< 2 Pedro 1 >
1 Simão Pedro, servo e apóstolo de Jesus Cristo, aos que conosco alcançaram fé igualmente preciosa pela justiça do nosso Deus e Salvador Jesus Cristo:
Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
2 Graça e paz vos seja multiplicada, pelo conhecimento de Deus, e de Jesus nosso Senhor;
Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.
3 Como o seu divino poder nos deu tudo o que diz respeito à vida e piedade, pelo conhecimento daquele que nos chamou por sua glória e virtude;
Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake.
4 Pelas quais ele nos tem dado grandíssimas e preciosas promessas, para que por elas fiqueis participantes da natureza divina, havendo escapado da corrupção, que pela concupiscência há no mundo.
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.
5 E vós também, pondo nisto mesmo toda a diligência, acrescentai à vossa fé a virtude, e à virtude a ciência,
Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru.
6 E à ciência temperança, e à temperança paciência, e à paciência piedade,
Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu.
7 E à piedade amor fraternal; e ao amor fraternal caridade.
Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.
8 Porque, se em vós houver, e abundarem estas coisas, não vos deixarão ociosos nem estéreis no conhecimento de nosso Senhor Jesus Cristo.
Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu.
9 Pois aquele em quem não há estas coisas é cego, nada vendo ao longe, havendo-se esquecido da purificação dos seus antigos pecados.
Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.
10 Portanto, irmãos, procurai fazer cada vez mais firme a vossa vocação e eleição; porque, fazendo isto, nunca jamais tropeçareis.
Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse.
11 Porque assim vos será abundantemente dada a entrada no reino eterno de nosso Senhor e Salvador Jesus Cristo. (aiōnios )
Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. (aiōnios )
12 Pelo que não deixarei de exhortar-vos sempre acerca destas coisas, ainda que bem as saibais, e estejais confirmados na presente verdade.
Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano.
13 E tenho por justo, enquanto estiver neste tabernáculo, despertar-vos com admoestações.
Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani,
14 Sabendo que brevemente hei de deixar este meu tabernáculo, como também nosso Senhor Jesus Cristo já mo tem revelado.
chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu.
15 Mas também eu procurarei em toda a ocasião que depois da minha morte tenhais lembrança destas coisas.
Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse.
16 Porque não vos fizemos saber a virtude e a vinda de nosso Senhor Jesus Cristo, seguindo fábulas artificialmente compostas: mas nós mesmos vimos a sua magestade.
Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake.
17 Porque recebeu de Deus Pai honra e glória, quando da magnífica glória lhe foi enviada uma tal voz: Este é o meu Filho amado, em quem me tenho comprazido.
Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.”
18 E ouvimos esta voz enviada do céu, estando nós com ele no monte santo;
Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.
19 E temos, mui firme, a palavra dos profetas, à qual bem fazeis em estar atentos, como a uma luz que alumia em lugar escuro, até que o dia esclareça, e a estrela da alva saia em vossos corações.
Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu.
20 Sabendo primeiramente isto, que nenhuma profecia da escritura é de particular interpretação.
Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha.
21 Porque a profecia não foi antigamente produzida por vontade de homem algum, mas os homens santos de Deus falaram inspirados pelo Espírito Santo.
Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.