< Hebreus 8 >
1 Ora, o ponto-chave do que falamos é que temos um Sumo Sacerdote que está sentado à direita do trono da Majestade nos céus,
Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba.
2 servidor do Santuário, e do verdadeiro Tabernáculo, que Senhor ergueu, e não o homem.
Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.
3 Pois todo sumo sacerdote é constituído para apresentar tanto ofertas como sacrifícios; por isso era necessário que também este tivesse alguma coisa a oferecer.
Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka.
4 Mas, se ele [ainda] estivesse na terra, nem sequer seria sacerdote, já que [ainda] há os que apresentam as ofertas segundo a Lei.
Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo.
5 Esses servem a um esboço, uma sombra das coisas celestiais, como Moisés foi divinamente avisado, antes de construir o Tabernáculo. Porque [Deus] disse: Olha, faze tudo conforme o modelo que te foi mostrado no monte.
Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”
6 Mas agora [Jesus] obteve um ofício mais relevante, como é também Mediador de um melhor pacto, que está firmado em melhores promessas.
Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.
7 Pois, se aquele primeiro tivesse sido infalível, nunca haveria se buscado lugar para o segundo.
Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake.
8 Porque, enquanto [Deus] repreendia os do povo, disse-lhes: Eis que vêm dias, diz o Senhor, que, sobre o povo de Israel e sobre o povo de Judá, estabelecerei um novo pacto;
Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati, “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachita pangano latsopano ndi Aisraeli ndiponso nyumba ya Yuda.
9 não conforme o pacto que fiz com os seus ancestrais no dia em que eu os tomei pelas mãos, para os tirar da terra do Egito. Pois não permaneceram naquele meu pacto, e parei de lhes dar atenção, diz o Senhor.
Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo, pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija ndipo Ine sindinawasamalire, akutero Ambuye.
10 Este, pois, é o pacto que farei com o povo de Israel depois daqueles dias, diz o Senhor: Porei minhas leis nas mentes deles, e as escreverei em seus corações. Eu serei o Deus deles, e eles serão o meu povo.
Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli: Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye, Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo, ndi kulemba mʼmitima mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
11 E não terão de ensinar cada um ao seu conterrâneo, ou ao seu irmão, dizendo: “Conhece ao Senhor”; porque todos me conhecerão, desde o menor deles até o maior.
Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake, kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye chifukwa onse adzandidziwa, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
12 Pois serei misericordioso com as suas injustiças, e não mais me lembrarei dos seus pecados.
Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
13 Quando ele disse: “Novo [pacto]”, ele tornou o primeiro ultrapassado. Ora, o que se torna ultrapassado e envelhece está perto de desaparecer.
Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.