< 1 Tessalonicenses 4 >
1 Assim que, irmãos, no demais vos rogamos e exhortamos no Senhor Jesus, que, assim como recebestes de nós, como vos convenha andar e agradar a Deus, assim n'isto abundeis cada vez mais.
Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale.
2 Porque vós bem sabeis que mandamentos vos temos dado pelo Senhor Jesus.
Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.
3 Porque esta é a vontade de Deus, a vossa sanctificação: que vos abstenhaes da fornicação;
Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama;
4 Que cada um de vós saiba possuir o seu vaso em sanctificação e honra;
aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu,
5 Não em sensualidade de concupiscencia, como os gentios, que não conhecem a Deus.
osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu.
6 Ninguem opprima nem engane a seu irmão em negocio algum, porque o Senhor é vingador de todas estas coisas, como tambem já d'antes vol-o dissemos e testificámos.
Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani.
7 Porque não nos chamou Deus para a immundicia, senão para a sanctificação.
Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.
8 Porque quem despreza isto não despreza ao homem, mas sim a Deus, o qual nos deu tambem o seu Espirito Sancto.
Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.
9 Emquanto, porém, á caridade fraternal, não necessitaes de que vos escreva, porque já vós mesmos estaes instruidos por Deus que vos ameis uns aos outros.
Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake.
10 Porque tambem já assim o fazeis, para com todos os irmãos que estão por toda a Macedonia. Exhortamo-vos, porém, irmãos, a que ainda n'isto abundeis cada vez mais
Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.
11 E procureis viver quietos, e tratar dos vossos proprios negocios, e trabalhar com vossas proprias mãos, como já vol-o temos mandado;
Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake.
12 Para que andeis honestamente para com os que estão de fóra, e não necessiteis de coisa alguma.
Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.
13 Não quero, porém, irmãos, que sejaes ignorantes ácerca dos que já dormem, para que vos não entristeçaes, como tambem os demais, que não teem esperança.
Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo.
14 Porque, se crêmos que Jesus morreu e resuscitou, assim tambem aos que em Jesus dormem Deus os tornará a trazer com elle.
Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
15 Dizemo-vos portanto isto pela palavra do Senhor: que nós, os que ficarmos vivos para a vinda do Senhor, não precederemos os que dormem.
Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale.
16 Porque o mesmo Senhor descerá do céu com alarido, e com voz de archanjo, e com a trombeta de Deus; e os que morreram em Christo resuscitarão primeiro.
Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba.
17 Depois nós, os que ficarmos vivos, seremos arrebatados juntamente com elles nas nuvens, a encontrar o Senhor nos ares, e assim estaremos sempre com o Senhor.
Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya.
18 Portanto, consolae-vos uns aos outros com estas palavras.
Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.