< Provérbios 13 >
1 O filho sábio ouve a correção do pai; mas o escarnecedor não ouve a repreensão.
Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake, koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.
2 Do fruto da boca cada um comerá o bem, mas a alma dos prevaricadores comerá a violência.
Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake, koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.
3 O que guarda a sua boca conserva a sua alma, mas o que dilata os seus lábios tem perturbação.
Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake, koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.
4 A alma do preguiçoso deseja, e coisa nenhuma alcança, mas a alma dos diligentes se engorda.
Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, koma munthu wakhama adzalemera.
5 O justo aborrece a palavra de mentira, mas o ímpio se faz vergonha, e se confunde.
Munthu wolungama amadana ndi zabodza, koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi.
6 A justiça guarda ao sincero de caminho, mas a impiedade transtornará o pecador.
Chilungamo chimateteza munthu wangwiro, koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
7 Há alguns que se fazem ricos, e não tem coisa nenhuma, e outros que se fazem pobres e tem muita fazenda.
Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse; munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri.
8 O resgate da vida de cada um são as suas riquezas, mas o pobre não ouve as ameaças.
Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake, koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.
9 A luz dos justos alegra, mas a candeia dos ímpios se apagará.
Nyale ya munthu wolungama ndi yokondweretsa, koma nyale ya munthu woyipa imazimitsidwa.
10 Da soberba só provém a contenda, mas com os que se aconselham se acha a sabedoria.
Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano, koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.
11 A fazenda que procede da vaidade se diminuirá, mas quem a ajunta com a mão a aumentará.
Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.
12 A esperança deferida enfraquece o coração, mas o desejo chegado é árvore de vida.
Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.
13 O que despreza a palavra perecerá, mas o que teme o mandamento será galardoado.
Amene amanyoza malangizo adzawonongeka, koma amene amasamala lamulo amalandira mphotho.
14 A doutrina do sábio é uma fonte de vida para se desviar dos laços da morte.
Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo; amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.
15 O bom entendimento dá graça, mas o caminho dos prevaricadores é áspero.
Munthu wa nzeru zabwino amapeza kuyanja pakati pa anthu, koma munthu wosakhulupirika adzawonongeka.
16 Todo o prudente obra com conhecimento, mas o tolo espraia a sua loucura.
Munthu wochenjera amachita zinthu mwanzeru, koma chitsiru chimaonetsa poyera uchitsiru wake.
17 O ímpio mensageiro cai no mal, mas o embaixador fiel é saúde.
Wamthenga woyipa amagwetsa anthu mʼmavuto, koma nthumwi yodalirika imabweretsa mtendere.
18 Pobreza e afronta virão ao que rejeita a correção, mas o que guarda a repreensão será venerado.
Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa, koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa.
19 O desejo que se cumpre deleita a alma, mas apartar-se do mal é abominável para os loucos.
Chinthu chochilakalaka chikachitika chimasangalatsa mtima, koma zitsiru zimadana ndi kuleka zoyipa.
20 O que anda com os sábios, ficará sábio, mas o companheiro dos tolos sofrerá severamente.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru; koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.
21 O mal perseguirá aos pecadores, mas os justos serão galardoados com bem.
Choyipa chitsata mwini, koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino.
22 O homem de bem deixa uma herança aos filhos de seus filhos, mas a fazenda do pecador se deposita para o justo.
Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa, koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.
23 A lavoura dos pobres dá abundância de mantimento, mas alguns há que se consomem por falta de juízo.
Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amachilanda.
24 O que retém a sua vara aborrece a seu filho, mas o que o ama madruga a castiga-lo.
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
25 O justo come até fartar-se a sua alma, mas o ventre dos ímpios terá necessidade.
Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta, koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.