pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu. Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu inu mukuona,” akutero Yehova.

< Софония 3 >