< Daniela 2 >
1 W drugim roku panowania Nabuchodonozora miał Nabuchodonozor sen i strwożył się jego duch, i nie mógł spać.
Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona.
2 Wtedy król rozkazał zwołać magów, astrologów, czarowników i Chaldejczyków, aby opowiedzieli królowi jego sen. Przyszli więc i stanęli przed królem.
Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu,
3 Król powiedział do nich: Miałem sen i strwożył się mój duch, i chcę wiedzieć, co ten sen oznacza.
mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.”
4 Wtedy Chaldejczycy odpowiedzieli królowi po syryjsku: Królu, żyj na wieki! Opowiedz sen swoim sługom, a objaśnimy [jego] znaczenie.
Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”
5 Król odpowiedział Chaldejczykom: Ta sprawa już uleciała mi z pamięci. Jeśli nie oznajmicie mi snu i jego znaczenia, będziecie rozsiekani na kawałki, a wasze domy będą zamienione w gnojowisko.
Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja.
6 Ale jeśli oznajmicie mi sen i jego znaczenie, otrzymacie ode mnie dary i nagrody oraz wielką cześć. Dlatego oznajmijcie mi sen i jego znaczenie.
Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.”
7 Odpowiedzieli powtórnie: Niech król opowie sen swoim sługom, a objaśnimy [jego] znaczenie.
Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.”
8 Król odpowiedział: Wiem na pewno, że celowo to odkładacie, gdyż wiecie, że ten sen uleciał mi z pamięci.
Ndipo mfumu inayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti mukungozengereza kufuna kutaya nthawi chabe chifukwa mukuzindikira kuti izi ndi zimene ndatsimikiza kuchita.
9 Jeśli więc nie oznajmicie mi snu, jest dla was tylko jeden dekret. Postanowiliście bowiem mówić wobec mnie słowa kłamliwe i przewrotne, aż czas upłynie. Dlatego oznajmijcie mi sen, a przekonam się, że będziecie mogli objaśnić mi jego znaczenie.
Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.”
10 Chaldejczycy odpowiedzieli królowi: Nie ma człowieka na ziemi, który by mógł oznajmić tę rzecz królowi. Dlatego żaden król, książę albo władca nie wymaga takiej rzeczy od żadnego maga, astrologa lub Chaldejczyka.
Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi.
11 Rzecz, której król wymaga, [jest] trudna, a nie ma nikogo, kto by mógł ją oznajmić królowi, oprócz bogów, którzy nie mieszkają wśród ludzi.
Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.”
12 Z tej przyczyny król się rozzłościł i bardzo się rozgniewał, i rozkazał wytracić wszystkich mędrców Babilonu.
Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe.
13 A gdy wyszedł dekret, aby zgładzić mędrców, szukano także Daniela i jego towarzyszy, aby ich wymordować.
Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe.
14 Wtedy Daniel odpowiedział mądrze i roztropnie Ariochowi, dowódcy gwardii królewskiej, który wyszedł zabić mędrców Babilonu;
Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni.
15 Powiedział do Ariocha, dowódcy króla: Czemu ten dekret tak szybko wyszedł od króla? Wtedy Arioch oznajmił Danielowi sprawę.
Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli.
16 Wszedł więc Daniel do króla i poprosił go, aby dał mu czas na oznajmienie królowi znaczenia [snu].
Danieli anapita mofulumira kwa mfumu ndipo anamupempha kuti amupatse nthawi kuti amuwuze zimene walota ndi tanthauzo lake.
17 Potem Daniel poszedł do swego domu i opowiedział sprawę swoim towarzyszom: Chananiaszowi, Miszaelowi i Azariaszowi;
Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya.
18 Aby prosili Boga nieba o miłosierdzie względem tej tajemnicy, żeby nie zginęli Daniel i jego towarzysze z resztą mędrców Babilonu.
Danieli anadandaulira anzake kuti apemphe kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kumuwululira chinsinsi, kuti iye ndi anzakewo asanyongedwe pamodzi ndi anzeru ena onse a ku Babuloni.
19 Wtedy Danielowi została objawiona ta tajemnica w nocnym widzeniu, za co Daniel błogosławił Bogu nieba.
Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba,
20 Daniel powiedział: Niech będzie błogosławione imię Boga na wieki wieków, bo mądrość i moc do niego należą;
ndipo anati: “Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi; nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake.
21 On zmienia czasy i okresy, usuwa królów i ustanawia królów. Daje mądrość mądrym, a wiedzę rozumnym;
Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.
22 On objawia rzeczy głębokie i ukryte, wie, co [jest] w ciemności, a światłość z nim mieszka.
Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika; amadziwa zimene zili mu mdima, ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.
23 Ciebie, Boże moich ojców, wysławiam i chwalę [za to], że dałeś mi mądrość i moc, że oznajmiłeś mi teraz to, o co cię prosiliśmy. Oznajmiłeś nam bowiem sen króla.
Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga: mwandipatsa nzeru ndi mphamvu, mwandiwululira zomwe tinakupemphani, mwatiwululira maloto a mfumu.”
24 Dlatego Daniel wszedł do Ariocha, którego król ustanowił, aby wytracił mędrców Babilonu. Gdy przyszedł, tak powiedział do niego: Nie trać mędrców Babilonu. Wprowadź mnie do króla, a [ja] oznajmię królowi znaczenie [snu].
Motero Danieli anapita kwa Ariyoki, amene mfumu inamusankha kuti akaphe anthu anzeru a ku Babuloni, ndipo anati kwa iye, “Musaphe anthu anzeru a ku Babuloni. Ndiperekezeni kwa mfumu, ndipo ndidzayimasulira maloto ake.”
25 Wtedy Arioch z pośpiechem wprowadził Daniela do króla i tak mu powiedział: Znalazłem męża spośród uprowadzonych z Judy, który oznajmi królowi znaczenie [snu].
Ariyoki anapita naye Danieli kwa mfumu nthawi yomweyo ndipo anati, “Ndapeza munthu pakati pa akapolo ochokera ku Yuda amene akhoza kuwuza mfumu zimene maloto ake akutanthauza.”
26 Król odpowiedział Danielowi, któremu na imię [było] Belteszassar: Czy potrafisz oznajmić mi sen, który miałem, oraz jego znaczenie?
Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, “Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?”
27 Daniel odpowiedział królowi: Tajemnicy, o którą król pyta, nie mogą oznajmić królowi mędrcy, astrologowie, magowie i wróżbici;
Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa,
28 Jest jednak Bóg w niebie, który objawia tajemnice, i [on] oznajmił królowi Nabuchodonozorowi, co nastąpi w ostatecznych dniach. Twój sen i widzenia w twojej głowie, które miałeś na swoim łożu, są takie;
koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:
29 Tobie, królu, przychodziły na twoim łożu myśli [o tym], co ma nastąpić później. Ten zaś, który objawia tajemnice, oznajmił ci to, co nastąpi.
“Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika.
30 I mnie została objawiona tajemnica, nie za [jakąś] mądrość, jakbym miał [jej] więcej niż wszyscy żyjący, ale przez modlitwę, aby znaczenie [snu] było oznajmione królowi i abyś poznał myśli swego serca.
Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.
31 Ty, królu, miałeś takie widzenie: Oto posąg wielki; ten wielki posąg o nadzwyczajnym blasku stał przed tobą, a jego wygląd był straszny.
“Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe.
32 Głowa tego posągu [wykonana] była z czystego złota, jego piersi i ramiona – ze srebra, jego brzuch i biodra – z brązu;
Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa.
33 Jego golenie – z żelaza, jego stopy – częściowo z żelaza, częściowo z gliny.
Miyendo yake inali yachitsulo, mapazi ake anali achitsulo chosakaniza ndi dongo.
34 Patrzyłeś na to, aż został odcięty kamień bez [pomocy] rąk, i uderzył posąg w jego stopy z żelaza i gliny, i skruszył je.
Inu mukuona, mwala unagamuka, koma osati ndi manja a munthu. Unagwera fanolo pa mapazi ake achitsulo chosakaniza ndi dongo aja ndi kuwaphwanya.
35 Wtedy zostały skruszone razem: żelazo, glina, brąz, srebro i złoto i stały się jak plewy na klepisku w lecie; i wiatr niósł je tak, że nie znaleziono ich w żadnym miejscu. Kamień zaś, który uderzył w posąg, stał się wielką górą i napełnił całą ziemię.
Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi.
36 Taki [jest] sen. Jego znaczenie też wypowiemy przed królem;
“Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu.
37 Ty, królu, jesteś królem królów, bo tobie Bóg nieba dał królestwo, moc, potęgę i sławę.
Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero;
38 I dał w twoją rękę wszystko to, gdzie mieszkają synowie ludzi, zwierzęta polne i ptactwo niebieskie, i ustanowił cię panem nad tym wszystkim. Ty jesteś tą głową ze złota.
Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.
39 Ale po tobie powstanie inne królestwo, mniejsze od twojego, a potem trzecie królestwo z brązu, które będzie panować nad całą ziemią.
“Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi.
40 Czwarte królestwo będzie mocne jak żelazo, bo jak żelazo kruszy i miażdży wszystko, jak żelazo łamie wszystko, tak i [ono] połamie i pokruszy [wszystko].
Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse.
41 A że widziałeś stopy i palce częściowo z gliny garncarskiej, a częściowo z żelaza – [oznacza to, że] królestwo będzie podzielone. Będzie w nim nieco siły żelaza, tak jak widziałeś żelazo zmieszane z mulistą gliną;
Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita.
42 A palce stóp częściowo z żelaza a częściowo z gliny [znaczą], że królestwo będzie częściowo silne, a częściowo kruche.
Monga zala zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho ufumu uwu udzakhala pangʼono wolimba ndi pangʼono wofowoka.
43 A że widziałeś żelazo zmieszane z mulistą gliną, oznacza [to], że się zmieszają ze sobą ludzie, ale nie będzie się trzymał jeden drugiego, tak jak żelaza nie można zmieszać z gliną.
Ndipo monga munaona chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, choncho anthu adzakhala wosakanizana ndipo sadzagwirizana, monga muja chitsulo sichingasakanizike ndi dongo.
44 Ale w dniach tych królów Bóg nieba wzbudzi królestwo, które nigdy nie będzie zniszczone. To królestwo nie przejdzie na inny lud, ale połamie i zniszczy wszystkie te królestwa, samo zaś będzie trwać na wieki.
“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya.
45 To, że widziałeś, jak kamień został odcięty z góry bez [pomocy] rąk i skruszył żelazo, brąz, glinę, srebro i złoto, [oznacza], że wielki Bóg oznajmił królowi, co nastąpi potem. Sen jest prawdziwy i jego znaczenie pewne.
Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa. “Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”
46 Wtedy król Nabuchodonozor padł na twarz, oddał pokłon Danielowi i rozkazał, aby złożono mu ofiarę i kadzidło.
Pamenepo mfumu Nebukadinezara inadzigwetsa chafufumimba pamaso pa Danieli ndi kumupatsa ulemu. Ndipo inalamula kuti anthu onse amuthirire Danieli nsembe ndi kumufukizira lubani.
47 Następnie król zwrócił się do Daniela i powiedział: Zaprawdę wasz Bóg jest Bogiem bogów i Panem królów, który objawia tajemnice, ponieważ zdołałeś objawić tę tajemnicę.
Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”
48 Potem król wywyższył Daniela [i] dał mu wiele wielkich darów, i uczynił go panem nad całą prowincją Babilonu i głównym przełożonym nad wszystkimi mędrcami Babilonu.
Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru.
49 Ale Daniel wyprosił od króla, aby ustanowił nad sprawami prowincji Babilonu Szadraka, Meszaka i Abed-Nego; Daniel zaś pozostał w bramie króla.
Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.