< Исаия 3 >
1 Вот, Господь, Господь Саваоф, отнимет у Иерусалима и у Иуды посох и трость, всякое подкрепление хлебом и всякое подкрепление водою,
Taonani tsopano, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu pamodzi ndi thandizo; adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
2 храброго вождя и воина, судью и пророка, и прозорливца и старца,
anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo, oweruza ndi aneneri, anthu olosera ndi akuluakulu,
3 пятидесятника и вельможу и советника, и мудрого художника и искусного в слове.
atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka, aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
4 И дам им отроков в начальники, и дети будут господствовать над ними.
Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo; ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
5 И в народе один будет угнетаем другим, и каждый - ближним своим; юноша будет нагло превозноситься над старцем и простолюдин над вельможею.
Anthu adzazunzana, munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake. Anthu wamba adzanyoza akuluakulu.
6 Тогда ухватится человек за брата своего, в семействе отца своего, и скажет: у тебя есть одежда, будь нашим вождем, и да будут эти развалины под рукою твоею.
Munthu adzagwira mʼbale wake mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati, “Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu; lamulira malo opasuka ano!”
7 А он с клятвою скажет: не могу исцелить ран общества; и в моем доме нет ни хлеба, ни одежды; не делайте меня вождем народа.
Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti, “Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake. Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga; musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
8 Так рушился Иерусалим, и пал Иуда, потому что язык их и дела их - против Господа, оскорбительны для очей славы Его.
Yerusalemu akudzandira, Yuda akugwa; zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova, sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
9 Выражение лиц их свидетельствует против них, и о грехе своем они рассказывают открыто, как Содомляне, не скрывают: горе душе их! ибо сами на себя навлекают зло.
Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa; amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu; salibisa tchimo lawolo. Tsoka kwa iwo odziputira okha mavuto.
10 Скажите праведнику, что благо ему, ибо он будет вкушать плоды дел своих;
Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino, pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
11 а беззаконнику - горе, ибо будет ему возмездие за дела рук его.
Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo! Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
12 Притеснители народа Моего - дети, и женщины господствуют над ним. Народ Мой! вожди твои вводят тебя в заблуждение и путь стезей твоих испортили.
Achinyamata akupondereza anthu anga, ndipo amene akuwalamulira ndi akazi. Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani; akukuchotsani pa njira yanu.
13 Восстал Господь на суд - и стоит, чтобы судить народы.
Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu; wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
14 Господь вступает в суд со старейшинами народа Своего и с князьями его: вы опустошили виноградник; награбленное у бедного - в ваших домах;
Yehova akuwazenga milandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake: “Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa; nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
15 что вы тесните народ Мой и угнетаете бедных? говорит Господь, Господь Саваоф.
Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga, nʼkudyera masuku pamutu amphawi?” Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
16 И сказал Господь: за то, что дочери Сиона надменны и ходят, подняв шею и обольщая взорами, и выступают величавою поступью и гремят цепочками на ногах, -
Yehova akunena kuti, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri, akuyenda atakweza makosi awo, akukopa amuna ndi maso awo akuyenda monyangʼama akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
17 оголит Господь темя дочерей Сиона и обнажит Господь срамоту их;
Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo; Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
18 в тот день отнимет Господь красивые цепочки на ногах и звездочки, и луночки,
Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi,
19 серьги, и ожерелья, и опахала,
ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope,
20 увясла и запястья, и пояса, и сосудцы с духами, и привески волшебные,
maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa,
21 перстни и кольца в носу,
mphete ndi zipini,
22 верхнюю одежду и нижнюю, и платки, и кошельки,
zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama,
23 светлые тонкие епанчи и повязки, и покрывала.
magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
24 И будет вместо благовония зловоние, и вместо пояса будет веревка, и вместо завитых волос - плешь, и вместо широкой епанчи - узкое вретище, вместо красоты - клеймо.
Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha, mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe; mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi; mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli; mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25 Мужи твои падут от меча, и храбрые твои - на войне.
Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga, asilikali ako adzafera ku nkhondo.
26 И будут воздыхать и плакать ворота столицы, и будет она сидеть на земле опустошенная.
Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira; Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.