< От Луки 21 >

1 Взглянув же, Он увидел богатых, клавших дары свои в сокровищницу;
Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu.
2 увидел также и бедную вдову, положившую туда две лепты,
Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri.
3 и сказал: истинно говорю вам, что эта бедная вдова больше всех положила;
Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa.
4 ибо все те от избытка своего положили в дар Богу, а она от скудости своей положила все пропитание свое, какое имела.
Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”
5 И когда некоторые говорили о храме, что он украшен дорогими камнями и вкладами, Он сказал:
Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati,
6 придут дни, в которые из того, что вы здесь видите, не останется камня на камне; все будет разрушено.
“Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
7 И спросили Его: Учитель! когда же это будет? и какой признак, когда это должно произойти?
Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”
8 Он сказал: берегитесь, чтобы вас не ввели в заблуждение, ибо многие придут под именем Моим, говоря, что это Я; и это время близко: не ходите вслед их.
Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo.
9 Когда же услышите о войнах и смятениях, не ужасайтесь, ибо этому надлежит быть прежде; но не тотчас конец.
Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”
10 Тогда сказал им: восстанет народ на народ, и царство на царство;
Kenaka anawawuza kuti, “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina.
11 будут большие землетрясения по местам, и глады, и моры, и ужасные явления, и великие знамения с неба.
Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.
12 Прежде же всего того возложат на вас руки и будут гнать вас, предавая в синагоги и в темницы, и поведут пред царей и правителей за имя Мое;
“Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa.
13 будет же это вам для свидетельства.
Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni.
14 Итак положите себе на сердце не обдумывать заранее, что отвечать,
Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire.
15 ибо Я дам вам уста и премудрость, которой не возмогут противоречить ни противостоять все, противящиеся вам.
Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa.
16 Преданы также будете и родителями, и братьями, и родственниками, и друзьями, и некоторых из вас умертвят;
Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani.
17 и будете ненавидимы всеми за имя Мое,
Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine.
18 но и волос с головы вашей не пропадет, -
Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke.
19 терпением вашим спасайте души ваши.
Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.
20 Когда же увидите Иерусалим, окруженный войсками, тогда знайте, что приблизилось запустение его:
“Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi.
21 тогда находящиеся в Иудее да бегут в горы; и кто в городе, выходи из него; и кто в окрестностях, не входи в него,
Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda.
22 потому что это дни отмщения, да исполнится все написанное.
Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa.
23 Горе же беременным и питающим сосцами в те дни; ибо великое будет бедствие на земле и гнев на народ сей:
Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira.
24 и падут от острия меча, и отведутся в плен во все народы; и Иерусалим будет попираем язычниками, доколе не окончатся времена язычников.
Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.
25 И будут знамения в солнце и луне и звездах, а на земле уныние народов и недоумение; и море восшумит и возмутится;
“Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja.
26 люди будут издыхать от страха и ожидания бедствий, грядущих на вселенную, ибо силы небесные поколеблются,
Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka.
27 и тогда увидят Сына Человеческого, грядущего на облаке с силою и славою великою.
Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.
28 Когда же начнет это сбываться, тогда восклонитесь и поднимите головы ваши, потому что приближается избавление ваше.
Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”
29 И сказал им притчу: посмотрите на смоковницу и на все деревья:
Iye anawawuza fanizo ili, “Taonani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse.
30 когда они уже распускаются, то, видя это, знаете сами, что уже близко лето.
Ikamatulutsa masamba, mumakhoza kudzionera nokha ndi kudziwa kuti dzinja lili pafupi.
31 Так, и когда вы увидите то сбывающимся, знайте, что близко Царствие Божие.
Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.
32 Истинно говорю вам: не прейдет род сей, как все это будет;
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika.
33 небо и земля прейдут, но слова Мои не прейдут.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
34 Смотрите же за собою, чтобы сердца ваши не отягчались объедением и пьянством и заботами житейскими, и чтобы день тот не постиг вас внезапно,
“Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha.
35 ибо он, как сеть, найдет на всех живущих по всему лицу земному;
Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi.
36 итак бодрствуйте на всякое время и молитесь, да сподобитесь избежать всех сих будущих бедствий и предстать пред Сына Человеческого.
Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”
37 Днем Он учил в храме, а ночи, выходя, проводил на горе, называемой Елеонскою.
Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse.
38 И весь народ с утра приходил к Нему в храм слушать Его.
Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.

< От Луки 21 >