< Псалтирь 55 >
1 Начальнику хора. На струнных орудиях. Учение Давида. Услышь, Боже, молитву мою и не скрывайся от моления моего;
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe. Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu, musakufulatire kupempha kwanga,
2 внемли мне и услышь меня; я стенаю в горести моей, и смущаюсь
mverani ndipo mundiyankhe. Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru
3 от голоса врага, от притеснения нечестивого, ибо они возводят на меня беззаконие и в гневе враждуют против меня.
chifukwa cha mawu a adani anga, chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa; pakuti andidzetsera masautso ndipo akundizunza mu mkwiyo wawo.
4 Сердце мое трепещет во мне, и смертные ужасы напали на меня;
Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga; mantha a imfa andigwera.
5 страх и трепет нашел на меня, и ужас объял меня.
Mantha ndi kunjenjemera zandizinga; mantha aakulu andithetsa nzeru.
6 И я сказал: “кто дал бы мне крылья, как у голубя? я улетел бы и успокоился бы;
Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda! Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.
7 далеко удалился бы я, и оставался бы в пустыне;
Ndikanathawira kutali ndi kukakhala mʼchipululu.
8 поспешил бы укрыться от вихря, от бури”.
Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo; kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”
9 Расстрой, Господи, и раздели языки их, ибо я вижу насилие и распри в городе;
Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo; pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.
10 днем и ночью ходят они кругом по стенам его; злодеяния и бедствие посреди его;
Usana ndi usiku iwo akuzungulirazungulira pa makoma ake; nkhwidzi ndi kuzunza kuli mʼkati mwake.
11 посреди его пагуба; обман и коварство не сходят с улиц его:
Mphamvu zowononga zili pa ntchito mu mzinda; kuopseza ndi mabodza sizichoka mʼmisewu yake.
12 ибо не враг поносит меня, - это я перенес бы; не ненавистник мой величается надо мною, от него я укрылся бы;
Akanakhala mdani akundinyoza, ine ndikanapirira; akanakhala mdani akudzikweza yekha kutsutsana nane, ndikanakabisala.
13 но ты, который был для меня то же, что я, друг мой и близкий мой,
Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.
14 с которым мы разделяли искренние беседы и ходили вместе в дом Божий.
Mnzanga amene nthawi ina tinkasangalala pa chiyanjano chokoma ku nyumba ya Mulungu.
15 Да найдет на них смерть; да сойдут они живыми в ад, ибо злодейство в жилищах их, посреди их. (Sheol )
Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi; alowe mʼmanda ali amoyo pakuti choyipa chili pakati pawo. (Sheol )
16 Я же воззову к Богу, и Господь спасет меня.
Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu, ndipo Yehova anandipulumutsa.
17 Вечером и утром и в полдень буду умолять и вопиять, и Он услышит голос мой,
Madzulo, mmawa ndi masana ndimalira mowawidwa mtima, ndipo Iye amamva mawu anga.
18 избавит в мире душу мою от восстающих на меня, ибо их много у меня;
Iye amandiwombola ine osavulazidwa pa nkhondo imene yafika kulimbana nane, ngakhale kuti ndi ambiri amene akunditsutsa.
19 услышит Бог, и смирит их от века Живущий, потому что нет в них перемены; они не боятся Бога,
Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya, adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga, chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa ndipo saopa Mulungu.
20 простерли руки свои на тех, которые с ними в мире, нарушили союз свой;
Mnzanga woyenda naye wathira nkhondo abwenzi ake; iye akuphwanya pangano ake.
21 уста их мягче масла, а в сердце их вражда; слова их нежнее елея, но они суть обнаженные мечи.
Mawu ake ndi osalala kuposa batala komabe nkhondo ili mu mtima mwake; mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta, komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.
22 Возложи на Господа заботы твои, и Он поддержит тебя. Никогда не даст Он поколебаться праведнику.
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
23 Ты, Боже, низведешь их в ров погибели; кровожадные и коварные не доживут и до половины дней своих. А я на Тебя, Господи, уповаю.
Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa kulowa mʼdzenje lachiwonongeko; anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo sadzakhala moyo theka la masiku awo, koma ine ndimadalira Inu.